-
Zinthu Zodetsa Nkhawa Zimachitika KulikonseNsanja ya Olonda—2015 | July 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIYANI CHINGATITHANDIZE TIKAKHALA NDI NKHAWA?
Zinthu Zodetsa Nkhawa Zimachitika Kulikonse
“Nditapita kukagula zakudya, ndinangopeza mabisiketi okhaokha ndipo mtengo wake unali utawonjezereka maulendo 10,000. Nditapitanso tsiku lotsatira, ndinapeza kuti m’masitolo onse munalibiretu zakudya.”—Paul, Zimbabwe.
“Tsiku lina amuna anga anangondiuza kuti akufuna kundisiya. Zimenezi zinandidetsa nkhawa kwambiri ndipo ndinadzifunsa kuti, Ndingapirire bwanji nkhanza zimenezi? Nanga ana angawa ziwathera bwanji?”—Janet, United States.
“Nditangomva kulira kwa masayilini, ndinathawa n’kugona pansi msangamsanga. Apa n’kuti ndege zikuphulitsa mabomba. Panapita maola angapo, koma ndinkanjenjemerabe ndi mantha.”—Alona, Israel.
Masiku ano zinthu zodetsa nkhawa ndi zambiri chifukwa tikukhala mu “nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Anthu ambiri akuvutika chifukwa chosowa ndalama, kutha kwa banja, nkhondo, matenda oopsa ndiponso ngozi zoyambitsidwa ndi anthu kapenanso zochitika mwadzidzidzi. Komatu si zokhazi, ena akatuluka chotupa amakhala ndi nkhawa chifukwa amaganiza kuti ndi khansa. Anthu enanso amakhala ndi nkhawa kuti zidzukulu zawo zikamadzakula, dzikoli lidzakhala litaipa kwambiri.
Nthawi zina kuda nkhawa sikumakhala kolakwika. Mwachibadwa munthu amada nkhawa akamakonzekera kulemba mayeso, kuchita zinazake, ndiponso kufunsidwa mafunso pofuna kulowa ntchito. Nkhawa imatithandizanso kuti tisachite zinthu zoipa. Koma si bwino kumangokhala ndi nkhawa nthawi zonse ndiponso mopitirira malire. Zotsatira za kafukufuku wokhudza anthu opitirira 68,000 yemwe anachitika posachedwapa zinasonyeza kuti kuda nkhawa ngakhale pang’ono pokha kumachititsa kuti munthu afe msanga. Mpake kuti Yesu anafunsa kuti: “Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha mwa kuda nkhawa?” Uwu ndi umboni wakuti nkhawa sitalikitsa moyo wa munthu. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Lekani kudera nkhawa.” (Mateyu 6:25, 27) Koma kodi n’chiyani chingathandize munthu kuti asamade nkhawa kwambiri?
Chofunika ndi kugwiritsa ntchito malangizo anzeru, kukhala ndi chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu ndiponso kukhulupirira ndi mtima wonse kuti m’tsogolo zinthu zidzakhala bwino. Tizikumbukira kuti ngakhale kuti panopa sitikukumana ndi zinthu zodetsa nkhawa kwambiri, tingadzakumane nazo m’tsogolo. Ndiye tiyeni tione mmene mfundozi zinathandizira Paul, Janet, ndi Alona pa nthawi imene anakumana ndi mavuto odetsa nkhawa.
-
-
Kuda Nkhawa Chifukwa cha Kusowa kwa NdalamaNsanja ya Olonda—2015 | July 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIYANI CHINGATITHANDIZE TIKAKHALA NDI NKHAWA?
Kuda Nkhawa Chifukwa cha Kusowa Kwa Ndalama
Paul, yemwe ali ndi ana awiri ananena kuti: “Mavuto a zachuma atakula m’dziko lathu, zakudya zinayamba kudula komanso zinkasowa. Tinkadikirira pamzere kwa maola ambiri koma nthawi zambiri chakudyacho chinkatha tisanagule n’komwe. Anthu anaonda kwambiri moti ena ankakomoka ndi njala. Mitengo ya zinthu inakwera kufika mamiliyoni kenako mabiliyoni ndipo pamapeto pake ndalama ya dziko lathu inatheratu mphamvu. Ndalama zanga zonse zakubanki, za inshuwalansi komanso za penshoni zinalibenso ntchito.”
Paul
Paul ankadziwa kuti kugwiritsa ntchito “nzeru zopindulitsa” ndi kumene kungamuthandize kuti akwanitse kusamalira banja lake. (Miyambo 3:21) Iye ananena kuti: “Ndinkagwira ntchito ya zamagetsi, koma zinthu zitavuta ndinkalolera kugwira ntchito iliyonse ngakhale yamalipiro ochepa. Anthu ena ankandipatsa zakudya kapena katundu monga malipiro anga. Akandipatsa sopo 4, ndinkagwiritsa ntchito muwiri winayo n’kugulitsa. Patapita nthawi, ndinagula tianapiye 40. Nkhukuzi zitakula, ndinagulitsa n’kugula anapiye ena 300. Kenako ndinasinthanitsa nkhuku 50 ndi matumba a ufa awiri olemera 50kg. Ufawu unali wokwanira kudyetsa banja langa ndi mabanja enanso kwa nthawi yaitali ndithu.”
Paul ankadziwanso kuti kudalira Mulungu ndi kothandiza kwambiri. Tikamamvera Mulungu, iye amatithandiza. Pa nkhani yokhudza kupeza zinthu zofunika pamoyo, Yesu anati: “Siyani kuvutika mumtima . . . Atate wanu amadziwa kuti zinthu zonsezi n’zofunika kwa inu.”—Luka 12:29-31.
N’zomvetsa chisoni kuti Satana, yemwe ndi mdani wamkulu wa Mulungu, amapusitsa anthu kuti aziika maganizo awo onse pa zofuna za moyo. Anthu amada nkhawa kwambiri ndi zinthu zimene zikuwachitikira ndiponso zimene sizingachitike n’komwe. Ndipo amavutika kufunafuna zinthu zomwe ndi zosafunika pamoyo wawo. Izi zimachititsa kuti anthu ambiri azingotenga ngongole ndipo pamapeto pake amakhala ndi nkhawa, chifukwa Baibulo limati: “Wobwereka amakhala kapolo wa wobwereketsayo.”—Miyambo 22:7.
Anthu ena amachita zinthu asanaganize bwino ndipo pamapeto pake amanong’oneza bondo. Paul anafotokoza kuti: “Anthu ambiri amene tinayandikana nawo anasiya mabanja ndi anzawo kuti akasakesake chuma kumaiko akunja. Ena anapita opanda mapepala owavomereza kukhala m’dziko lina ndipo izi zinachititsa kuti asalembedwe ntchito. Nthawi zambiri ankangokhalira kuthawa apolisi komanso ankagona m’misewu. Zonsezi zinawachitikira chifukwa chosakhulupirira kuti Mulungu awathandiza. Koma ine ndi banja langa tinaona kuti ndi bwino kukhalabe limodzi ndi kudalira Mulungu kuti atithandize pa nthawi ya mavuto a zachumayi.”
MUZITSATIRA MALANGIZO A YESU
Paul anapitiriza kuti: “Yesu ananena kuti: ‘Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.’ Potsatira malangizo amenewa, ndinkangopempha Mulungu kuti, ‘mutipatse ife lero chakudya chathu chalero’ kuti tikhale ndi moyo. Mulungu ankatithandizadi kupeza chakudya monga mmene Yesu analonjezera. Nthawi zambiri sitinkapeza zakudya za kumtima kwathu. Ndikukumbukira kuti tsiku lina nditapita kokagula chakudya, ndinakhala pamzere ndisakudziwa n’komwe kuti akugulitsa chakudya chanji. Nditafika kutsogolo, ndinangoona kuti akugulitsa yogati yekhayekha. Sindikonda yogati koma ndinagulabe popeza chinali chakudya, moti tsiku limenelo tinagonera yogatiyo. Ndikuthokoza Mulungu kuti kwa nthawi yonseyi, ine ndi banja langa sitinagonepo ndi njala.”a
Mulungu walonjeza kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.”—Aheberi 13:5
“Panopa zinthu zayamba kutiyendera bwino. Koma pa nthawi yonse imene tinali ndi vuto la ndalama, taphunzira kuti kudalira Mulungu ndi kofunika kuti munthu usamade nkhawa kwambiri. Tikamachita zimene Yehovab amafuna, iye nthawi zonse amatithandiza. Taona kuti lemba la Salimo 34:8 limanenadi zoona. Lembali limati: ‘Talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino. Wodala ndi munthu wamphamvu amene amathawira kwa iye.’ Sitida nkhawa kuti tidzatani tikadzakumananso ndi vuto la kusowa kwa ndalama.
Mulungu amathandiza atumiki ake okhulupirika kupeza chakudya cha tsiku lililonse
“Tazindikira kuti anthufe timafunikira chakudya kuti tikhale ndi moyo osati ntchito kapena ndalama. Mulungu analonjeza kuti: ‘Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri.’ Tidzasangalala kwambiri lonjezo limeneli likadzakwaniritsidwa. Koma panopa tikakhala ‘ndi chakudya, zovala ndi pogona, timakhala okhutira ndi zinthu zimenezi.’ Timalimbikitsidwanso ndi mawu a m’Baibulo akuti: ‘Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo. Pakuti Mulungu anati: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” Moti tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa.”’”c
Kuti ‘tiyende ndi Mulungu’ ngati mmene Paul ndi banja lake anachitira, tifunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. (Genesis 6:9) Kaya panopa tikuda nkhawa chifukwa cha vuto la kusowa kwa ndalama, kapena ngati m’tsogolo titadzakumana ndi vutoli, chikhulupiriro komanso nzeru zimene Paul anasonyeza, zingatiphunzitse zinthu zofunika kwambiri.
Kodi tingatani ngati tikuda nkhawa chifukwa cha mavuto a m’banja?
a Onani Mateyu 6:11, 34.
b Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova.
-
-
Kuda Nkhawa Chifukwa cha Mavuto a M’banjaNsanja ya Olonda—2015 | July 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIYANI CHINGATITHANDIZE TIKAKHALA NDI NKHAWA?
Kuda Nkhawa Chifukwa cha Mavuto a M’banja
Janet ananena kuti: “Patangopita nthawi yochepa bambo anga atamwalira, mwamuna wanga anandiuza kuti akufuna kukwatira mkazi wina. Kenako anangotenga zovala zake n’kundisiya ndi ana athu awiri osatsanzika n’komwe.” Janet anapeza ntchito koma ankalandira ndalama zochepa moti sankakwanitsa kusamalira ana ake bwinobwino. Janet anakumana ndi mavuto enanso ambiri. Iye anati: “Ndinayamba kuda nkhawa kwambiri poganizira kuti ndili ndi udindo waukulu wolera ndekha ana. Ndinkadziimba mlandu chifukwa ndinkaona kuti ndikulephera kusamalira ana anga ngati mmene makolo ena amachitira. Ndipo ngakhale panopa ndimadabe nkhawa ndi mmene anthu amaonera ineyo ndi ana anga. Ndimaganiza kuti ena samandimvetsa ndipo amaganiza kuti ndinapasula banja ndi manja anga.”
Janet
Janet amakonda kupemphera kwa Mulungu. Zimenezi zimamuthandiza kuti azikondabe Mulungu komanso asamade nkhawa mopitirira malire. Iye anati: “Ndimavutika kwambiri ndi nkhawa makamaka usiku chifukwa ana amakhala atagona ndipo zoganiza zimandichulukira. Koma kupemphera ndi kuwerenga Baibulo kumandithandiza kuti ndipeze tulo. Lemba limene limanditonthoza kwambiri ndi la Afilipi 4:6, 7, lomwe limati: ‘Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.’ Ndimakonda kupemphera usiku uliwonse ndipo ndimaona kuti Yehova amanditonthoza ndi kundipatsa mtendere.”
Pa Ulaliki wa Paphiri, Yesu ananena mawu olimbikitsa okhudza kupemphera omwe angathandize anthu onse amene ali ndi nkhawa. Iye anati: “Atate wanu amadziwa zimene mukufuna musanapemphe n’komwe.” (Mateyu 6:8) Ngakhale kuti Yehova amadziwa zimene tikufuna, tiyenera kumupemphabe chifukwa pemphero ndi njira yofunika kwambiri kuti ‘tiyandikire Mulungu.’ Tikatero nayenso ‘adzatiyandikira.’—Yakobo 4:8.
Pemphero limathandizanso m’njira zambiri. Yehova, yemwe ndi “Wakumva pemphero,” amathandiza anthu onse amene amamufunafuna ndi chikhulupiriro. (Salimo 65:2) Mpake kuti Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti “azipemphera nthawi zonse, osaleka.” (Luka 18:1) Choncho tisasiye kupempha Mulungu kuti azititsogolera ndi kutithandiza, ndiponso tisamakayikire kuti adzatipatsa mphoto chifukwa chakuti timamukhulupirira. Tizikhulupiriranso kuti amafunitsitsa kutithandiza tikakhala pamavuto. Timasonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba ‘tikamapemphera mosalekeza.’—1 Atesalonika 5:17.
KODI KUKHALA NDI CHIKHULUPIRIRO KUMATANTHAUZA CHIYANI?
Kodi kukhulupirira Mulungu kumatanthauza chiyani? Kumatanthauza “kudziwa” Mulungu kuti ndi weniweni. (Yohane 17:3) Kuti zimenezi zitheke tiyenera kudziwa maganizo a Mulungu, ndipo tingawadziwe tikamaphunzira Baibulo. Kuphunzira Baibulo kungatithandize kuzindikira kuti Mulungu amaona aliyense payekha ndipo amafunitsitsa kutithandiza. Kukhala ndi chikhulupiriro sikutanthauza kungodziwa zinazake zokhudza Mulungu. Koma kumatanthauzanso kumuona kuti ndi mnzathu wapamtima. Kuti munthu winawake akhale mnzathu wapamtima zimatenga nthawi yaitali. Mofanana ndi zimenezi, pamatenganso nthawi kuti ubwenzi wathu ndi Mulungu ukule. Chikhulupiriro chathunso ‘chimawonjezeka’ tikamaphunzira za iye, tikamachita “zinthu zomukondweretsa” komanso tikamaona mmene akutithandizira. (2 Akorinto 10:15; Yohane 8:29) Chikhulupiriro chotere ndi chimene chinathandiza Janet pa nthawi imene anali ndi nkhawa.
Janet anati: “Kuona mmene Yehova wandithandizira pa zinthu zosiyanasiyana ndi kumene kwandithandiza kuti ndikhale ndi chikhulupiriro cholimba. Nthawi zambiri tinkachitidwa zinthu zopanda chilungamo zimene tinkaona ngati sitingathe kuzipirira. Tikapemphera, Yehova ankatithandiza kuti zinthu ziyambenso kutiyendera bwino kuposa mmene tinkaganizira. Ndikamapemphera pandekha, ndimamuthokoza ndipo zimenezi zimandithandiza kukumbukira zinthu zabwino zimene watichitira. Nthawi zambiri amatithandiza pamene zinthu zatikoka manja ndipo tasoweratu mtengo wogwira. Yehova wandipatsanso anzanga enieni omwenso ndi atumiki ake. Iwo amandithandiza nthawi zonse ndipo ali ndi makhalidwe osiririka amene ana anga angatengere.”a
“Panopa ndikumvetsa chifukwa chimene pa Malaki 2:16, Yehova ananena kuti ‘ndimadana ndi zakuti anthu azithetsa mabanja.’ Kwa anthu okwatirana, wosalakwayo amakhala ngati wagwiritsidwa fuwa lamoto. Tsopano patha zaka zambiri ndithu kuchokera pamene amuna anga anandithawa, koma nthawi zina ndimasowabe wocheza naye ndipo ndimaona kuti ndine munthu wosafunika. Ndikayamba kudziona chonchi, ndimayesetsa kuthandiza winawake ndipo zimenezi zimachititsa kuti ndisinthe mmene ndimadzionera.” Janet amayesetsa kutsatira mfundo yopezeka m’Baibulo yakuti sibwino kudzipatula. Ndipo zimenezi zimamuthandiza kuti asamade nkhawa mopitirira malire.b—Miyambo 18:1.
Mulungu ndi “Tate wa ana amasiye ndi woweruzira akazi amasiye milandu.”—Salimo 68:5
Janet anati: “Mawu akuti Mulungu ndi ‘tate wa ana amasiye ndi woweruzira akazi amasiye milandu’ amandilimbikitsa kwambiri. Ndimadziwa kuti iye sangatisiye ngati mmene amuna anga anatisiyira.” (Salimo 68:5) Janet amadziwanso kuti Mulungu satiyesa “ndi zinthu zoipa” koma amapereka nzeru “mowolowa manja kwa onse” ndiponso amatipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti tisamade nkhawa kwambiri.—Yakobo 1:5, 13; 2 Akorinto 4:7.
Kodi tingatani ngati tili ndi nkhawa chifukwa chakuti moyo wathu uli pangozi?
a Onani 1 Akorinto 10:13; Aheberi 4:16.
b Kuti mupeze mfundo zina zokuthandizani mukakhala ndi nkhawa, onani nkhani ya pachikuto ya mutu wakuti, “Kodi Mumatani Mukakumana ndi Mavuto?” mu Galamukani! ya July 2015 yomwe ili pa www.pr418.com/ny.
-
-
Kuda Nkhawa Chifukwa cha Zinthu ZoopsaNsanja ya Olonda—2015 | July 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIYANI CHINGATITHANDIZE TIKAKHALA NDI NKHAWA?
Kuda Nkhawa Chifukwa cha Zinthu Zoopsa
Alona ananena kuti: “Ndikangomva phokoso la masayilini, ndimachita mantha kwambiri ndipo ndimathamangira m’chipinda chobisalirako mabomba akamaphulika. Ngakhale nditabisala kumeneko ndimakhalabe ndi nkhawa. Koma ndimakhala ndi nkhawa kwambiri ndikamamva kulira kwa masayilini ndili kwina. Tsiku lina ndikuyenda mumsewu, ndinayamba kumva kulira kwa sayilini ndipo ndinayamba kulira mpaka kubanika. Panatenga maola ambiri kuti mtima wanga ukhale m’malo ndipo posakhalitsa masayilini aja anayambiranso kulira.”
Alona
Pali zinthu zinanso zambiri zimene zingatidetse nkhawa. Mwachitsanzo, mukadziwa kuti inuyo kapena wachibale wanu akudwala matenda oopsa, mungayambe kuda nkhawa kwambiri. Koma anthu ena amada nkhawa chifukwa choopa zimene zingadzawachitikire m’tsogolo. Iwo amaganiza kuti, ‘Kodi ana athu ndi zidzukulu zathu adzakhalabe m’dziko la nkhondo, matenda oopsa, loonongeka chifukwa cha kusintha kwa nyengo, komanso limene anthu ambiri ndi osamvera malamuloli?’ Kodi tingatani ngati tili ndi nkhawa chifukwa cha zinthu zimenezi?
Ngakhale kuti palibe chimene tingachite kuti zinthu zoipa zisamachitike Baibulo limati, “wochenjera amene waona tsoka amabisala.” (Miyambo 27:12) Mofanana ndi mmene timatetezera thupi lathu kuti lisavulale, tizitetezanso maganizo ndi mtima wathu ku zinthu zoipa. Kuona zinthu zachiwawa komanso nkhani za pa TV zosonyeza zithunzi zoopsa kungapangitse kuti ifeyo komanso ana athu tikhale ndi nkhawa. Tikamapewa kuona zithunzi zoopsa, sizitanthauza kuti sitidera nkhawa anthu amene akukumana ndi zoopsawo. Kungoti anthufe sitinalengedwe kuti tizingoona zinthu zoopsa. Choncho m’malo moganizira zinthu zoopsa, tiyenera kumaganizira “zinthu zilizonse zoona, . . . zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zachikondi.” Tikamachita zimenezi, “Mulungu wamtendere” adzatipatsa mtendere wa m’maganizo ndi wa mumtima.—Afilipi 4:8, 9.
PEMPHERO NDI LOTHANDIZA
Kukhulupirira kwambiri Mulungu kumatithandiza kuti tisamakhale ndi nkhawa kwambiri. Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Khalani maso kuti musanyalanyaze kupemphera.” (1 Petulo 4:7) Tizipempha Mulungu kuti atithandize, atipatse nzeru komanso mphamvu kuti tikhale olimba mtima pothana ndi mavuto athu. Tizikhulupirira ndi mtima wonse kuti iye “amatimvera tikapempha chilichonse.”—1 Yohane 5:15.
Ndi mwamuna wake dzina lake Avi
Baibulo limanena kuti Satana ndiye “wolamulira wa dzikoli” osati Mulungu. Limanenanso kuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (Yohane 12:31; 1 Yohane 5:19) Mpake kuti Yesu anati tizipemphera kuti: “Mutilanditse kwa woipayo.” (Mateyu 6:13) Alona ananena kuti: “Ndikamva kulira kwa masayilini, ndimapemphera kuti Yehova andithandize kuti mtima ukhale m’malo. Komanso amuna anga amabwera pafupi n’kupemphera nane. Pemphero limathandiza kwambiri. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye. Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’choonadi.”—Salimo 145:18.
ZINTHU ZABWINO ZIMENE TIKUZIYEMBEKEZERA
Pa Ulaliki wa Paphiri, Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere.” (Mateyu 6:10) Ufumu wa Mulungu udzachotseratu zinthu zonse zimene zimatidetsa nkhawa. Mulungu adzagwiritsa ntchito Yesu yemwe ndi “Kalonga Wamtendere” kuti adzathetse “nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Yesaya 9:6; Salimo 46:9) “Mulungu adzakhala woweruza pakati pa mitundu yambiri ya anthu . . . Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo. . . . Sipadzakhala wowaopsa.” (Mika 4:3, 4) Mabanja azidzakhala mosangalala ndipo “adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.” (Yesaya 65:21) Ndipotu “palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”—Yesaya 33:24.
Masiku ano, pali zinthu zambiri zothandiza anthu kudziwiratu zinthu zoopsa zimene zingachitike. Koma n’zosatheka kupeweratu “zinthu zosayembekezereka” kapena kupewa kukhala malo olakwika pa nthawi yolakwikanso. (Mlaliki 9:11) Kwa zaka zambiri, ngakhale anthu osalakwa akhala akufa chifukwa cha nkhondo, chiwawa komanso matenda. Kodi anthu amenewa adzakhalanso ndi moyo?
Anthu amene anafa ndi ochuluka kwambiri ndipo Mulungu yekha ndi amene akudziwa chiwerengero chawo. Onsewa adzakhalanso ndi moyo. Panopa zili ngati akugona, ndipo Mulungu amawakumbukirabe mpaka pa tsiku limene “onse ali m’manda achikumbutso . . . adzatuluka.” (Yohane 5:28, 29) Pa nkhani ya kuuka kwa akufa, Baibulo limatitsimikizira kuti: “Chiyembekezo chimene tili nachochi chili ngati nangula wa miyoyo yathu ndipo n’chotsimikizika ndiponso chokhazikika.” (Aheberi 6:19) Ndipo Mulungu “wapereka chitsimikizo kwa anthu onse mwa kumuukitsa [Yesu] kwa akufa.”—Machitidwe 17:31.
Panopa, aliyense kuphatikizapo amene amayesetsa kusangalatsa Mulungu amakhala ndi nkhawa. Paul, Janet, ndi Alona amakhalabe osangalala ngakhale kuti anakumanapo ndi zinthu zodetsa nkhawa kwambiri. Izi zatheka chifukwa amachita zinthu zothandiza kuchepetsa nkhawa, amapemphera kwa Mulungu ndiponso amakhulupirira kwambiri zimene Mulungu analonjeza m’Baibulo kuti adzachita m’tsogolo. Ngati inunso muli ndi nkhawa, “Mulungu amene amapereka chiyembekezo akudzazeni ndi chimwemwe chonse ndi mtendere wonse chifukwa cha kukhulupirira kwanu.”—Aroma 15:13.
-