NYIMBO 68
Tizifesa Mbewu za Ufumu
Losindikizidwa
1. Bwerani mudzagwire ntchito
Yotumikira Ambuye.
Iye adzakuthandizani
Mukamvera malangizo.
Mbewu za choonadi zikula
M’mitima ya omvetsera.
Choncho tumikirani mwakhama
Pa ntchito imene mwapatsidwa.
2. Kuti ntchito iyende bwino
Zingadalire inuyo.
Mukaphunzitsa bwino anthu
Adzakonda choonadi.
Muziwathandiza kupirira
Mavuto amudzikoli.
Mudzasangalala mukaona
Kuti akukonda choonadi.
(Onaninso Mat. 13:19-23; 22:37.)