-
Kodi Kudzipha Ndi Njira Yabwino Yothetsera Mavuto?Galamukani!—2014 | April
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO
Kodi Kudzipha Ndi Njira Yabwino Yothetsera Mavuto?
DIANAa amaoneka kuti ndi mtsikana wanzeru, wansangala komanso wokonda kucheza ndi anthu. Koma ngakhale amaoneka chonchi, ali ndi mavuto aakulu amene amam’chititsa kuti nthawi zambiri azivutika maganizo. Iye anati: “Tsiku silidutsa ndisanaganize zoti kuli bwino nditangofa. Ndimaona kuti ngakhale nditamwalira, palibe amene angandisowe chifukwa ndine wosafunika.”
Nyuzipepala ina ya ku Canada inanena kuti: “Kafukufuku wina anasonyeza kuti pa anthu 200 amene amafuna kudzipha, mmodzi amadziphadi ndipo pa anthu 400 amene amaganiza zoti adzadzipha, m’modzi amadzadziphadi.”—THE GAZETTE, MONTREAL, CANADA.
Diana amanena kuti sangayerekeze n’komwe kudzipha. Komabe, nthawi zina amaona kuti palibe chifukwa chokhalira ndi moyo. Iye ananena kuti: “Ndimalakalaka patachitika ngozi inayake ine n’kufa. Kwa ine imfa si mdani, ndipo sindiiopa.”
Anthu ambiri amaganiza zofanana ndi zimene Diana amaganizazi, ndipo ena amaganiza zodzipha pamene ena anayesapo kudzipha. Koma akatswiri amanena kuti anthu ambiri amene amafuna kudzipha sikuti kwenikweni amafunadi kufa, koma amangoona kuti kudzipha ndi njira imene angathetsere mavuto awo. Mwachidule tingati, anthu amenewa amaona kuti pali zifukwa zokwanira zoti kuli bwino angofa, choncho amafunika kuwatsimikira kuti palinso zifukwa zomveka zokhalira ndi moyo.
Kodi zifukwa zimenezi ndi ziti? Taonani mfundo zitatu zimene zatchulidwa m’nkhani yotsatirayi.
a Si dzina lake lenileni.
-
-
1 Zinthu Zimasintha pa MoyoGalamukani!—2014 | April
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI KUDZIPHA NDI NJIRA YABWINO YOTHETSERA MAVUTO?
1 Zinthu Zimasintha pa Moyo
“Timapanikizidwa mwamtundu uliwonse, koma osati kupsinjidwa moti n’kulephera kusuntha. Timathedwa nzeru, koma osati mochita kusoweratu pothawira.”—2 AKORINTO 4:8.
Kudzipha kuli ngati kuwotcha nyumba chifukwa choti m’nyumbamo muli makoswe, m’malo mongopha makoswewo. Ngakhale munthu atakumana ndi mavuto aakulu ooneka ngati sangathe, m’kupita kwa nthawi akhoza kutha. Ndipotu zinthu zikhoza kusintha n’kuyamba kuyenda bwino.—Onani bokosi lakuti “Zinthu Zinasintha pa Moyo Wawo.”
Ngakhale zitakhala kuti zinthu sizingasinthe pa moyo wanu, ndi bwino kumathana ndi mavuto amene mukukumana nawo panopa, m’malo momada nkhawa ndi mavuto amene angabwere m’tsogolo. Yesu ananena kuti: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.”—Mateyu 6:34.
Nanga kodi mungatani zitakhala kuti vuto lanu ndi loti silingathe? Mwachitsanzo, mwina muli ndi matenda okhalitsa. Kapenanso mukuvutika maganizo chifukwa cha zinthu zoti sizingasinthe, monga kutha kwa ukwati kapena imfa ya munthu amene munkamukonda?
Dziwani kuti ngakhale pa zochitika zoterezi, mungathebe kusintha zinazake. Mungasinthe mmene mukuonera nkhaniyo. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muyambe kuona zinthu moyenera. (Miyambo 15:15) Zingakuthandizeninso kuti mupirire vuto lanulo m’malo momaganiza zoti ndi bwino kungofa. Zotsatira zake zingakhale zoti ngakhale kuti simungathetse vutolo, mungayambe kuliona moyenera.—Yobu 2:10.
MFUNDO YOYENERA KUIKUMBUKIRA: Simungathe kukwera phiri mwa kungoyenda sitepe imodzi yokha, koma mutayenda masitepe ambirimbiri mungapezeke muli pamwamba pa phirilo. N’chimodzimodzinso ndi mavuto anu amene mwina mungamawaone kuti ndi aakulu ngati phiri. Muyenera kumathana nawo pang’onopang’ono.
ZIMENE MUYENERA KUCHITA PANOPA: Uzani mnzanu kapena wachibale za vuto lanulo. Munthu ameneyo angakuthandizeni kuti muyambe kuona vutolo moyenera.—Miyambo 11:14.
-
-
2 Pali Zimene ZingakuthandizeniGalamukani!—2014 | April
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI KUDZIPHA NDI NJIRA YABWINO YOTHETSERA MAVUTO?
2 Pali Zimene Zingakuthandizeni
‘Mutulireni [Mulungu] nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’—1 PETULO 5:7.
Anthu amene amaganiza kuti ndi bwino angofa, amaona kuti palibe chimene angachite kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino pa moyo wawo. Koma dziwani kuti zinthu zotsatirazi zingakuthandizeni kulimbana ndi vuto lanu.
Pemphero. Sikuti pemphero limangothandiza munthu kuti mtima wake ukhale m’malo komanso sikuti timafunika kupemphera pamene zinthu zatithina basi. Pemphero ndi njira yolankhulira ndi Yehova Mulungu, amene amakukondani kwambiri. Yehova amafuna kuti muzimuuza zimene zikukudetsani nkhawa. Ndipotu Baibulo limatiuza kuti: “Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza.”—Salimo 55:22.
Choncho mungachite bwino kupemphera kwa Mulungu panopa. Popemphera muzitchula dzina lake lakuti Yehova ndipo muzimuuza zimene zili mumtima mwanu. (Salimo 62:8) Yehova amafuna kuti muzimuona kuti ndi mnzanu wapamtima. (Yesaya 55:6; Yakobo 2:23) Pemphero ndi njira yolankhulira ndi Yehova yoti mungathe kuigwiritsa ntchito nthawi iliyonse komanso kulikonse komwe muli.
Mogwirizana ndi zotsatira za kafukufuku wina, “pa anthu 100 alionse amene amadzipha, anthu oposa 90 amakhala oti anali ndi matenda a kuvutika maganizo pa nthawi yomwe anadziphayo. Koma nthawi zambiri anthuwa amakhala oti sanalandire mankhwala a matendawa chifukwa choti sanazindikire kuti akudwala matendawa”
Anthu amene amakukondani. Achibale anu komanso anzanu amakukondani ndipo mwina anasonyeza kale kuti akufuna kuti zinthu ziyambe kukuyenderani bwino. Palinso anthu ena oti mwina simukuwadziwa amene amakufunirani zabwino. Mwachitsanzo, nthawi zina a Mboni za Yehova akamalalikira kunyumba ndi nyumba, amakumana ndi anthu omwe asowa mtengo wogwira chifukwa cha mavuto, ndipo mwina akuganiza zongodzipha. Ntchito yolalikira imene a Mboni za Yehova amagwirayi imachititsa kuti akumane ndi anthu oterewa, n’kuwathandiza. Iwo amatsanzira Yesu ndipo amakonda anthu. Choncho inunso amakukondani.—Yohane 13:35.
Madokotala odziwa za matendawa. Nthawi zambiri munthu amene amaganiza zodzipha, amakhala kuti wadwala matenda a kuvutika maganizo kwa nthawi yaitali. Koma dziwani kuti kuvutika maganizo n’chimodzimodzi ndi matenda ena onse, choncho palibe chifukwa chochitira manyazi ndi vutoli. Ndipotu ambiri amati matenda a kuvutika maganizo ndi ofala ngati chimfine. Choncho, aliyense angathe kudwala matenda a kuvutika maganizo. Koma ubwino wake, matendawa ali ndi mankhwala.a
MFUNDO YOYENERA KUIKUMBUKIRA: Ngati mukudwala matenda a kuvutika maganizo zimakhala ngati muli m’dzenje lakuya ndipo simungathe kutulukamo nokha. Koma anthu ena atakuthandizani, mungathe kuthetsa vuto lanulo.
ZIMENE MUYENERA KUCHITA PANOPA: Pitani kwa dokotala amene amadziwa za matenda a kuvutika maganizo.
a Ngati nthawi zambiri mumaganiza zodzipha, mungachite bwino kupita kuchipatala kukaonana ndi dokotala wodziwa za vutoli, kuti akuthandizeni.
-
-
3 Pali Chiyembekezo Choti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogoloGalamukani!—2014 | April
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI KUDZIPHA NDI NJIRA YABWINO YOTHETSERA MAVUTO?
3 Pali Chiyembekezo Choti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo
“Anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—SALIMO 37:11.
Baibulo limavomereza kuti moyo wa munthu ndi “waufupi, wodzaza ndi masautso.” (Yobu 14:1) Masiku ano aliyense amakumana ndi mavuto. Koma anthu ena alibe chiyembekezo chilichonse ndipo saganiza n’komwe zoti mavuto awowo angadzathe m’tsogolo. Ngati inunso mumaona choncho, dziwani kuti Baibulo limaphunzitsa kuti inuyo komanso anthu ena onse, mungathe kukhala ndi tsogolo labwino. Mwachitsanzo:
Baibulo limanena kuti Yehova Mulungu amafuna kuti anthufe tizisangalala.—Genesis 1:28.
Yehova Mulungu amatilonjeza kuti dziko lapansili lidzakhala paradaiso.—Yesaya 65:21-25.
N’zosakayikitsa kuti Mulungu adzakwaniritsa lonjezo limeneli. Lemba la Chivumbulutso 21:3, 4 limanena kuti:
“Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo. Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”
Zimenezi si nkhambakamwa chabe. Yehova Mulungu akufunitsitsa kudzakwaniritsa lonjezo limeneli ndipo ali ndi mphamvu yochitira zimenezi. Zimene Baibulo limanena zokhudza tsogolo la anthu zidzachitikadi. Choncho Baibulo limatithandizanso kudziwa kuti pali zifukwa zabwino zokhalirabe ndi moyo ngakhale mukukumana ndi mavuto.
MFUNDO YOYENERA KUIKUMBUKIRA: Ngakhale kuti mungaone kuti mavuto amene mukukumana nawo ndi ofanana ndi mafunde apanyanja, zimene Baibulo limaphunzitsa zokhudza tsogolo la anthu zili ngati nangula amene angakulimbitseni kwambiri.
ZIMENE MUYENERA KUCHITA PANOPA: Phunzirani Baibulo mozama kuti mudziwe zimene limaphunzitsa zokhudza zinthu zosangalatsa zimene zidzachitike m’tsogolo. A Mboni za Yehova angakuthandizeni kuchita zimenezi. Mungalankhule ndi a Mboni a m’dera lanu kapena mungapite pa webusaiti ya jw.org/ny.a
a Zimene mungachite: Pitani pa webusaiti ya jw.org/ny ndipo muyang’ane pamene palembedwa kuti, MABUKU > LAIBULALE YA PA INTANETI. Kenako fufuzani mawu akuti, “kuvutika maganizo” kapena “kudzipha” kuti mudziwe zambiri.
-