Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gl tsamba 8-9
  • Kuchoka ku Igupto Kupita ku Dziko Lolonjezedwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchoka ku Igupto Kupita ku Dziko Lolonjezedwa
  • ‘Onani Dziko Lokoma’
  • Nkhani Yofanana
  • B3 Ulendo Wochoka ku Iguputo
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • Aisrayeli ndi Mitundu Yowazungulira
    ‘Onani Dziko Lokoma’
  • Girisi ndi Roma Akhudza Moyo wa Ayuda
    ‘Onani Dziko Lokoma’
  • Chikristu Chifalikira Kumayiko Ena
    ‘Onani Dziko Lokoma’
Onani Zambiri
‘Onani Dziko Lokoma’
gl tsamba 8-9

Kuchoka ku Igupto Kupita ku Dziko Lolonjezedwa

ANTHU kulikonse amadziŵa za ulendo wa Aisrayeli wochoka ku Igupto. Koma kodi Mose ndi anthu a Mulungu anakumana ndi zotani atawoloka Nyanja Yofiira? Kodi analoŵera kuti, ndipo anakafika bwanji pa Mtsinje wa Yordano kuti aloŵe m’Dziko Lolonjezedwa?

M’mene Aisraeli Anayendera

Ulendo wawo unali wa ku Kanani, koma Mose sanatsate njira yaifupi kwambiri, ya makilomita pafupifupi 400 yodutsa kugombe lamchenga, yomwe ikanawadutsitsa m’Filistiya mwenimweni, m’dziko la adani. Komanso iye sanaloŵere pakati pa dera lalikulu la Sinai, komwe nsangalabwi ndi mapiri ake a miyala ya njereza n’zotentha kwambiri. M’malo mwake, Mose analoŵera nawo kum’mwera anthuwo, n’kudutsa nawo mu mkwasa wa kuchigwa kugombe la nyanja. Anamanga msasa woyamba ku Mara, pamene Yehova anasandutsa madzi owawa kukhala okoma.a Atachoka ku Elimu, anthuwo anadandaula pofuna chakudya; Yehova n’kutumiza zinziri ndipo kenako anatumiza mana. Ku Refidimu, nkhani ya madzi inavutanso, Aamaleki omwe anaputa Aisrayeli anagonjetsedwa, ndipo mpongozi wa Mose analangiza Mose kuti amuna anzeru azimuthandiza ntchito.—Eks., machap. 15-18.

Mose kenako anatsogolera Israyeli kumapiri a kum’mwera kwenikweni, n’kukamanga msasa ku Phiri la Sinai. Kumeneko, anthu a Mulungu analandira Chilamulo, anakonza chihema, komanso anapereka nsembe. Chaka chachiŵiri cha ulendowu, iwo anapita kumpoto podzera ‘m’chipululu chachikulu ndi choopsa,’ ulendo wopita kudera la Kadesi (Kadesi Barinea) womwe mwachionekere unatenga masiku 11. (Deut. 1:1, 2, 19; 8:15) Chifukwa chochita mantha ndi nkhani yolakwika imene azondi khumi anabweretsa, anthuwo anayamba kumangoyendayenda zaka 38. (Num. 13:1–14:34) Ena mwa malo omwe anaimako ndi monga ku Abirona ndi ku Ezioni Geberi, kenako anabwerera ku Kadesi.—Num. 33:33-36.

Nthaŵi itakwana tsopano yoti Israyeli apite ku Dziko Lolonjezedwa, Aisrayeliwo sanapite mwachindunji kumpoto. M’malo mwake anazungulira dziko la Edomu n’kuloŵera kumpoto motsata “msewu wachifumu.” (Num. 21:22; Deut. 2:1-8) Kwa mtundu wonsewo, womwe unkayenda ndi ana, ziŵeto, mahema, sunali ulendo wamaseŵera kuyenda mu msewu umenewu. Anadutsa njira yokhotakhota kutsika ndi kukwera zigwembe zoipa kwambiri, m’zigwa monga Zaredi ndi Arinoni (zakuya pafupifupi mamita 520).—Deut. 2:13, 14, 24.

Kenako Aisrayeli anafika pa Phiri la Nebo. Miriamu anali atamwalira ku Kadesi, ndipo Aroni anamwalira pa Phiri la Hori. Koma Mose anamwalirira pamenepa pafupi penipeni ndi dziko lomwe ankalakalaka ataloŵamo. (Deut. 32:48-52; 34:1-5) Yoswa ndiye anapatsidwa udindo wotsogolera Israyeli kuloŵa m’dzikolo, kutsiriza ulendo womwe unayambika zaka 40 m’mbuyomo.—Yos. 1:1-4.

[Mawu a M’munsi]

a Malo ambiri amene anamangapo misasa sakudziŵika bwinobwino kuti anali pati.

[Bokosi patsamba 8]

MABUKU A M’BAIBULO OLEMBEDWA NTHAŴIYI:

Genesis

Eksodo

Levitiko

Numeri

Deuteronomo

Yobu

Masalmo (mbali yake ina)

[Mapu patsamba 9]

(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)

Njira Imene Israyeli Anadutsa yotchulidwa m’buku la Ekisodo

Njira Imene Israyeli Anadutsa

A7 IGUPTO

A5 Ramese?

B5 Sukoti?

C5 Etamu?

C5 Pihahiroti

D6 Mara

D6 Elimu

E6 CHIPULULU CHA SINI

E7 Dofika

F8 Refidimu

F8 Phiri la Sinai (Horebe)

F8 CHIPULULU CHA SINAI

F7 Kibiroti Hatava

G7 Hazeroti

G6 Rimon Perezi

G5 Risa

G3 Kadesi

G3 Bene Yaakana

G5 Hori Hagidigadi

H5 Yotibata

H5 Abirona

H6 Ezioni Geberi

G3 Kadesi

G3 CHIPULULU CHA ZINI

H3 Phiri la Hori

H3 Tsalimona

I3 Punoni

I3 Iyebarimu

I2 MOABU

I1 Diboni

I1 Alimoni Diblataimu

H1 Yeriko

[Malo Ena]

A3 GOSENI

A4 Oni

A5 Mofi (Nofi)

B3 Zoani

B3 Tapanesi

C5 Migidoli

D3 SURI

D5 CHIPULULU CHA ETAMU

F5 CHIPULULU CHA PARANA

G1 FILISTIYA

G1 Asidodo

G2 Gaza

G2 Beereseba

G3 Azimoni

G3 NEGEBU

H1 Yerusalemu

H1 Hebroni (Kiriyati Araba)

H2 Aradi (Mkanani)

H4 SEIRI

H4 EDOMU

I7 MIDYANI

Njira Zazikulu

Njira ya Dziko la Afilisti

Njira ya ku Suri

I4 Msewu Wachifumu

Njira ya Apaulendo

Njira ya El Haj

[Mapiri]

F8 Phiri la Sinai (Horebe)

H3 Phiri la Hori

I1 Phiri la Nebo

[Nyanja]

E2 Mediterranean (Nyanja Yaikulu)

D7/G7 Nyanja Yofiira

I1 Nyanja Yamchere

[Mitsinje]

A6 Mtsinje wa Nile

F3 C. cha Igupto

I2 Arinoni

I3 Zaredi

[Chithunzi patsamba 8]

Apaulendo ankadutsa m’kati mwa dera la Sinai

[Chithunzi patsamba 8]

AIsrayeli anamanga msasa pafupi ndi Phiri la Sinai

[Chithunzi patsamba 9]

Anapeza madzi pa akasupe ku Kadesi kapena m’madera a kufupi

[Chithunzi patsamba 9]

Aisrayeli onse anawoloka chigwa cha Arinoni

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena