-
Kutsindika Malemba MoyenereraPindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
-
-
PHUNZIRO 21
Kutsindika Malemba Moyenerera
PAMENE muuza ena zolinga za Mulungu, kaya panokha kapena papulatifomu, zimene mukunena zizikike m’Mawu a Mulungu. Zimenezi zimatanthauza kuŵerenga malemba m’Baibulo, kuwaŵerenga bwino.
Kutsindika Koyenerera Kumaphatikizapo Mmene Mukumvera. Malemba aziŵerengedwa ndi mzimu wake wa nkhaniyo. Talingalirani zitsanzo zotsatirazi. Pamene muŵerenga Salmo 37:11, mawu anu ayenera kusonyeza chisangalalo choyembekezera mtendere wolonjezedwa pamenepo. Poŵerenga Chivumbulutso 21:4 za kutha kwa mavuto ndi imfa, mawu anu asonyeze kuyamikira mpumulo wodabwitsa wonenedweratuwo. Mawu a pa Chivumbulutso 18:2, 4, 5, ochonderera anthu kuti atuluke mu “Babulo Wamkulu” wodzaza ndi machimo, tiwaŵerenge ndi mzimu wosonyeza kufunika kochitapo kanthu msangamsanga. Inde, kukhudzika mtima kosonyezedwako kuzichokeradi mumtima, koma kusakhale konyanyira. Kukhudzika mtima koyenerera kumadalira mawuwo ndi mmene awagwiritsira ntchito.
Tsindikani Mawu Oyenerera. Ngati mfundo yanu palemba lina ikukhudza mbali imodzi yokha ya lembalo, tsindikani mbali yokhayo poŵerenga. Mwachitsanzo, ngati mukufuna kufotokoza tanthauzo la mawu akuti “muthange mwafuna Ufumu” pa Mateyu 6:33, poŵerenga simungatsindike kwambiri mawu akuti “chilungamo chake” kapena akuti “zonse zimenezo.”
M’nkhani ya pa Msonkhano wa Utumiki, mungafune kuŵerenga Mateyu 28:19. Kodi mungatsindike mawu ati? Ngati mukufuna kulimbikitsa khama loyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba, tsindikani mawu akuti “phunzitsani anthu.” Koma ngati mukufuna kufotokoza udindo wa Mkristu wolalikira choonadi cha m’Baibulo kwa alendo m’dziko kapena pofuna kulimbikitsa ofalitsa ena kukatumikira kumalo osoŵa, mungatsindike mawu akuti “anthu a mitundu yonse.”
Kaŵirikaŵiri, timapereka lemba kuti liyankhe funso kapena kutsimikizira mfundo imene ena angatsutse. Ngati titsindika mofanana ganizo lililonse palemba, omvera sangathe kuona kuti likukhudzana motani ndi nkhaniyo. Mfundo yake ingakhale yoonekera bwino kwa inu koma osati kwa iwo.
Mwachitsanzo, poŵerenga Salmo 83:18 m’Baibulo lokhala ndi dzina la Mulungu, ngati mutsindika kwambiri mawu akuti “Wam’mwambamwamba,” mwininyumba angalephere kugwirapo mfundo yoonekeratu yakuti Mulungu ali ndi dzina lakelake. Tsindikani dzina lakuti “Yehova.” Komabe, pogwiritsa ntchito lemba lokhalokhalo kufotokoza ufumu wa Yehova, tsindikani kwambiri mawu akuti “Wam’mwambamwamba.” Mofananamo, poŵerenga Yakobo 2:24 kusonyeza kuti chikhulupiriro chiyenera kukhala ndi ntchito, ngati mutsindika kwambiri mawu akuti “ayesedwa wolungama” m’malo mwa “ntchito,” ena okumverani angaphonye mfundo yake.
Chitsanzo china chothandiza chili pa Aroma 15:7-13. Imeneyi ndi mbali ya kalata imene mtumwi Paulo analembera mpingo wokhala ndi Akristu osakhala Ayuda ndi Akristu achiyuda. Pamenepa mtumwi Paulo akufotokoza mfundo yakuti utumiki wa Kristu supindulitsa Ayuda odulidwa okha komanso anthu a mitundu kotero kuti “anthu a mitundu ina akalemekeze Mulungu, chifukwa cha chifundo” chake. Ndiyeno, Paulo akugwira mawu malemba anayi posonyeza mwayi wotsegukira amitunduwo. Kodi mawu ogwidwawo mungawaŵerenge motani kuti mutsindike mfundo imene Paulo anali nayo m’maganizo? Ngati mufuna kuchonga mawu oyenera kuwatsindika, mungachonge mawu akuti “anthu a mitundu ina” pavesi 9, “amitundu inu” pavesi 10, “a mitundu yonse” ndi “anthu onse” pavesi 11, ndi “anthu amitundu” pavesi 12. Ndi kutsindika koteroko, yesani kuŵerenga Aroma 15:7-13. Mmene mukutero, mudzatha kumveketsa bwino lomwe kalingaliridwe ka Paulo pamfundo zake.
Njira Zotsindikira. Mawu opereka ganizo limene mukufuna kuunika akhoza kutsindikidwa m’njira zingapo. Njira imene muigwiritse ntchito ikhale yogwirizana ndi lembalo komanso nkhani yake. Nazi njira zingapo.
Kutsindika ndi liwu. Izi zimachitika mwa kusintha kamvekedwe ka liwu kumene kumachititsa mawu opereka ganizo lofunikira kuonekera kwambiri m’sentensi. Kutsindikako kumachitika mwa kusintha liwu—kulikweza kapena kulitsitsa. M’zinenero zambiri, amatsindika mawu mwa kukweza kapena kutsitsa liwu. Koma m’zinenero zina, kuchita zimenezo kungasinthiretu tanthauzo la mawu. Nthaŵi zina timalankhula pang’onopang’ono pofuna kumveketsa bwino mawu ofunikira. Kuteroko kumawonjezera ulemerero wa mawuwo. M’zinenero zosatsindika ganizo mwa kukweza kapena kutsitsa liwu pofuna kugogomeza mawu ofunika, m’pofunika kugwiritsa ntchito njira zina za chinenerocho kuti mumveketse mfundo zofunikira.
Kupuma. Mungapume musanaŵerenge kapena mutaŵerenga mbali yofunikira ya lemba—kapena ponse paŵiri. Kupuma musanaŵerenge ganizo lalikulu kumadzutsa chidwi; kupuma pambuyo pake kumakhomereza ganizolo. Koma ngati mupuma pafupipafupi kwambiri, palibe chimaoneka chapadera.
Kubwereza mawu. Mutha kutsindikanso mwa kudzidula ndi kuŵerenganso mawuwo. Koma njira imene ambiri amagwiritsa ntchito ndiyo ya kumaliza lemba lonse kenako n’kutchulanso mawu ofunikirawo.
Manja ndi nkhope. Kachitidwe ka manja ndi nkhope ndi thupi lonse kaŵirikaŵiri kamawonjezera mzimu wa mawu.
Kamvekedwe ka liwu. M’zinenero zina, mawu angaŵerengedwe ndi liwu logwirizana ndi tanthauzo lake. Apanso m’pofunika kusamala, makamaka kupeŵa kulankhula mozaza.
Pamene Ena Aŵerenga Malemba. Pamene mwininyumba aŵerenga lemba, angatsindike mawu olakwika kapena sangatsindike alionse. Kodi mungatani pamenepo? Mungamveketse tanthauzo la lembalo mwa kufotokoza cholinga chake. Mutatero, mungaunike mwachindunji mawu opereka ganizo lofunikawo m’Baibulo.
-
-
Kugwiritsa Ntchito Malemba MoyenereraPindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
-
-
PHUNZIRO 22
Kugwiritsa Ntchito Malemba Moyenerera
POPHUNZITSA ena, sikokwanira kungoŵerenga malemba m’Baibulo. Mtumwi Paulo polembera mnzake Timoteo anati: ‘Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.’—2 Tim. 2:15.
Kuti tichite zimenezo tiyenera kutanthauzira malemba mogwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Tiyenera kumvetsa nkhani yonse, osati kungosankha mawu otisangalatsa ndiyeno n’kuwagwirizanitsa ndi malingaliro athuathu. Kudzera mwa mneneri Yeremiya, Yehova anachenjeza za aneneri omwe anali kunamiza anthu kuti anali kunenera za m’kamwa mwa Yehova koma ‘ananena masomphenya m’mitima yawo.’ (Yer. 23:16) Mtumwi Paulo anachenjezanso Akristu za kuipitsa Mawu a Mulungu ndi nzeru zaumunthu pamene analemba kuti: “Takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nawo mawu a Mulungu konyenga.” M’masiku amenewo amalonda achinyengo omwe anali kugulitsa vinyo anali kuthira madzi m’vinyo kuti achuluke ndi cholinga choti apezepo ndalama zambiri. Ife sitichita nawo monyenga Mawu a Mulungu mwa kuwasakaniza ndi nzeru zaumunthu. “Sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nawo mawu a Mulungu,” anatero Paulo, “koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Kristu.”—2 Akor. 2:17; 4:2.
Nthaŵi zina, mungagwire mawu lemba pofuna kuunika mfundo ya makhalidwe abwino. Baibulo lili ndi mfundo za makhalidwe abwino zambiri zothandiza pamakhalidwe ambiri osiyanasiyana. (2 Tim. 3:16, 17) Koma tsimikizani kuti mukugwiritsa ntchito lembalo molondola, osati kulikhotetsa kuti lioneke ngati likunena zimene inuyo mukufuna kuti linene. (Sal. 91:11, 12; Mat. 4:5, 6) Gwiritsani ntchito lemba malinga ndi cholinga cha Yehova, mogwirizana ndi Mawu a Mulungu onsewo.
‘Kulunjika nawo mawu a choonadi’ kumaphatikizaponso kuzindikira mzimu wa zimene Baibulo likunena. Mawu a Mulungu si “chibonga” choopsezera ena. Aphunzitsi achipembedzo amene anatsutsa Yesu Kristu anagwira mawu Malemba, koma sanayang’ane pankhani zenizeni zofunika—zokhudza chilungamo ndi chifundo ndi kukhulupirika—zimene Mulungu amafuna. (Mat. 22:23, 24; 23:23, 24) Pophunzitsa Mawu a Mulungu, Yesu anaonetsa mtima wa Atate wake. Kukangalika kwa Yesu pa choonadi kunatsagana ndi chikondi chake chozama chimene anali nacho pa anthu amene anali kuwaphunzitsa. Tiyeni tiyesetse kutengera chitsanzo chake.—Mat. 11:28.
Nanga tingatsimikize bwanji kuti tikugwiritsa ntchito malemba moyenerera? Kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse kungatithandize. Tiyeneranso kuyamikira mphatso ya Yehova ya “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” limene ndi bungwe la Akristu odzozedwa ndi mzimu. Yehova amagwiritsa ntchito bungwe limeneli kugaŵira chakudya chauzimu kwa a m’banja la chikhulupiriro. (Mat. 24:45) Phunziro laumwini, kufika pamisonkhano nthaŵi zonse ndi kutengamo mbali kudzatithandiza kupindula ndi malangizo operekedwa kudzera m’gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.
Ngati buku la Kukambitsirana za m’Malemba lilipo m’chinenero chanu ndipo ngati mungaphunzire kuligwiritsira bwino ntchito, lidzakuthandizani kugwiritsa ntchito moyenerera malemba ambirimbiri omwe timagwiritsa ntchito kaŵirikaŵiri mu utumiki wathu wa kumunda. Ngati mukufuna kugwiritsa ntchito lemba losazoloŵereka, kudzichepetsa kudzakupangitsani kufufuza kotero kuti pokalankhula, muzikalunjika nawo mawu a choonadi.—Miy. 11:2.
Gwiritsani Ntchito Malemba Momveka Bwino. Pophunzitsa ena, onetsetsani kuti akuona bwino lomwe mgwirizano womwe ulipo pakati pa nkhani imene mukufotokozayo ndi malemba amene mukuŵerenga. Ngati mutsogoza funso potchula lemba, omvera anu aone mmene lembalo liyankhire funsolo. Ngati cholinga choŵerengera lemba ndi kupereka umboni pa mfundo inayake, onetsetsani kuti wophunzirayo akuona bwino lomwe mmene lembalo likutsimikizira mfundoyo.
Kungoŵerenga lemba—ngakhale motsindika—kaŵirikaŵiri kumakhala kosakwanira. Kumbukirani kuti anthu ambiri salidziŵa bwino Baibulo moti sangamvetse mfundo yanu ngati mungoŵerenga lemba basi. Unikani mawu a lembalo okhudza mwachindunji nkhani imene mukukambirana.
Zimenezi zimafuna kuti mumveketse mawu ofunikira kwambiri, aja okhudza mwachindunji mfundo imene mukukambirana. Njira yosavuta yochitira zimenezo ndiyo kubwerezanso mawu opereka malingaliro ofunikawo. Ngati mukukambirana ndi munthu mmodzi, mungafunse mafunso omwe angam’thandize kuona mawu ofunikawo. Polankhula ku gulu la anthu, okamba nkhani ena amachita zimenezo mwa kugwiritsa ntchito mawu ofanana matanthauzo kapena mwa kubwerezanso mfundo. Komabe, mukasankha kuchita zimenezo, samalani kuti omverawo asataye mgwirizano wa pakati pa mfundo yanu ndi mawu a lembalo.
Popeza mwaunika mawu ofunika kwambiri, pamenepo mwayala maziko ofunikira. Tsopano pitirizani. Kodi potchula lembalo mwasonyeza bwino lomwe cholinga choliŵerengera? Ngati mwatero, sonyezani mmene mawu omwe mwaunikawo akusonyezera cholingacho. Sonyezani momveka bwino mgwirizano wa mawuwo ndi cholingacho. Ngakhale kuti simunachite kutchula cholingacho popereka lembalo, muyenera kuchitchulabe potsirizira pake.
Afarisi anafunsa Yesu funso limene m’maganizo mwawo analiona kukhala lovuta kwambiri. Iwo anati: “Kodi n’kuloledwa kuti munthu achotse mkazi wake pa chifukwa chilichonse?” Yesu anayankha kuchokera pa Genesis 2:24. Onani kuti iye anangounika mbali imodzi yokha ya lembalo, kenako anapereka tanthauzo lofunikira. Atasonyeza kuti mwamuna ndi mkazi anakhala “thupi limodzi,” Yesu anati: “Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Mat. 19:3-6.
Kodi muyenera kufotokoza zochuluka motani pofuna kumveketsa tanthauzo la lemba? Zimadalira mtundu wa omvera anu ndi kufunika kwa mfundo imene mukuifotokoza. Koma cholinga chanu nthaŵi zonse chizikhala kufeŵetsa zinthu ndi kulunjika pamfundo.
Lingalirani Nawo Kuchokera M’malemba. Kunena za utumiki wa mtumwi Paulo ku Tesalonika, Machitidwe 17:2, 3 amatiuza kuti iye ‘ananena za m’malembo.’ Mtumiki wa Yehova aliyense ayenera kuyesetsa kukhala ndi luso lolingalira kuchokera m’malemba. Mwachitsanzo, Paulo anafotokoza mfundo zokhudza moyo wa Yesu ndi utumiki wake, anasonyeza kuti Malemba Achihebri ananeneratu zimenezi, ndiyeno anaphera mphongo ndi ndemanga yakuti: “Amene ndikulalikirani inu, ndiye Kristu.”
Pamene Paulo anali kulembera Ahebri, mobwerezabwereza anagwira mawu m’Malemba Achihebri. Pofuna kutsindika kapena kumveketsa mfundo, kaŵirikaŵiri anaunika liwu limodzi kapena mawu angapo kenako n’kufotokoza tanthauzo lake. (Aheb. 12:26, 27) M’nkhani yopezeka pa Ahebri chaputala 3, Paulo anagwira mawu Salmo 95:7-11. Onani kuti anaunika mbali zitatu za lembalo: (1) mtima wotchulidwawo (Aheb. 3:8-12), (2) tanthauzo la mawu akuti “Lero” (Aheb. 3:7, 13-15; 4:6-11), ndipo (3) tanthauzo la mawu akuti: “Ngati adzaloŵa mpumulo wanga” (Aheb. 3:11, 18, 19; 4:1-11). Yesetsani kutengera chitsanzo chimenecho pamene mugwiritsa ntchito lemba lililonse.
Onani mmene Yesu analingalirira mwaluso kuchokera m’Malemba pokambirana ndi munthu wina m’nkhani yopezeka pa Luka 10:25-37. Mwamuna wodziŵa Chilamuloyo anafunsa kuti: “Mphunzitsi, ndidzaloŵa moyo wosatha ndi kuchita chiyani?” Yesu poyankha, choyamba anafunsa mwamunayo kuti anene maganizo ake pankhaniyo, kenako Yesu anatsindika kufunika kochita zimene Mawu a Mulungu anena. Yesu ataona kuti mwamunayo sanamve mfundo yake, anatenga kanthaŵi ndithu kuti afotokoze mofatsa liwu limodzi lokha pa lembalo—liwu lakuti “mnansi.” M’malo mongomasulira liwulo, anagwiritsa ntchito fanizo pofuna kuthandiza mwamunayo kuzindikira yekha mfundoyo.
N’zoonekeratu kuti Yesu pofuna kuyankha mafunso, sanangogwira mawu malemba opereka yankho lachindunji ndi lodziŵikiratu. Anasanthula zimene malembawo anali kunena ndiyeno anawagwiritsa ntchito poyankha funso loperekedwa.
Pamene Asaduki anatsutsa za chiyembekezo cha kuuka kwa akufa, Yesu anatchula mbali imodzi yokha ya Eksodo 3:6. Koma iye sanangogwira mawuwo ndi kusiyira pomwepo. Analingalira nawo lembalo pofuna kusonyeza momvekera bwino kuti kuukitsa akufa ndi mbali ya cholinga cha Mulungu.—Marko 12:24-27.
Kupeza luso lolingalira moyenera ndi mwaluso kuchokera m’Malemba kudzakuthandizani kwambiri kukhala mphunzitsi waluso.
-
-
Kumveketsa Phindu la Nkhani YanuPindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
-
-
PHUNZIRO 23
Kumveketsa Phindu la Nkhani Yanu
KAYA mukulankhula kwa munthu mmodzi kapena kwa anthu ambiri, musaganize kuti anthuwo akhala ndi chidwi pankhani yanu kokha chifukwa inuyo muli nayo chidwi. Inde uthenga wanu ndi wofunika, koma ngati simumveketsa bwino phindu lake, chidwi cha omvera chingazilale.
Zimakhaladi choncho ngakhale kwa omvera mu Nyumba ya Ufumu. Iwo angatchere khutu pamene mugwiritsa ntchito fanizo kapena chochitika chimene sanamvepo. Koma angasiye kumvetsera mukayamba kulankhula nkhani imene akuidziŵa kale, makamaka mukalephera kufotokoza m’njira yatsopano mfundo zimene akuzidziŵa kale pankhaniyo. Athandizeni kuona chifukwa chake zimene mukunenazo zili zothandiza ndi kuwafotokozera phindu lake.
Baibulo limatilimbikitsa kulingalira zinthu zopindulitsa. (Miy. 3:21) Yehova anagwiritsa ntchito Yohane Mbatizi kuonetsa anthu “nzeru ya olungama mtima.” (Luka 1:17) Imeneyi ndi nzeru yochokera m’mantha akulemekeza Yehova. (Sal. 111:10) Awo amene amazindikira nzeru imeneyi amakhoza kuthana ndi zovuta za moyo uno ndi kugwira zolimba moyo weniweni, moyo wosatha ukudzawo.—1 Tim. 4:8; 6:19.
Kupangitsa Nkhani Kukhala ya Phindu. Kuti nkhani yanu ikhale yopindulitsa, lingalirani mosamala mfundo zanu, komanso omvera anu. Musawaone ngati gulu chabe la anthu. Onani kuti mwa omverawo muli anthu osiyanasiyana komanso mabanja. Mungakhalenso ana achichepere, achinyamata, achikulire, ndi ena okalamba. Mungakhalenso okondwerera atsopano komanso aja amene anayamba kutumikira Yehova inuyo musanabadwe. Ena angakhale okhwima mwauzimu; ena angakhalebe ndi maganizo ndi machitachita ena a dzikoli. Dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhani imene ndikakambeyi ikawapindulitsa motani omvera? Kodi ndingakawathandize motani kumvetsa mfundo yake yaikulu?’ Mwina mungaganize zolunjikitsa kwambiri nkhani yanu ku gulu limodzi kapena aŵiri mwa anthu omwe tatchulawo. Komabe, musaiwaliretu enawo.
Bwanji ngati mwapatsidwa nkhani yoti mufotokoze chimodzi cha ziphunzitso zazikulu za m’Baibulo? Kodi nkhani imeneyo mungaikambe motani kuti ipindulitse omvera amene amakhulupirira kale chiphunzitsocho? Yesetsani kulimbikitsa chikhulupiriro chawo. Motani? Mwa kufotokoza umboni wa m’Malemba wovomereza chiphunzitsocho. Mukhoza kuwathandizanso kuzamitsa chidziŵitso chawo pa chiphunzitso cha Baibulo chimenecho. Mungachite zimenezi mwa kusonyeza mmene chiphunzitsocho chimagwirizanira ndi mfundo zina za choonadi cha Baibulo komanso ndi mkhalidwe wa Yehova. Gwiritsani ntchito zitsanzo—zochitika zenizeni ngati n’kotheka—zosonyeza kuti kumvetsa chiphunzitso chimenechi kwathandizadi anthu, ndi mmene chimathandizira munthu kuyang’ana m’tsogolo ndi chidaliro.
Kuonetsa mmene mfundo zimagwirira ntchito musakufotokoze m’mawu omaliza okha a nkhani yanu. Kuchokera pachiyambi pa nkhani yanu, womvera aliyense ayenera kunena mumtima mwake kuti “izi zikundikhudza.” Pokhala mutayala maziko amenewo, pitirizani kusonyeza mmene mfundo yaikulu iliyonse m’nkhaniyo ikugwirira ntchito. Teroninso m’mawu omaliza.
Posonyeza mmene mfundo zikugwirira ntchito, samalani kuti muchite mogwirizana ndi mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo. Kutanthauza chiyani? Kutanthauza kuchita zimenezo m’njira yachikondi ndi yosonyeza chifundo. (1 Pet. 3:8; 1 Yoh. 4:8) Ngakhale pamene mtumwi Paulo anali kusamalira mavuto aakulu ku Tesalonika, anagogomeza kwambiri mbali zolimbikitsa abale ndi alongo ake achikristu kupita patsogolo mwauzimu. Anasonyezanso kuti anali ndi chidaliro chakuti iwo akakhala ofunitsitsa kuchita zoyenera m’nkhani imene anakambirana nawo. (1 Ates. 4:1-12) Chitsanzo chabwino kwambiri choti ifenso titengere!
Kodi cholinga cha nkhani yanu ndi kulimbikitsa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa ena uthenga wabwino? Pamenepo alimbikitseni kuti azikhala osangalala ndi oyamikira mwayi umenewo. Komabe, musaiwale kuti anthu angathe kugwira ntchito imeneyo pamlingo wosiyanasiyana; Baibulonso limavomereza zimenezo. (Mat. 13:23) Musachititse abale anu kukhala ndi maganizo odziimba mlandu. Pa Ahebri 10:24 timalimbikitsidwa kuti “tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino.” Ngati tifulumiza ena ku chikondano, adzatha kugwira ntchito ndi cholinga chabwino. Kusiyana ndi kuumirira kuti onse azichita zinthu mofanana, zindikirani kuti chimene Yehova amafuna n’chakuti ife tilimbikitse ‘kumvera mwa chikhulupiriro.’ (Aroma 16:26) Pokumbukira zimenezi, tidzayesetsa kulimbikitsa chikhulupiriro chathu ndi cha abale athu.
Kuthandiza Ena Kuona Phindu la Nkhani Yanu. Pamene mulalikira kwa ena, musalephere kumveketsa phindu lenileni la uthenga wabwino. Kuti mukathe kuchita zimenezo muyenera kulingalira zimene zili m’maganizo mwa anthu a m’gawo lanu. Kodi mungadziŵe bwanji? Mverani nkhani pawailesi ya mawu kapena ya kanema. Yang’anani nkhani zosonyezedwa patsamba loyamba la nyuzipepala. Ndiponso, yesetsani kukambirana ndi anthu, ndipo mvetserani pamene akulankhula. Mungapeze kuti iwo akulimbana ndi mavuto akutiakuti, monga kuchotsedwa ntchito, kusoŵa ndalama zalendi, matenda, imfa ya wina m’banja, kuopa zigawenga, kuchitidwa mopanda chilungamo ndi wina waudindo, kutha kwa ukwati, kupulupudza kwa ana, ndi zina zotero. Kodi Baibulo lingawathandize? Ndithudi lingawathandize.
Poyamba kukambirana, mwachidziŵikire mudzakhala ndi nkhani inayake m’maganizo mwanu. Komabe, ngati munthuyo aonetsa kuti ali ndi nkhani ina yofuna kukambirana msanga, kambiranani imeneyo ngati mungathe kutero. Apo ayi pemphani kuti mukabwere ndi mfundo zothandiza. N’zoona kuti timakana ‘kuloŵerera nkhani zosatikhudza,’ komabe timakonda kugaŵana ndi ena uphungu wothandiza wochokera m’Baibulo. (2 Ates. 3:11, NW) Inde, uphungu umene anthu angakonde kwambiri kuumva ndi uphungu wa m’Baibulo umene umakhudza miyoyo yawo.
Anthu akapanda kuona mmene uthenga wathu ukuwakhudzira, nthaŵi zina amangothetsa kukambiranako. Ngakhale atatilola kulankhula, ngati tilephera kusonyeza phindu lenileni la nkhani yathu, uthenga wathuwo sungakhudze miyoyo yawo kwenikweni. Koma ngati timveketsa bwino lomwe phindu la uthengawo, kukambiranako kungakhale chiyambi cha kusintha kwa moyo wa munthuyo.
Pochititsa maphunziro a Baibulo, pitirizani kuunika phindu lenileni la phunzirolo. (Miy. 4:7) Athandizeni ophunzira kuti amvetse uphungu wa m’Malemba, mfundo za makhalidwe abwino, ndi zitsanzo zowasonyeza mmene angayendere m’njira za Yehova. Tsindikani mapindu amene amakhalapo pochita motero. (Yes. 48:17, 18) Zimenezo zidzalimbikitsa ophunzirawo kusintha mbali zofunikira kusintha m’miyoyo yawo. Mangani mwa iwo chikondi cha pa Yehova ndi chikhumbo chofuna kum’kondweretsa. Ndipo athandizeni kukhala ndi mtima wofunitsitsa kugwiritsa ntchito uphungu wochokera m’Mawu a Mulungu.
-