Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kukonzekera Nkhani za Onse
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
    • Kukonzekera Nkhani za Onse

      MLUNGU uliwonse, mipingo yambiri ya Mboni za Yehova imakhala ndi nkhani ya onse pa mutu wochokera m’Malemba. Ngati ndinu mkulu kapena mtumiki wotumikira, kodi mumaonetsa umboni wakuti ndinu wokamba nkhani waluso, mphunzitsi? Ngati mumatero, angakupempheni kuti mukambe nkhani ya onse. Sukulu ya Utumiki wa Mulungu yathandiza zikwizikwi za abale kuti ayenerere utumiki umenewu. Mukapatsidwa nkhani ya onse, kodi muyenera kuyambira pati kukonzekera?

      Iŵerengeni ndi Kuimvetsa Bwino Autilainiyo

      Musanayambe kufufuza kulikonse, ŵerengani autilainiyo ndipo musinkhesinkhe kufikira mutamvetsa mfundo yake yaikulu. Sungani m’maganizo mutu wake. Kodi n’chiyani chimene mukayenera kuphunzitsa omvera anu? Kodi cholinga chanu n’chiyani?

      Mvetsetsani mitu ya m’katiyo. Zimenezo ndizo mfundo zazikulu, choncho zipendeni mofatsa. Kodi iliyonse imagwirizana motani ndi mutu waukulu? Pansi pa mfundo yaikulu iliyonse, pandandalikidwa mfundo zina zing’onozing’ono. Malingaliro ochirikiza mfundo zing’onozing’ono zimenezi andandalikidwa pansi pake. Onani mmene chigawo chilichonse cha autilainiyo chikutulukira m’chigawo chapamwamba ndi mmene chikuloŵera m’chigawo chotsatira, ndi mmenenso chikuthandizira kukwaniritsa cholinga cha nkhaniyo. Mutazindikira bwino mutu wa nkhani, cholinga cha nkhaniyo, ndi mmene mfundo zazikulu zikukwaniritsira cholingacho, ndiye kuti mwakonzeka kuyamba kuikonza nkhani yanu.

      Choyamba, mungachite bwino kuiona nkhani yanu ngati nkhani zinayi kapena zisanu zifupizifupi, iliyonse yokhala ndi mutu wake. Zikonzekereni payokhapayokha.

      Autilainiyo yangokhala chipangizo chokonzekerera. Si manotsi akuti muzikambirapo nkhani yanu ayi. Yangokhala ngati mafupa okhaokha, titero kukamba kwake. Ndiye mufunikira kuikamo mnofu, mtima, ndi mpweya kuti ikhale yamoyo.

      Kugwiritsa Ntchito Malemba

      Yesu Kristu ndi ophunzira ake anali kuphunzitsa kuchokera m’Malemba. (Luka 4:16-21; 24:27; Mac. 17:2, 3) Mukhoza kutero inunso. Malemba ayenera kukhala maziko a nkhani yanu. M’malo mongofotokoza mawu a pa autilaini yoperekedwayo ndi kusonyeza mmene amagwirira ntchito, onani mmene Malemba amachirikizira mawuwo, ndiyeno phunzitsani kuchokera pa Malembawo.

      Pokonzekera nkhani yanu, ŵerengani ndi kupenda lemba lililonse losagwidwa mawu pa autilainipo. Onetsetsani nkhani yake ya lembalo. Malemba ena amangopereka mfundo zongopereka chithunzi chokwanira. Si onse amene muyenera kuŵerenga kapena kulankhulapo pokamba nkhani yanu. Sankhani okhawo amene angathandize kwambiri omvera anu. Ngati mukonzekera bwino lomwe malemba osagwidwa mawu a pa autilaini, simungafunikire kwenikweni kutenganso kwina Malemba ena owonjezerapo.

      Kuti nkhani yanu ikhale yogwira mtima, sizidalira kwenikweni kuchuluka kwa malemba oŵerengedwa, koma luso la kuphunzitsa. Potchula lemba loti muŵerenge, nenani chifukwa choliŵerengera. Fotokozani mmene tingaligwiritsire ntchito. Mutaŵerenga lemba, Baibulo lanu likhale chitsegukire pamene mukufotokoza lembalo. Mwachidziŵikire, omvera anu adzachitanso chimodzimodzi. Kodi mungalimbikitse motani chidwi cha omvera anu ndi kuwathandiza kuti apindule kwathunthu ndi Mawu a Mulungu? (Neh. 8:8, 12) Mungatero mwa kuwafotokozera lemba, kuperekapo chitsanzo, ndi kuwaonetsa mmene tingaligwiritsire ntchito.

      Kufotokozera. Pokonzekera kufotokozera lemba lofunika, dzifunseni kuti: ‘Kodi limatanthauzanji? N’chifukwa chiyani ndikuligwiritsa ntchito m’nkhani yangayi? Kodi omverawo angakhale akudzifunsa zotani pa vesiyi?’ Mungafunikire kupenda mavesi ozungulira, zochitika za m’lembalo, malo a zochitikazo, mphamvu ya mawuwo, ndi cholinga cha wolemba wake. Zimenezi zimalira kufufuza. Mudzapeza mfundo zothandiza zankhaninkhani m’mabuku ofalitsidwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45-47) Musayese kufotokoza zonse zokhudza vesiyo, koma fotokozani chimene mwapemphera omvera anu kuti aiŵerenge, malinga ndi mfundo imene mukukambirana.

      Kuperekapo Chitsanzo. Cholinga cha zitsanzo ndicho kuthandiza omvera anu kumvetsa lingaliro lozamirapo kapena kuwathandiza kukumbukira mfundo ina imene mwaifotokoza. Zitsanzo zimathandiza anthu kumvetsa zimene mwawauza ndi kuzigwirizanitsa ndi zimene akuzidziŵa kale. Umu ndi mmene Yesu anachitira pa Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri. Mawu akuti “mbalame za kumwamba,” “maluŵa akuthengo,” “chipata chopapatiza,” ‘nyumba yomangidwa pathanthwe,’ limodzi ndi mawu ena ambirimbiri anapangitsa kuphunzitsa kwake kukhala kotsindika, komvekera bwino, ndi kosaiŵalika.—Mat., macha. 5–7.

      Kuonetsa Mmene Tingawagwiritsire Ntchito. Kufotokozera lemba ndi kuperekapo chitsanzo kumaphunzitsa zambiri, koma kugwiritsa ntchito zimene taphunzira n’kumene kumabala zipatso. Zoona, ndi udindo wa omvera anu kuchitapo kanthu pa uthenga wa m’Baibulo umene akumvera, komabe mukhoza kuwathandiza kuzindikira zimene ayenera kuchita. Mutatsimikiza kuti omvera anu amvetsa vesi imene mwafotokozayo ndipo aona mmene ikugwirizanira ndi mfundo yanu, aonetseni mmene imakhudzira chikhulupiriro chathu ndi khalidwe lathu. Unikani mapindu ake a kusiya maganizo kapena khalidwe lolakwika losemphana ndi choonadi chimene mukufotokoza.

      Pamene mukulingalira za mmene mungagwiritsire ntchito malembawo, kumbukirani kuti omvera anuwo anakula mosiyanasiyana ndipo mikhalidwe ya moyo wawo n’njosiyanasiyananso. Mwa iwo mungakhale atsopano, achinyamata, okalamba, ndi aja omwe akulimbana ndi mavuto osiyanasiyana pamoyo wawo. Nkhani yanu ikhale yothandiza ndi yonena zenizeni. Peŵani kupereka uphungu womveka ngati muli ndi anthu oŵerengeka chabe m’maganizo.

      Zimene Wokamba Nkhani Ayenera Kusankha

      Zinthu zina zokhudza nkhani yanu anakusankhirani kale. Mfundo zazikulu n’zosonyezedwa bwino lomwe, ndipo nthaŵi imene muyenera kuwonongera pa mutu waung’ono uliwonse yasonyezedwanso bwinobwino. Koma zinthu zina muyenera kusankha nokha. Mungasankhe kuwonongera nthaŵi yochulukirapo pa mutu waung’ono wina kusiyana ndi mitu ina. Musaganize kuti muyenera kumveketsa bwino mfundo ya mutu waung’ono uliwonse mofanana. Zimenezo zingakupangitseni kudutsa mofulumira pa mfundo zanu ndi kuwasiya m’malere omvera anu. Kodi mungadziŵe bwanji mutu waung’ono umene mungafotokozepo mfundo zambiri ndi umene mungafotokoze mwachidule, kapena mongodutsa? Dzifunseni kuti: ‘Ndi mfundo ziti zimene zingandithandize kumveketsa lingaliro lalikulu la nkhaniyi? Nanga zimene zikuoneka kuti zingapindulitse kwambiri omvera anga ndi ziti? Kodi kuchotsapo lemba lina losagwidwa mawu ndi mfundo zake kungafooketse tsatanetsatane wa umboni umene ukuperekedwa?’

      Yesetsani kwambiri kusaloŵetsapo nkhambakamwa kapena maganizo anuanu. Ngakhaletu Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, anapeŵa kulankhula za ‘iye yekha.’ (Yoh. 14:10) Dziŵani kuti chifukwa chimene anthu amafikira pamisonkhano ya Mboni za Yehova n’chakuti adzamve mfundo za m’Baibulo. Ngati inuyo mumadziŵika ngati wodziŵa kukamba bwino nkhani, mwachidziŵikire n’chifukwa chakuti nkhani zanu sizikopera maganizo a anthu kwa inu mwini, koma ku Mawu a Mulungu. Pachifukwa chimenechi, anthu amazikonda nkhani zanu.—Afil. 1:10, 11.

      Popeza kuti mu autilaini ya mafupa okhaokhayo mwaikamo mnofu wa malongosoledwe a Malemba, tsopano mufunikira kuyeseza nkhani yanu. N’kothandiza kuchita zimenezo motulutsa mawu. Koma chofunikira ndicho kutsimikiza kuti mfundo zonse mwazisunga bwino lomwe m’maganizo mwanu. Mufunikira kukamba nkhani yanu mwachidaliro, mwaumoyo, ndi kufotokoza choonadi mosangalala. Musanakambe nkhani yanu, dzifunseni kuti: ‘Kodi cholinga changa n’chiyani? Kodi mfundo zazikulu zikuonekera? Kodi ndayaladi Malemba kukhala maziko a nkhani yanga? Kodi mfundo yaikulu iliyonse imatsogolera moonekera bwino ku inzake? Kodi nkhaniyi idzathandizadi anthu kuŵirikiza chiyamikiro chawo kwa Yehova ndi zogaŵira zake? Kodi mawu omaliza akukhudzana mwachindunji ndi mutu wake. Kodi akusonyeza omvera zimene ayenera kuchita, ndi kuwalimbikitsa kukachita zimenezo?’ Ngati mungayankhe kuti inde pa mafunso ameneŵa, ndiye kuti mwakonzeka ‘kunena bwino zimene mudziŵa,’ kuti mupindulitse mpingo ndi kuti Yehova atamandike!—Miy. 15:2.

  • Kulitsani Luso la Kuphunzitsa
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
    • Kulitsani Luso la Kuphunzitsa

      KODI cholinga chanu ngati mphunzitsi n’chiyani? Ngati mwangokhala kumene wofalitsa Ufumu, mosakayika mukulakalaka kudziŵa mmene mungachititsire phunziro la Baibulo lapanyumba, chifukwa Yesu anapatsa otsatira ake ntchito yopanga ophunzira. (Mat. 28:19, 20) Ngati munayamba kale kuigwira ntchito imeneyi, mwina cholinga chanu ndi kukulitsa luso lofika pamtima anthu amene mumayesa kuwathandiza. Ngati ndinu kholo, muyenera kuti mukufuna kukhala mphunzitsi amene angathe kulimbikitsa ana ake kupereka miyoyo yawo kwa Mulungu. (3 Yoh. 4) Ngati ndinu mkulu kapena ngati mukukalamira ukulu, mwinamwake mukufuna kudzakhala wokamba nkhani amene angamathe kuthandiza omvera ake kuzamitsa chiyamikiro chawo kwa Yehova ndi njira zake. Kodi zolinga zimenezi mungazikwaniritse motani?

      Tengerani phunziro kwa Mphunzitsi Wamkulu, Yesu Kristu. (Luka 6:40) Kaya Yesu anali kulankhula ku khamu la anthu kumbali kwa phiri kapena kwa anthu oŵerengeka chabe poyenda m’njira, zimene anali kunena komanso njira imene anali kuzinenera zinali kuzikika mozama m’maganizo mwa omvera ake. Yesu anakhudza maganizo ndi mitima ya omvera ake, ndipo anasonyeza mmene zimene anaphunzitsazo zingagwirire ntchito. Anachita zimenezo m’njira imene omverawo anatha kumvetsa bwino lomwe. Kodi inunso mungachite chimodzimodzi?

      Dalirani Yehova

      Luso la Yesu la kuphunzitsa linapita patsogolo chifukwa cha chikondi chozama chimene anali nacho kwa Atate wake wakumwamba komanso chifukwa cha chithandizo cha mzimu wa Mulungu. Kodi inunso mumapemphera ndi mtima wonse kwa Yehova kuti muzitha kuchititsa phunziro la Baibulo lapanyumba mogwira mtima? Ngati ndinu kholo, kodi mumapemphera nthaŵi zonse kuti Mulungu akutsogolereni pophunzitsa ana anu? Kodi mumapemphera mochokera pansi pa mtima pokonzekera kukakamba nkhani kapena kukachititsa misonkhano? Podalira pemphero kwa Yehova, mungathe kukhala mphunzitsi weniweni wogwira mtima.

      Kudalira Yehova kumaonekeranso mwa kudalira Mawu ake, Baibulo. M’pemphero limene anapereka madzulo otsiriza a moyo wake monga munthu wangwiro, Yesu anati kwa Atate wake: “Ndawapatsa iwo mawu anu.” (Yoh. 17:14) Ngakhale kuti Yesu anali kudziŵa zambiri, sanalankhulepo konse za iye yekha. Nthaŵi zonse analankhula zimene Atate wake anam’phunzitsa, akumatisiyira chitsanzo choti titengere. (Yoh. 12:49, 50) Mawu a Mulungu, osungidwa m’Baibulo, ali ndi mphamvu yolimbikitsa anthu—zochita zawo, malingaliro awo, ndi mitima yawo. (Aheb. 4:12) Pamene mukukula m’kudziŵa Mawu a Mulungu ndi kuphunzira kulunjika nawo mu ulaliki, mudzakhala mukukulitsa luso la kuphunzitsa limene limakopera anthu kwa Mulungu.—2 Tim. 3:16, 17.

      Lemekezani Yehova

      Kukhala mphunzitsi potengera Kristu sikutanthauza kungodziŵa kukamba nkhani zosangalatsa. Zoona, anthu anachita chidwi ndi “mawu achisomo” a Yesu. (Luka 4:22) Koma kodi cholinga cha Yesu polankhula mwaluso choncho chinali chiyani? Anafuna kulemekeza Yehova, osati kuti atchuke kwa anthu ayi. (Yoh. 7:16-18) Ndipo analimbikitsa otsatira ake kuti: ‘Muŵalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.’ (Mat. 5:16) Uphungu umenewu uyenera kutithandiza pa kaphunzitsidwe kathu. Tiyenera kupeŵa chilichonse chimene chingatipatutse pa cholinga chimenecho. Choncho, polingalira za chimene tikufuna kunena kapena mmene tingachinenere, ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi chimenechi chidzathandiza kukulitsa chiyamikiro kwa Yehova, kapena chidzachititsa anthu kuganiza kwambiri za ine?’

      Mwachitsanzo, zitsanzo ndi zochitika zenizeni m’moyo zingagwiritsidwe ntchito pofuna kuphunzitsa mogwira mtima. Komabe, ngati tifotokoza chitsanzo chachitali kwambiri, kapena ngati tilongosola mbali iliyonse ya chochitika, mfundo imene tikufuna kuphunzitsa ingatayike. Komanso, kusimba nkhani zongofuna kuseketsa anthu kumatipatutsa pa cholinga cha utumiki wathu. Mphunzitsi akamatero, amakopera chidwi cha anthu kwa iye mwini m’malo mokwaniritsa cholinga cha maphunziro auzimu.

      “Musiyanitse”

      Kuti munthu akhale wophunzira weniweni, afunikira kumvetsa bwino lomwe zimene akuphunzitsidwa. Ayenera kumva choonadi ndi kuonanso mmene chimasiyanirana ndi ziphunzitso zina. Kusiyanitsa zinthu kumathandiza pambali imeneyi.

      Mobwerezabwereza, Yehova analangiza anthu ake kuti “musiyanitse” pakati pa choyera ndi chodetsedwa. (Lev. 10:9-11) Iye anati aja amene adzatumikira m’kachisi wake wamkulu wauzimu adzaphunzitsa anthu ‘kusiyanitsa pakati pa chinthu chopatulika ndi chodetsedwa.’ (Ezek. 44:23) Buku la Miyambo lili ndi zinthu zambiri zoonetsa kusiyana pakati pa chilungamo ndi kuipa, pakati pa nzeru ndi kupusa. Ngakhale pakati pa zinthu zosatsutsana, pamakhalabe kusiyana kwa china ndi chinzake. Mtumwi Paulo anasonyeza kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi munthu wabwino, malinga ndi zimene zalembedwa pa Aroma 5:7. M’buku la Ahebri, iye anasonyeza kuti utumiki waunsembe wa Kristu umaposa uja wa Aroni. Inde, n’zogwirizana ndi zimene mphunzitsi wina wa m’zaka za m’ma 1600, John Amos Comenius, analemba kuti: “Kuphunzitsa kumangotanthauza kusonyeza mmene zinthu zimasiyanirana china ndi chinzake, pa zolinga zake, mitundu yake, ndi magwero ake. . . . Choncho, wodziŵa kusiyanitsa amadziŵa kuphunzitsa.”

      Mwachitsanzo, tinene kuti mukuphunzitsa munthu za Ufumu wa Mulungu. Ngati munthuyo sadziŵa kuti Ufumuwo n’chiyani, mungafunikire kum’sonyeza mfundo za m’Baibulo zotsutsa lingaliro lakuti Ufumuwo wangokhala mtima wa munthu. Kapena mungam’sonyeze mmene Ufumuwo umasiyanirana ndi maboma a anthu. Koma kwa anthu amene amadziŵa kale mfundo zoyambirira za choonadi zimenezo, mungafike nawo pa mfundo zozamirapo. Mungawasonyeze mmene Ufumu Waumesiya umasiyanirana ndi ufumu wa Yehova wa chilengedwe chonse, wofotokozedwa pa Salmo 103:19. Komanso mmene umasiyanirana ndi ‘ufumu wa Mwana wa chikondi cha Mulungu,’ wotchulidwa pa Akolose 1:13, kapena mmene umasiyanirana ndi “makonzedwe,” onenedwa pa Aefeso 1:10. Kusiyanitsa zinthu kotereku kungathandize kumveketsa bwino chiphunzitso cha Baibulo chimenechi kwa omvera anu.

