Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lff phunziro 33
  • Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?
  • Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • FUFUZANI MOZAMA
  • ZOMWE TAPHUNZIRA
  • ONANI ZINANSO
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
Onani Zambiri
Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
lff phunziro 33
Phunziro 33. Anthu ali m’Paradaiso padziko lapansi.

PHUNZIRO 33

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?

Losindikizidwa
Losindikizidwa
Losindikizidwa

Ufumu wa Mulungu unayamba kale kulamulira. Posachedwapa Ufumuwu ubweretsa madalitso ambiri padzikoli. Tiyeni tione ena mwa madalitso amene tidzasangalale nawo Ufumuwu ukadzayamba kulamulira dziko lonse lapansi.

1. Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita chiyani kuti ubweretse mtendere ndi chilungamo padzikoli?

Yesu yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzawononga anthu oipa ndi maboma onse a anthu pa nkhondo ya Aramagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Pa nthawi imeneyo, tidzaona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la m’Baibulo ili: “Kwatsala kanthawi kochepa, ndipo oipa sadzakhalaponso.” (Salimo 37:10) Yesu adzagwiritsa ntchito Ufumuwu pobweretsa mtendere komanso chilungamo padziko lonse lapansi.​—Werengani Yesaya 11:4.

2. Kodi moyo udzakhala wotani zimene Mulungu amafuna zikadzachitika padziko lapansi?

Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira dzikoli, “olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo mpaka kalekale.” (Salimo 37:29) Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kukhala m’dziko limene aliyense ndi wolungama ndipo amakonda Yehova komanso anthu ena. Palibe aliyense amene azidzadwala ndipo anthu onse adzakhala ndi moyo mpaka kalekale.

3. Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita zotani anthu oipa akadzawonongedwa?

Anthu oipa akadzawonongedwa, Yesu adzalamulira monga Mfumu kwa zaka 1,000. Pa nthawiyi, Yesu ndi olamulira anzake okwana 144,000, adzathandiza anthu onse padzikoli kuti akhale angwiro. Pofika kumapeto kwa zaka 1,000, dziko lonse lidzakhala paradaiso ndipo anthu azidzakhala mosangalala chifukwa chomvera malamulo a Yehova. Kenako Yesu adzabwezera Ufumu kwa Atate wake Yehova. Pa nthawi imeneyo, dzina la Yehova ‘lidzayeretsedwa’ kwambiri kuposa kale lonse. (Mateyu 6:9, 10) Aliyense adzadziwa kuti Yehova ndi Wolamulira wabwino kwambiri yemwe amaganizira atumiki ake. Kenako Yehova adzawononga Satana, ziwanda ndi anthu onse amene adzasonyeze kuti sakufuna kumvera ulamuliro wake. (Chivumbulutso 20:7-10) Zimenezi zikadzachitika, madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse padzikoli adzakhalapo mpaka kalekale.

FUFUZANI MOZAMA

Fufuzani kuti mudziwe chifukwa chake sitikayikira kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wake pokwaniritsa malonjezo onse amene ali m’Baibulo.

4. Ufumu wa Mulungu udzathetsa maboma onse a anthu

Baibulo limati: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.” (Mlaliki 8:9) Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu wake pothetsa zinthu zonse zopanda chilungamo zimene anthu amachitira anzawo.

Werengani Danieli 2:44 ndi 2 Atesalonika 1:6-8, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi Yehova komanso Mwana wake Yesu, adzachita chiyani ndi maboma a anthu komanso anthu amene amawatsatira?

  • Kodi zimene mwaphunzira zokhudza Yehova ndi Yesu zikukutsimikizirani bwanji kuti azidzachita zinthu mwachilungamo?

Yesu ndi Mfumu kumwamba ndipo akulamulira dziko lapansi.

5. Yesu ndi Mfumu yabwino kwambiri

Monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, Yesu adzachitira anthu zinthu zabwino kwambiri padzikoli. Onerani VIDIYO kuti muone umboni wosonyeza kuti Yesu ndi wofunitsitsa kuthandiza anthu komanso kuti Mulungu anamupatsa mphamvu zochitira zimenezo.

VIDIYO: Yesu Anasonyeza Zimene Ufumu wa Mulungu Udzachitire Anthu (1:13)

Zimene Yesu ankachita ali padzikoli, zinasonyeza zimene Ufumu wa Mulungu udzachitire anthu. Pa madalitso amene ali m’munsiwa, ndi madalitso ati amene inuyo mukuwayembekezera kwambiri? Werengani malemba amene akukuthandizani kumvetsa madalitso amenewa.

ALI PADZIKOLI, YESU . . .

ALI KUMWAMBA, YESU . . .

  • anathetsa chimphepo chamkuntho.​—Maliko 4:36-41.

  • adzakonza zinthu zonse zimene zawonongedwa padzikoli.​—Yesaya 35:1, 2.

  • anadyetsa anthu ambiri modabwitsa.​—Mateyu 14:17-21.

  • adzathetsa njala padziko lonse.​—Salimo 72:16.

  • anachiritsa anthu ambiri.​—Luka 18:35-43.

  • adzathetsa matenda onse.​—Yesaya 33:24.

  • anaukitsa anthu amene anamwalira.​—Luka 8:49-55.

  • adzathetsa imfa.​—Chivumbulutso 21:3, 4.

6. Ufumu wa Mulungu udzabweretsa madalitso ambiri

Ufumu wa Mulungu udzachititsa kuti anthu azikhala moyo wabwino ngati mmene Yehova ankafunira poyamba. Anthu adzakhala ndi moyo m’paradaiso padzikoli mpaka kalekale. Onerani VIDIYO kuti muone mmene Yehova akukwaniritsira cholinga chake pogwiritsa ntchito Mwana wake Yesu.

VIDIYO: Anatisonyeza Zimene Adzatichitire M’tsogolo (4:38)

Werengani Salimo 145:16, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi mumamva bwanji mukaganizira kuti Yehova ‘adzakwaniritsa zolakalaka za chamoyo chilichonse’?

ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Ngati titamachita zinthu mogwirizana, tikhoza kuthetsa mavuto apadziko lonse.”

  • Kodi Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto ati amene maboma a anthu alephera kuwathetsa?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Ufumu wa Mulungu udzakwaniritsa cholinga chimene Mulungu anali nacho poyamba. Udzasintha dzikoli kuti likhale paradaiso, ndipo mudzakhala anthu abwino omwe azidzalambira Yehova mpaka kalekale.

Kubwereza

  • Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita zotani kuti dzina la Yehova liyeretsedwe?

  • N’chifukwa chiyani timakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu udzakwaniritsa zonse zimene Baibulo linalonjeza?

  • Pa madalitso onse amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse, ndi dalitso liti limene inuyo mukuliyembekezera kwambiri?

Zoti Muchite

ONANI ZINANSO

Fufuzani kuti mudziwe zimene nkhondo ya Aramagedo imatanthauza.

“Kodi Nkhondo ya Aramagedo Idzakhala Yotani?” (Nkhani yapawebusaiti)

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zomwe zidzachitike pa nthawi imene Yesu anaitchula kuti “chisautso chachikulu.”​—Mateyu 24:21.

“Kodi Chisautso Chachikulu N’chiyani?” (Nkhani yapawebusaiti)

Onani zimene zingathandize mabanja kuyerekezera kuti ali m’Paradaiso.

Yerekeza Kuti Uli M’Paradaiso (1:50)

Munkhani yakuti, “Ndinali Ndi Mafunso Ambiri Omwe Ankandisowetsa Mtendere,” onani zimene zinathandiza munthu wina woukira boma kupeza mayankho a mafunso omwe ankamusowetsa mtendere.

“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, January 1, 2012)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena