-
Kodi kudziwa zimene Baibulo limanena kungakuthandizeni bwanji?Nsanja ya Olonda—2015 | December 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI N’ZOTHEKA KUMVETSA ZIMENE BAIBULO LIMANENA?
Baibulo Ndi Buku Lothandiza Kwambiri
Mayi wina wa ku China, dzina lake Lin anati: “Ndimadziwa ndithu kuti Baibulo ndi buku limene anthu ambiri opemphera amaligwiritsa ntchito koma ndimaona kuti ndi lothandiza m’mayiko ena osati ku China kuno.”
Bambo wina wa ku India, dzina lake Amit, ananena kuti: “Ngati ndimalephera kumvetsa mabuku a chipembedzo changa chachihindu, ndiye kuli bwanji Baibulo?”
Mayi wina wa ku Japan, dzina lake Yumiko anati: “Ndimangomva zoti Baibulo ndi buku lakale komanso kuti anthu ambiri ali nalo. Koma chibadwire sindinalionepo.”
Padzikoli anthu ambiri ali ndi Baibulo ndipo amaona kuti ndi lofunika. Ngakhale zili choncho, anthu ambiri a m’mayiko a ku Asia amadziwa zochepa kwambiri ndipo ena sadziwa n’komwe zimene Baibulo limanena. Ndipo n’zodabwitsanso kwambiri kuti m’mayiko omwe Baibulo ndi buku lofala kwambiri, anthu owerengeka chabe ndi amene amadziwa zimene limanena.
Ndiye mwina mungafunse kuti, ‘Kodi kudziwa zimene Baibulo limanena kungandithandize bwanji?’ Kumvetsa zimene Baibulo limanena kungakuthandizeni:
Kudziwa zimene mungachite kuti muzisangalala
Kukhala ndi banja losangalala
Kuti musakhale ndi nkhawa
Kuti muzigwirizana ndi anthu ena
Kuti muzitha kugwiritsa ntchito bwino ndalama
Mayi wina wa ku Japan, dzina lake Yoshiko, ankafuna kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa ndipo anaganiza zongoliwerenga yekha. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Yoshiko anati: “Baibulo landithandiza kudziwa chifukwa chake Mulungu anatilenga komanso zimene tikuyembekezera kutsogoloku. Zimenezi zandithandiza kuti ndizisangalala.” Nayenso Amit amene tamutchula poyamba uja anawerenga Baibulo payekha ndipo ananena kuti: “Nditawerenga Baibulo ndinadabwa nditadziwa kuti ndi buku lothandiza wina aliyense.”
Baibulo lathandiza anthu mamiliyoni ambiri. Inunso lingakuthandizeni ngati mutaliwerenga ndi kumvetsa zimene limanena.
-
-
Baibulo Ndi Buku Lomveka BwinoNsanja ya Olonda—2015 | December 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI N’ZOTHEKA KUMVETSA ZIMENE BAIBULO LIMANENA?
Baibulo Ndi Buku Lomveka Bwino
Baibulo linayamba kulembedwa zaka 3,500 zapitazo ku Middle East. Pa nthawi imene linkayamba kulembedwa n’kuti ufumu wa Shang wa ku China uli wamphamvu kwambiri. Komanso panali patatsala zaka 1,000 kuti chipembedzo chachibuda chiyambe ku India.—Onani bokosi lakuti, “Mfundo Zachidule Zokhudza Baibulo.”
Baibulo lili ndi mayankho a mafunso ofunika kwambiri amene anthu amakhala nawo
Koma mwina mungaganize kuti, ‘Ngati Baibulo lili lakale chonchi, ndiye kuti linatha ntchito.’ Komabe dziwani kuti ngakhale kuti linalembedwa kalekale, ndi lothandizabe kwambiri masiku ano. Ndi lomveka bwino komanso limayankha mogwira mtima mafunso ofunika kwambiri amene anthu amakhala nawo.
Mwachitsanzo, kodi munayamba mwadzifunsapo kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu anatilenga?’ Funso limeneli lakhala likuvutitsa maganizo anthu ambiri. Komatu mungadabwe kudziwa kuti m’Baibulo muli yankho la funsoli ndipo limapezeka m’machaputala awiri oyambirira a buku la Genesis. Mwachidule, machaputala awiriwa amafotokoza zimene zinachitika zaka mabiliyoni apitawo. Baibulo limanena kuti “pa chiyambi,” Mulungu analenga dziko lapansi, nyenyezi komanso zinthu zina za m’mlengalenga. (Genesis 1:1) Kenako anayamba kukonza dzikoli kuti pakhale zamoyo. Atachita zimenezi analenga zamoyo zosiyanasiyana. Pamapeto pake Mulungu analenga anthu n’kuwaika padziko lapansi. Baibulo limafotokozanso cholinga chimene Mulungu anali nacho pamene ankalenga anthu.
LINALEMBEDWA MOMVEKA BWINO
M’Baibulo muli malangizo abwino amene angatithandize tikamakumana ndi mavuto. Malangizo ake ndi osavuta kuwatsatira. Tikunena zimenezi pa zifukwa ziwiri.
Choyamba, Baibulo limanena zinthu momveka bwino komanso mosapita m’mbali. Lili ndi mawu osavuta kumva ndipo likamafotokoza zinthu zovuta, limagwiritsa ntchito mawu omwe anthu amawadziwa bwino.
Mwachitsanzo, Yesu anagwiritsa ntchito zitsanzo komanso mafanizo a zinthu zimene anthu ankazidziwa bwino ndipo zimenezi zinkawagwira mtima kwambiri. Zitsanzo zina komanso mafanizo amenewa anazitchula pa ulaliki wake wa paphiri ndipo m’Baibulo zimapezeka m’buku la Mateyu, machaputala 5 mpaka 7. Munthu wina ananena kuti zimene Yesu ananena pa ulalikiwu “zingatithandize kuti tikhale ndi moyo wabwino.” Mukhoza kuwerenga zimene Yesu ananena pa ulalikiwu, mwina kwa maminitsi 15 kapena 20 okha. Koma mungagome ndi mfundo zake chifukwa n’zomveka bwino komanso zothandiza kwambiri.
Chifukwa chachiwiri chimene chimapangitsa kuti Baibulo likhale lomveka bwino n’choti limafotokoza zochitika zenizeni. Baibulo ndi losiyana kwambiri ndi mabuku a nthano omwe amangofotokoza zinthu zam’maluwa. Buku lina linanena kuti nkhani zambiri za m’Baibulo “zimanena za anthu otchuka komanso ngakhale za anthu wamba.” Limanenanso mavuto amene anthuwo “ankakumana nawo, zimene ankayembekezera, zimene ankalakwitsa ndiponso zimene anachita bwino.” (The World Book Encyclopedia) M’Baibulo mulinso nkhani za anthu komanso zochitika zenizeni zomwe ifeyo tingaphunzirepo kanthu.—Aroma 15:4.
NDI BUKU LIMENE ALIYENSE AKHOZA KULIPEZA
Kuti munthu amvetse zimene buku likunena, bukulo liyenera kukhala m’chinenero chimene munthuyo amachimva bwinobwino. Masiku ano, Baibulo likupezeka m’zinenero zambiri zimene anthu amalankhula padzikoli. Koma kodi zimenezi zimatheka bwanji?
Ntchito yomasulira. Baibulo linalembedwa m’Chiheberi, Chiaramu komanso Chigiriki. Choncho, anthu amene sankadziwa zinenerozi sankamva uthenga wake. Ndiye pofuna kuthandiza anthu amenewa, anthu ena omasulira mabuku anayamba ntchito yomasulira Baibulo m’zinenero zina. Ntchito imene anthuwa anachita ndi yotamandika zedi, chifukwa panopa Baibulo lonse kapena mbali yake, likupezeka m’zinenero pafupifupi 2,700. Zimenezi zikusonyeza kuti pa anthu 100 alionse, anthu 90 akhoza kuwerenga Baibulo m’chinenero chawo.
Ntchito yosindikiza. Poyamba, Baibulo linkalembedwa pa zinthu zosachedwa kuwonongeka monga zikopa komanso pamapepala opangidwa ndi gumbwa. Chifukwa cha zimenezi, nthawi zonse akatswiri okopera mabuku ankayenera kumakopera Baibulo pamanja. Mabuku amenewa ankakhala odula kwambiri moti ndi anthu ochepa chabe amene ankapezeka nawo. Koma zaka zoposa 550 zapitazo, munthu wina dzina lake Gutenberg, anapanga mashini osindikiza mabuku ndipo zimenezi zinathandiza kuti Baibulo lizipezeka mosavuta. Kafukufuku wina anasonyeza kuti kungochokera nthawi imeneyo, Mabaibulo oposa 5 biliyoni kapena mbali yake, afalitsidwa.
Palibenso buku lina lachipembedzo limene limafalitsidwa kuposa Baibulo. Baibulo ndi losiyananso ndi mabuku amenewa chifukwa ndi losavuta kumva komanso limapezeka mosavuta. Ngakhale zili choncho, anthu ena amavutikabe kumvetsa zimene Baibulo limanena. Ngati nanunso mumavutika kulimvetsa, dziwani kuti anthu ena akhoza kukuthandizani. Koma kodi ndi ndani amene angakuthandizeni? Nanga mungapindule bwanji ngati mutamvetsa zimene Baibulo limanena? Werengani nkhani yotsatirayi kuti mudziwe mayankho a mafunso amenewa.
-
-
Mukhoza Kumvetsa Zimene Baibulo LimanenaNsanja ya Olonda—2015 | December 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI N’ZOTHEKA KUMVETSA ZIMENE BAIBULO LIMANENA?
Mukhoza Kumvetsa Zimene Baibulo Limanena
Tiyerekeze kuti mwapita kudziko lachilendo. Muli kumeneko, mukuona kuti anthu ake ndi osiyana kwambiri ndi a kwanu. Zakudya zimene amakonda, chikhalidwe chawo komanso ndalama zimene amagwiritsa ntchito, n’zosiyana kwambiri ndi zimene munazolowera. N’zosakayikitsa kuti zingakuvuteni kuzolowera kukhala m’dziko limenelo. Ndipo sitikukayikira kuti mungakonde kuti munthu wina azikuthandizani.
Nanunso mukhoza kumva chimodzimodzi ngati n’koyamba kuwerenga Baibulo. Zimenezi zikhoza kuchitika chifukwa Baibulo limafotokoza zinthu zimene zinachitika kale kwambiri, zomwenso mwina zingakhale zosiyana ndi zimene zimachitika kwanuko. Mwachitsanzo Baibulo limanena za anthu ena otchedwa Afilisiti, chakudya chotchedwa mana, ndalama zotchedwa madalakima komanso chikhalidwe chachilendo ‘chong’amba zovala’ munthu akakhumudwa ndi zinazake. (Yoswa 13:2; Ekisodo 16:31; Luka 15:9; 2 Samueli 3:31) Monga taonera m’chitsanzo chija, munthu ukapita ku dziko lachilendo umafuna kuti wina azikuthandiza. Ndiye kodi simungakonde kuti munthu wina yemwe amadziwa bwino Baibulo akuthandizeni kumvetsa zimene limanena?
ANTHU AKALE ANKATHANDIZIDWA KUMVETSA MALEMBA
Kungochokera pamene Malemba Opatulika anayamba kulembedwa mu 1513 B.C.E., Mulungu wakhala akuthandiza anthu kumvetsa bwino Malemba. Mwachitsanzo, Mose yemwe ankatsogolera mtundu wa Isiraeli ‘anayamba kufotokozera’ anthu zimene zinalembedwa.—Deuteronomo 1:5.
Kungochokera nthawi imeneyo, Aisiraeli ankakhala ndi anthu oyenerera amene ankawaphunzitsa Malemba. Mwachitsanzo mu 455 B.C.E. gulu la Ayuda, kuphatikizaponso ana, linasonkhanitsidwa pabwalo lina mumzinda wa Yerusalemu. Ndiyeno aphunzitsi a Mawu a Mulungu anayamba “kuwerenga bukulo [Malemba Opatulika aja] mokweza.” Koma si kuti ankangowawerengera, basi n’kusiya. ‘Ankawathandizanso kumvetsa tanthauzo la zimene anali kuwerengazo.’—Nehemiya 8:1-8.
Patapita zaka zambiri, Yesu ankathandiza anthu kumvetsa Mawu a Mulungu ndipo anthu ankamutchula kuti mphunzitsi. (Yohane 13:13) Nthawi zina Yesu ankaphunzitsa anthu monga gulu, koma nthawi zina ankaphunzitsa munthu payekhapayekha. Pa nthawi ina, Yesu anaphunzitsa khamu la anthu pa ulaliki wina womwe unachitikira paphiri. Anthuwo atamva zimene Yesu ananena ‘anakhudzidwa moti anadabwa ndi kaphunzitsidwe kake.’ (Mateyu 5:1, 2; 7:28) Ndiponso m’chaka cha 33 C.E., ophunzira awiri a Yesu ankapita kumudzi wina womwe unali pafupi ndi mzinda wa Yerusalemu. Kenako Yesu anawapeza n’kuyamba ‘kuwafotokozera Malemba momveka bwino.’—Luka 24:13-15, 27, 32.
Nawonso ophunzira a Yesu ankaphunzitsa ena Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, pa nthawi inayake nduna ya ku Itiyopiya inkawerenga mbali ina ya Malemba Opatulika. Kenako wophunzira wa Yesu, dzina lake Filipo, anafika kwa ndunayi n’kuifunsa kuti: “Kodi mukumvetsa zimene mukuwerengazo?” Ndunayo inayankha kuti: “Ndingamvetse bwanji popanda wondimasulira?” Ndiye Filipo anaifotokozera tanthauzo la zimene inali kuwerengazo.—Machitidwe 8:27-35.
NANUNSO MUKHOZA KULIMVETSA BAIBULO
Mofanana ndi anthu akale omwe ankaphunzitsa ena mfundo za m’Malemba, a Mboni za Yehova masiku ano amaphunzitsa anthu Baibulo m’mayiko 239. (Mateyu 28:19, 20) Mlungu uliwonse, amaphunzira Baibulo ndi anthu oposa 9 miliyoni. Ambiri mwa anthuwa amakhala oti si Akhristu. A Mboniwa samalipiritsa kalikonse akamaphunzira Baibulo ndi munthu ndipo amachita zimenezi kunyumba kapena malo ena amene munthu angasankhe kuti aziphunzirirako. Phunziroli limathanso kuchitika munthu ali kwina. Mwachitsanzo, ena amaphunzira kudzera pa foni, kompyuta kapena pa tabuleti.
Kodi nanunso mukufuna kumvetsa zimene Baibulo limanena? Tikukupemphani kuti mufunse wa Mboni za Yehova aliyense kuti akuthandizeni. Ngati mutaphunzira Baibulo ndi a Mboni, mudzaona kuti Baibulo ndi buku ‘lopindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza m’chilungamo.’ Ndi lothandizanso “kuti munthu wa Mulungu akhale woyenerera bwino ndi wokonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.”—2 Timoteyo 3:16, 17.
-