Mutu 25
Kuchitira Chifundo Wakhate
PAMENE Yesu ndi ophunzira ake anayi akucheza m’mizinda ya Galileya, mbiri ya zinthu zodabwitsa zimene akuchita ikufalikira m’chigawo chonsecho. Mawu a ntchito zake afika mumzinda wina kumene kuli munthu wodwala khate. Dokotala Luka akumfotokoza monga “wodzala ndi khate.” Itakula kwambiri, nthenda yowopsa imeneyi imayamba kudya ziŵalo za thupi mwapang’onopang’ono. Chotero wakhate ameneyu ali mumkhalidwe womvetsa chisoni.
Pamene Yesu akufika mumzindawo, wakhateyo akumfikira. Malinga ndi Chilamulo cha Mulungu, wakhate ayenera kuchenjeza mofuula kuti, ‘Wodetsedwa, wodetsedwa!’ kutchinjiriza ena kuti asafike pafupi ndi kupatsiridwa nthendayo. Wakhateyo tsopano akugwetsa nkhope yake pansi napempha Yesu kuti: “Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza.”
Nchikhulupiriro chotani nanga chimene munthuyu ali nacho mwa Yesu! Komabe, mmene nthenda yakeyo ikumchititsira kuwonekera kukhala womvetsa chisoni chotani nanga! Kodi Yesu adzachitanji? Kodi inu mukadachitanji? Posonkhezeredwa ndi chifundo, Yesu akutambasula dzanja lake ndi kukhudza mwamunayo, akumati: “Ndifuna, takonzeka.” Ndipo nthaŵi yomweyo khate lizimilirika pa iye.
Kodi mukakonda munthu wina wachifundo motere kukhala mfumu yanu? Njira imene Yesu akuchiritsira wakhate ameneyu imatipatsa chidaliro kuti mkati mwa ulamuliro Waufumu Wake, ulosi wa Baibulo udzakwaniritsidwa: “Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi.” Inde, Yesu adzakwaniritsa chikhumbo cha mtima wake kuthandiza anthu onse okanthidwa.
Ngakhale poyambirira kuchiritsa wakhate kusanachitike, uminisitala wa Yesu wakhala ukupangitsa chisangalalo chachikulu pakati pa anthu. M’kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesaya, Yesu tsopano akuuza munthu wochiritsidwayo kuti: “Wona, usati unene kanthu kwa munthu aliyense.” Pamenepo iye akumulangiza kuti: “Muka, ukadziwonetse kwa wansembe, nupereke pa makonzedwe ako zimene adalamulira Mose, zikhale mboni kwa iwo.”
Koma munthuyo ngwachimwemwe kwambiri kotero kuti sangakhoze kusunga chozizwitsacho kwa iye yekha. Akupita ndi kuyamba kufalitsa mbiriyo kulikonse, mwachiwonekere akumapangitsa chikondwerero ndi chidwi pakati pa anthu kotero kuti Yesu sangapite mowonekera mu mzindawo. Motero, Yesu akukhala kumalo ayekha kumene sikumakhala munthu aliyense, ndipo anthu ochokera mbali zonse akudza kudzamumvetsera ndi kuchiritsidwa matenda awo. Luka 5:12-16; Marko 1:40-45; Mateyu 8:2-4; Levitiko 13:45; 14:10-13; Salmo 72:13; Yesaya 42:1, 2.
▪ Kodi khate lingakhale ndi chiyambukiro chotani, ndipo kodi ndichenjezo lotani limene wakhate anafunikira kupereka?
▪ Kodi wakhate akupempha motani kwa Yesu, ndipo kodi tingaphunzirenji kuchokera kuyankho la Yesu?
▪ Kodi ndimotani mmene munthu wochiritsidwayo akulepherera kumvera Yesu, ndipo kodi nchiyani chimene chiri zotulukapo zake?