Mutu 23
Zozizwitsa Zowonjezereka m’Kapernao
SABATA limene Yesu anaitana ophunzira ake anayi litapita—Petro, Andreya, Yakobo, ndi Yohane—onsewo akupita kusunagoge yamomwemo m’Kapernao. Kumeneko Yesu akuyamba kuphunzitsa, ndipo anthu akudabwitsidwa chifukwa akuwaphunzitsa monga munthu wokhala ndi ulamuliro ndipo osati monga alembi.
Pa Sabata limeneli pali munthu wina wogwidwa ndi chiŵanda. Pambuyo pakanthaŵi, akukuwa ndi mawu aakulu: “Tiri ndi chiyani ife ndi inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzatiwononga ife? Ndikukudziŵani, ndinu Woyerayo wa Mulungu.”
Chiŵanda chimene chikulamulira munthuyo kwenikweni ndicho mmodzi wa angelo a Satana. Podzudzula chiŵandacho, Yesu akuti: “Khala uli chete, nutuluke mwa iye!”
Eya, chiŵandacho chikugwetsera munthuyo pansi kumtsalimitsa ndi kumpangitsa kukuwa kwambiri. Koma chikutuluka mwa munthuyo osampweteka. Aliyense akungodabwa! “Ichi nchiyani?” iwo akufunsa. “Ndi mphamvu alamula ingakhale mizimu yonyansa, ndipo imvera iye.” Mbiri yonena za zimenezi ikufalikira kudera lonse lozungulira malowo.
Pochoka pa sunagoge, Yesu ndi ophunzira ake akumka kunyumba ya Simoni, kapena Petro. Kumeneko apongozi a Petro akudwala kwambiri ndi malungo. ‘Chonde mthandizeni,’ akupempha motero. Chotero Yesu akupita pafupi naye, namgwira dzanja, namdzutsa. Pomwepo akuchiritsidwa nayamba kuwakonzera chakudya!
Pambuyo pake, mmene dzuŵa likuloŵa, anthu ochokera konse akuyamba kudza kunyumba kwa Petro ndi odwala awo. Mwamsanga mzinda wonse wasonkhana pakhomo! Ndipo Yesu akuchiritsa odwala awo onse, mosasamala kanthu kuti nthenda zawo nzotani. Iye akuchiritsa ngakhale munthu wogwidwa ndi ziŵanda. Pamene zikutuluka, ziŵanda zimene wazitulutsazo zikufuula kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.” Koma Yesu akuzidzudzula ndipo sakuzilola kulankhula chifukwa zidziŵa kuti iye ndiye Kristu. Marko 1:21-34; Luka 4:31-41; Mateyu 8:14-17.
▪ Kodi chikuchitika nchiyani m’sunagoge pa la Sabata pambuyo pakuti Yesu waitana ophunzira ake anayi?
▪ Kodi Yesu akumka kuti pamene akuchoka pa sunagoge, ndipo akuchita chozizwitsa chotani kumeneko?
▪ Kodi chikuchitika nchiyani pambuyo pake madzulo amenewo?