      Mobwerezabwereza, Yesu anagwiritsa ntchito kaphunzitsidwe kameneka. Iye anasiyanitsa mmene anthu ambiri anamvera Chilamulo cha Mose ndi cholinga chenicheni cha Chilamulocho. (Mat. 5:21-48) Analekanitsa kulambira koona ndi machitidwe achinyengo a Afarisi. (Mat. 6:1-18) Anasonyezanso kusiyana pakati pa mzimu wa aja amene ‘anachita umbuye’ pa anzawo ndi mzimu wodzimana umene otsatira ake anasonyeza. (Mat. 20:25-28) Pachochitika china, cholembedwa pa Mateyu 21:28-32, Yesu anapempha omvera ake kusiyanitsa okha pakati pa kudzilungamitsa ndi kulapa kwenikweni. Zimenezi zikutifikitsa pa mbali ina yothandiza kwambiri ya kuphunzitsa kwabwino.

      Limbikitsani Omvera Anu Kulingalira

      Pa Mateyu 21:28, timaŵerenga kuti Yesu anayamba kuyerekeza kwake mwa kufunsa kuti: ‘Nanga muganiza bwanji?’ Mphunzitsi waluso samangofikira kupereka zifukwa kapena mayankho. M’malo mwake, amalimbikitsa omvera ake kugwiritsa ntchito luso la kulingalira. (Miy. 3:21; Aroma 12:1) Mbali ina yochitira zimenezi ndiyo kufunsa mafunso. Monga kwalembedwa pa Mateyu 17:25, Yesu anafunsa kuti: ‘Simoni, uganiza bwanji? mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? kwa ana awo kodi, kapena kwa akunja?’ Mafunso a Yesu opangitsa munthu kuganiza anam’thandiza Petro kuzindikira yankho lolondola pankhani ya kupereka msonkho wa pakachisi. Mofananamo, poyankha munthu amene anafunsa kuti, “Mnansi wanga ndani?” Yesu anaonetsa mmene wansembe ndi Mlevi anachitira mosiyana ndi Msamariya uja. Kenako anafunsa kuti, ndi “uti wa awa atatu, uyesa iwe, anakhala mnansi wa iye uja adagwa m’manja a achifwamba?” (Luka 10:29-36) Panonso, posafuna kum’lingalirira womvera wakeyo, Yesu anam’pempha kuti ayankhe yekha funso lake.—Luka 7:41-43.

      Yesetsani Kufika Pamtima

      Aphunzitsi amene amamvetsa lingaliro la Mawu a Mulungu amazindikira kuti kulambira koona si nkhani yongoloŵeza pamtima mfundo zakutizakuti ndi kutsatira malamulo akutiakuti. Kumadalira ubale wabwino ndi Yehova ndi kuzindikira njira zake. Kulambira koteroko kumadaliranso mtima wa munthu. (Deut. 10:12, 13; Luka 10:25-27) M’Malemba, liwu lakuti “mtima” kaŵirikaŵiri limatanthauza umunthu wonse wa munthu, kuphatikizapo zinthu ngati zokhumba zake, chikondi, maganizo, ndi zolinga zake.

      Yesu anadziŵa kuti, pamene anthu amayang’ana maonekedwe akunja, Mulungu amaona zimene zili mumtima. (1 Sam. 16:7) Utumiki wathu kwa Mulungu uyenera kulimbikitsidwa ndi chikondi chathu pa iye, osati kufuna kusangalatsa anthu anzathu ayi. (Mat. 6:5-8) Koma kunena za Afarisi, iwo anachita zinthu zambiri pofuna kudzionetsera. Anasamalira kwambiri za kutsatira mfundo zonse za Chilamulo ndi malamulo amene anawakhazikitsa iwo okha. Koma analephera kusonyeza m’miyoyo yawo makhalidwe abwino amene akanawafananitsa ndi Mulungu yemwe anati anali kum’lambira. (Mat. 9:13; Luka 11:42) Yesu anaphunzitsa kuti, pamene kumvera zofuna za Mulungu n’kofunika, phindu la kumverako limadalira zimene zili m’mtima. (Mat. 15:7-9; Marko 7:20-23; Yoh. 3:36) Ngati titengera chitsanzo cha Yesu, kuphunzitsa kwathu kudzabweretsa mapindu osaneneka. N’kofunika kwambiri kuti tithandize anthu kudziŵa zimene Mulungu amafuna kwa iwo. Koma iwonso afunikira kum’dziŵa ndi kum’konda Yehova kotero kuti khalidwe lawo lionetse kuti ubale wawo ndi Mulungu woona amauona kukhala wamtengo wapatali kwambiri.

      Koma kuti anthu apindule ndi kuphunzitsa koteroko, afunikira kuvomereza zimene zili m’mitima mwawo. Yesu analimbikitsa anthu kuti apende zolinga zawo ndi kusanthula maganizo awo. Pofuna kuwongolera maganizo olakwika, Yesu anafunsa omvera ake chifukwa chimene iwo anaganizira, kapena kunena, kapena kuchita zimene anachitazo. Komabe, posafuna kuwasiya m’malere, anali kuphatikizapo ndemanga, chitsanzo, kapena kuchita chinthu chimene chinawalimbikitsa kuona nkhaniyo moyenerera. (Marko 2:8; 4:40; 8:17; Luka 6:41, 46) Ifenso tikhoza kuthandiza omvera athu mwa kuwapempha kuti azidzifunsa mafunso ngati aŵa: ‘N’chifukwa chiyani njira imeneyi ikuoneka kukhala yabwino kwa ine? N’chifukwa chiyani mkhalidwewu ndikuuona choncho?’ Kenako alimbikitseni kuti aone nkhanizo mmene Yehova amazionera.

      Sonyezani Mmene Zimagwirira Ntchito

      Mphunzitsi wabwino amadziŵa kuti “nzeru ipambana.” (Miy. 4:7) Nzeru ndiyo kugwiritsa ntchito zimene mwaphunzira, kuthetsera mavuto, kupeŵera ngozi, kukwaniritsira zolinga zanu, ndi kuthandizira ena. Ndi udindo wa mphunzitsi kuthandiza ophunzira ake kuchita zimenezo, koma osati kuwasankhira zochita. Pokambirana mfundo za makhalidwe abwino zosiyanasiyana za m’Baibulo, thandizani wophunzirayo kulingalira. Mukhoza kum’patsa chitsanzo cha mkhalidwe wina wake, kenako m’funseni mmene mfundo ya makhalidwe abwino ya m’Baibulo imene mwakambiranayo ingam’thandizire ngati angakumane ndi mkhalidwewo.—Aheb. 5:14.

      M’nkhani yake pa Pentekoste wa mu 33 C.E., mtumwi Petro anapereka chitsanzo choonetsa mmene mfundo zimagwirira ntchito. Anachita zimenezo m’njira imene inakhudza kwambiri mitima ya anthu. (Mac. 2:14-36) Atafotokoza Malemba atatu amene omverawo anati anali kuwakhulupirira, Petro anaonetsa mmene malembawo anagwirira ntchito pa zochitika zimene anadzionera okha. Anthuwo atamva zimenezo, anafuna kuchitapo kanthu pa zimene anamvazo. Kodi kaphunzitsidwe kanu kamakhudza anthu mofananamo? Kodi mumachita zoposa kungotchula mfundozo, ndi kuthandiza anthu kuzindikira chifukwa chake zinthu zili choncho? Kodi mumawalimbikitsa kuona mmene zinthu zimene amaphunzirazo ziyenera kukhudzira miyoyo yawo? Zoona, iwo sangafuule kuti, “Tidzachita chiyani?” muja linachitira khamu lija pa Pentekoste, koma ngati mwasonyeza bwino lomwe tanthauzo la malemba, adzalimbikitsidwa kuchitapo kanthu moyenerera.—Mac. 2:37.

      Poŵerenga Baibulo ndi ana anu, makolonu mumakhala ndi mwayi wabwino kwambiri wophunzitsa ana anu kulingalira mmene mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo zimagwirira ntchito. (Aef. 6:4) Mwachitsanzo, mungasankhe mavesi ochepa pandandanda yanu ya kuŵerenga Baibulo ya mlunguwo. Kambiranani matanthauzo ake, kenako funsani mafunso ngati aŵa: ‘Kodi lembali limatithandiza motani? Kodi mavesiŵa tingawagwiritse ntchito motani mu ulaliki? Kodi amasonyezanji za Yehova ndi njira yake yochitira zinthu? Ndipo amakulitsa motani chiyamikiro chathu kwa iye?’ Limbikitsani banja lanu kuti likafotokoze mfundozo pokakambirana mfundo zazikulu za m’Baibulo pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Mwachidziŵikire, iwo adzalankhula pa mavesi omwe adzawakumbukira.

      Khalani Chitsanzo Chabwino

      Kuphunzitsa si zimene mumanena zokha, komanso zimene mumachita. Zochita zanu zimapereka chitsanzo chenicheni cha kugwiritsa ntchito zimene mumanena. Umu ndi mmene ana amaphunzirira. Akamatsanzira makolo awo, umenewo ndi umboni wakuti akufuna kukhala ngati makolo awo. Akufuna kudziŵa mmene kumamvekera kuchita zimene makolo amachita. Mofananamo, amene mumaphunzitsa ‘akamakutsanzirani mmene inunso mumatsanzirira Kristu,’ amayamba kupeza madalitso omwe amadza poyenda m’njira za Yehova. (1 Akor. 11:1) Amayamba kuona dzanja la Mulungu m’miyoyo yawo.

      Zimenezi ziyenera kumatikumbutsa kuti kupereka chitsanzo choyenera n’kofunika kwambiri. Mtundu wa anthu amene tikukhala ‘m’mayendedwe opatulika ndi m’kupembedza’ kwathu udzapereka chitsanzo kwa anthu amene timawaphunzitsa mmene angagwiritsire ntchito mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo. (2 Pet. 3:11) Ngati mulimbikitsa wophunzira Baibulo kuti aziŵerenga Mawu a Mulungu nthaŵi zonse, muyambe ndinu kukhala ndi khama lowaŵerenga. Ngati mukufuna kuti ana anu aphunzire kutsatira mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo, onetsetsani kuti aziona kuti zochita zanu zikugwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Ngati mulimbikitsa mpingo kuti uzikangalika mu ulaliki, onetsetsani kuti inuyo mumadzipereka ndi mtima wonse m’ntchito imeneyo. Ngati muchita zimene mumaphunzitsa, zimamveka mukamalimbikitsa ena.—Aroma 2:21-23.

      Pofuna kukulitsa luso lanu la kuphunzitsa, dzifunseni kuti: ‘Pamene ndikuphunzitsa, kodi omverawo amaona kuti n’zothandizadi pa maganizo awo, malankhulidwe, kapena khalidwe lawo? Pofuna kumveketsa zinthu, kodi ndimaonetsa kusiyana kwa lingaliro lina ndi linzake, kapena kachitidwe kena ndi kanzake? Kodi ndimatani pofuna kuthandiza ophunzira anga, ana anga, kapena omvera anga pamsonkhano kuti azikumbukira zimene ndimanena? Kodi ndimasonyeza omvera anga bwino lomwe mmene angagwiritsire ntchito zimene akuphunzira? Kodi amatha kuona zimenezo mwa ine? Kodi amazindikira mmene kulabadira kwawo nkhani imene ikukambidwayo kungakhudzire ubale wawo ndi Yehova?’ (Miy. 9:10) Pitirizani kusamalira mbali zimenezi pamene mukuyesetsa kukulitsa luso la kuphunzitsa. ‘Mudzipenyerere nokha, ndi chiphunzitsocho. Muzikhala mu izi; pakuti pochita ichi mudzadzipulumutsa inu nokha ndi iwo akumva inu.’—1 Tim. 4:16.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena