Phwando la Chikumbutso la 1994
1 Kodi ndinjira yotani imene iyenera kutsatiridwa paphwando la Chikumbutso? Yesu anagwiritsira ntchito mkate wopanda chotupitsa pa Mgonero wa Ambuye, chotero Mboni za Yehova zimachita zimenezo lerolino. Mkate wotero ngwoyenerera chifukwa ulibe chotupitsa (yisiti), chimene Baibulo limagwiritsira ntchito kuimira chivundi kapena uchimo.—Kuti mupeze mfundo zina onani w90-CN 2/15 16-17.
2 Vinyo wamphesa wofiira wosasukuluka, monga Chianti, Burgundy, kapena claret, ndiwo wokha umene uyenera kugwiritsidwa ntchito. Vinyo wofiira wopangidwa panyumba ungagwiritsiridwe ntchito ngati sunatsekemeretsedwe, kukoleretsedwa, kapena kukalipitsidwa.
3 Pambuyo pa pemphero, mkate udzaperekedwa. Pemphero lina lidzayambitsa kuperekedwa kwa chikho. Akulu ayenera kutsimikizira kuti ulemu ukusonyezedwa pa Mgonero wa Ambuye mwa kukhala ndi ziphiphiritso zamtundu woyenera. Chiŵerengero cha mikate kapena zikho ndi njira imene zidzaperekedwera zimakonzedwa malinga ndi mkhalidwe wakumaloko. Chofunika nchakuti zinthuzo ziyenera kufika kwa onse opezekapo, ngakhale kuti ochuluka adzangopatsira ena popanda kudyako.
4 Sipayenera kukhala dzoma ndi mwambo wocholoŵana. Ayi, popeza kuti pa Mateyu 26:26-30 timaona njira yosavuta imene inagwiritsiridwa ntchito ndi Yesu poyambitsa phwando lofunika kwambiri limeneli. (1 Akor. 11:23-26) Palibe chifukwa chobisira zizindikirozo kumbuyo kwa nsalu yochinga kupulatifomu—monga momwe mipingo ina yachitira. Nyimbo siziyenera kuimbidwa pamene zizindikirozo zikuperekedwa. Okamba nkhani ndi awo amene akupanga makonzedwe ayenera kutsatira malangizo a muautilaini ya nkhani ya Chikumbutso ndi kupeŵa kupangana njira zopeka okha kapena kuyambitsa malingaliro awoawo.
5 Akalinde opatsidwa thayo la kutenga chiŵerengero pamsonkhano uwu ndi ina yonse ayenera kusamala kuti asamapereke ziŵerengero zopambanitsa. Anthu ochotsedwa amaloledwa kupezeka pa Chikumbutso ndipo ayenera kuŵerengedwa. Komabe, munthu wochotsedwa kapena wosabatizidwa amene wadyako samaŵerengedwa. Pamenepa, tiyeni tiyang’anire mwachidwi kuphwando losangalatsa pa March 26. Idzakhala nthaŵi ya kugwiritsira ntchito nzeru komanso nthaŵi yachimwemwe.—Chiv. 19:7; Yoh. 3:29.