Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • uw mutu 3 tsamba 20-28
  • Gwirani Zolimba pa Mawu a Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Gwirani Zolimba pa Mawu a Mulungu
  • Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nchiyani Chimene Chidzathandiza Ena Kulizindikira?
  • Kuwerenga Baibulo kwa Ife Eni
  • Gwiritsitsani Mawu a Mulungu
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Kupindula ndi Kuŵerenga Baibulo Tsiku ndi Tsiku
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kondwerani ndi Mawu a Mulungu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kuŵerenga Baibulo—N’kopindulitsa ndi Kosangalatsa
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
uw mutu 3 tsamba 20-28

Mutu 3

Gwirani Zolimba pa Mawu a Mulungu

1. (a) Kodi ndimotani mmene Israyeli wakale anawonera kutsimikizirika kwa Mawu a Mulungu? (b) Kodi nchifukwa ninji kumeneko kuli kokondweretsa kwa ife?

“MUDZIWA m’mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasowapo mawu amodzi.” Ichi chinali chikumbutso chimene Yoswa anapatsa akulu a Israyeli pambuyo pa kukhazikika m’Dziko Lolonjezedwa. Koma m’zaka zimene zinatsatira iwo sanatengere Mawu a Mulungu m’mtima kosalekeza ndi kuwagwiritsira ntchito mwanjirayo. Kodi nchiyani chinali chotulukapo? Baibulo limamveketsa bwino lomwe kuti monga momwedi malonjezo a Yehova a dalitso anatsimikizirira kukhala odalirika, choteronso, iye anakwaniritsa zimene adanena monga zotulukapo zakusamvera. (Yos. 23:14-16) Cholembedwa chimenecho, limodzi ndi mbali yotsala yonse ya Baibulo, chatetezeredwa kaamba ka chilangizo chathu—kotero kuti “tikhale ndi chiyembekezo” ndi kuti tisachite kanthu kena kamene kangachititse kutayikiridwa kwathu ndi chiyembekezo chimenecho.—Aroma 15:4.

2. (a) Kodi Baibulo liri “louziridwa ndi Mulungu” m’lingaliro lotani? (b) Titazindikira izi, kodi ndithayo lanji limene tiri nalo?

2 Ngakhale kuti “alembi” aumunthu okwanira 40 anagwiritsiridwa ntchito kulemba Baibulo, Yehova iye mwiniyo ndiye Mwiniwake. Kodi chimenecho chitanthauza kuti anatsogolera mwachindunji kulembedwa kwa chirichonse m’menemo? Inde. Monga momwe mtumwi Paulo motsimikizira ananenera, “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu.” Pokhala okhutira ndi zimenezo, tikuchichiza anthu kulikonse kulilabadira ndi kulinganiza miyoyo yawo pa zimene zalembedwamo, monga momwe ife tikuyesayesera kutero.—2 Tim. 3:16; 1 Ates. 2:13.

Kodi Nchiyani Chimene Chidzathandiza Ena Kulizindikira?

3. Kodi ndi njira yabwino koposa yotani yothandizira unyinji wa awo osakhutira kuti Baibulo ndilo Mawu a Mulungu?

3 Ndithudi, unyinji umene timalankhula nawo ulibe chikhutiro chimene tiri nacho chakuti Baibulo liridi Mawu a Mulungu. Kodi ndimotani mmene tingawathandizire? Kawirikawiri njira yabwino koposa ndiyo kutsegula Baibulo ndi kuwasonyeza zimene liri nazo. “Mawu a Mulungu ngamoyo ndipo amapereka mphamvu ndipo ali akuthwa koposa lupanga lirilonse lakuthwa konsekonse . . . ndipo ali okhoza kuzindikira malingaliro ndi zolinga za mtima.” (Aheb. 4:12, NW) “Mawu a Mulungu” ndiwo mawu ake alonjezo, olembedwa m’Baibulo. Siiri mbiri yakale yakufa koma ali amoyo ndipo amayenda mosaletseka kulinga ku kukwaniritsidwa. Pamene akutero, zisonkhezero za mtima wowona za anthu amene amagwirizanitsidwa nalo zimasonyezedwa kuti ziyenerere mikhalidweyo. Chisonkhezero chake chiri champhamvu kwambiri koposa chinthu chirichonse chimene ife enife tinganene.

4. Kodi ndimalongosoledwe osavuta otani a chowonadi cha Baibulo amene asintha khalidwe la anthu ena kulinga ku Baibulo? Chifukwa ninji?

4 Kungowona kokha dzina la Mulungu m’Baibulo kwakhala posinthira pa anthu ambiri. Ena asankha kuphunzira Baibulo pamene asonyezedwa chimene limanena ponena za chifuno cha moyo, chifukwa chake Mulungu amalola kuipa, tanthauzo la zochitika zamakono kapena chiyembekezo chenicheni chozikidwa pa Ufumu wa Mulungu. M’maiko mmene machitachita achipembedzo achititsa anthu kukhala ovutitsidwa kwambiri ndi mizimu yoipa, malongosoledwe a Baibulo a chochititsa cha zimenezi ndi mmene mpumulo ungapezedwere adzutsa chikondwerero. Kodi nchifukwa ninji mfundo zimenezi ziri zochititsa chidwi motero kwa iwo? Chifukwa chakuti Baibulo ndilo magwero okha a chidziwitso chodalirika pa nkhani zofunika zimenezi.—Sal. 119:130.

5. Pamene munthu anena kuti samakhulupirira Baibulo, kodi nchiyani chingakhale chifukwa? Kodi tingamthandize motani?

5 Komabe, bwanji ngati munthu atiuza mwachindunji kuti samakhulupirira Baibulo? Kodi zimenezo ziyenera kuthetsa makambitsiranowo? Sizingatero ngati iye ali wofunitsitsa kuganiza. Tiyenera kudziwona kukhala ndi thayo la kulankhula ndi chikhutiro moimira Mawu a Mulungu. Kungakhale kwakuti munthuyo amawona Baibulo monga bukhu la Dziko Lachikristu. Mbiri yake ya chinyengo ndi kulowerera m’ndale za dziko, kudzanso kupemphapempha kwake ndalama kosalekeza, kungachititse kachitidwe kake kotsutsa Baibulo. Bwanji osafunsa ngati zimenezo ziri choncho? Kutsutsa kwa Baibulo njira zaudziko za Dziko Lachikristu, limodzi ndi mfundo zosemphana pakati pa Dziko Lachikristu ndi Chikristu chowona, zingadzutse chikondwerero chake.—Yerekezerani Mateyu 15:7-9; Yakobo 4:4; Mika 3:11, 12.

6. (a) Kodi nchiyani chimakukhutiritsani inu mwininu kuti Baibulo ndilo Mawu a Mulungu? (b) Kodi ndimfundo zina ziti za kukhutiritsa zingagwiritsiridwe ntchito kuthandiza anthu kuzindikira kuti Baibulo liridi lochokera kwa Mulungu?

6 Kwa ena, makambitsirano achindunji a maumboni a kuuziridwa ali othandiza. Kodi nchiyani chimene mwachiwonekere chimatsimikiziritsa kwa inu kuti Baibulo liri lochokera kwa Mulungu? Kodi chiri chimene Baibulo lenilenilo limanena ponena za chiyambi chake? (2 Tim. 3:16, 17; Chiv. 1:1) Kapena kodi chiri chenicheni chakuti Baibulo liri ndi maulosi ochuluka osonyeza chidziwitso chatsatanetsane chonena za mtsogolo, cha maulosi amene chotero ayenera kukhala atachokera ku magwero oposa aumunthu? (2 Pet. 1:20, 21; Yes. 42:9) Kodi mwinamwake ndiko kugwirizana kwamkati kwa Baibulo, ngakhale kuti liri lolembedwa ndi amuna ambiri mkati mwa nyengo ya zaka 1,610? Kapena kulondola kwake kwausayansi mosiyana ndi zolembedwa zina za pa nthawizo? Kapena kodi ndiko kuwona mtima kwa olemba ake? Kapena kodi ndiko kutetezereka kwake poyang’anizana ndi zoyesayesa zachiwawa za kuliwononga? Chirichonse chimene mwapeza kukhala chochititsa chidwi chingakhozenso kugwiritsiridwa ntchito kuthandiza anthu ena.

Kuwerenga Baibulo kwa Ife Eni

7, 8. (a) Kodi nchiyani chimene ife aliyense payekha tiyenera kukhala tikuchita ndi Baibulo? (b) Kodi timafunikiranji kuwonjezera pa kuwerenga Baibulo kwaumwini, ndipo kodi Baibulo lenilenilo limasonyeza motani mfundoyi? (c) Kodi ndimotani mmene inu mwininu mwapezera kuzindikira zifuno za Yehova?

7 Kuwonjezera pa kuthandiza ena kukhulupirira Baibulo, ife enife tifunikira kukhala ndi nthawi ya kuliwerenga mokhazikika. Kodi inu mukuchita zimenezo? Pa mabukhu onse amene analembedwa, limeneli ndilo lofunika koposa. Ndithudi, chimenecho sichimatanthauza kuti ngati tiriwerenga sitifunikiranso kanthu kena. Malemba amachenjeza motsutsa kudzilekanitsa ife eni, tikumalingalira kuti tingakhoze kuchita chinthu chirichonse mwa kusanthula kwa ife eni. Ponse pawiri phunziro laumwini ndi kufika pamisonkhano mokhazikika ziri zofunika ngati titi tikhale Akristu achikatikati.—Miy. 18:1; Aheb. 10:24, 25.

8 Kaamba ka phindu la ife eni Baibulo limatiuza za mdindo wina Wachiaitiopiya kwa amene mngelo anatsogolerako mlaliki Wachikristu Filipo pamene mdindoyo anali kuwerenga ulosi wa Yesaya. Filipo adafunsa mwamunayo kuti: “Kodi muzindikira chimene muwerenga?” Modzichepetsa Mwaitiopiyayo anayankha: “Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine?” Anafulumiza Filipo kulongosola mbali ya Lembalo. Tsopano, Filipo sanali kokha wowerenga Baibulo woima payekha amene panthawiyo anapereka lingaliro lake la Malemba. Ayi; cholembedwacho chimasonyeza kuti anali atasunga kugwirizana kwathithithi ndi atumwi mu mpingo pa Yerusalemu ndipo anali chiwalo cha gulu lowoneka ndi maso la Yehova. Chotero anakhoza kuthandiza Mwaitiopiya kupindula ndi chilangizo chimene Yehova anachititsa kupezeka kupyolera mwa gulu limenelo. (Mac. 6:5, 6; 8:5, 14, 15, 26-35) Mofananamo lerolino, kodi ndani wa ife amene anafikira pa kuzindikira bwino ndi kolondola zifuno za Yehova mwa iye yekha? Mmalo mwake, tinafunikira, ndipo tikupitirizabe kufunikira, chithandizo chimene Yehova amapereka mwachikondi kupyolera mwa gulu lake lowoneka ndi maso.

9. Kodi ndimaprogramu a kuwerenga Baibulo otani amene angapindulitse ife tonse?

9 Kutithandiza kugwiritsira ntchito ndi kuzindikira Baibulo, gulu la Yehova limapereka chidziwitso chabwino koposa Chamalemba mu Nsanja ya Olonda ndi mabukhu ena ofanana. M’kuwonjezera, programu yanthawi zonse ya kuwerenga Baibulo imalinganizidwa kaamba ka ife m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki m’mipingo ya Mboni za Yehova. Ena a Mboni za Yehova amalinganiza kuwerenga Baibulo kotsatizanatsatizana kuwonjezera apa. Phindu lalikulu lingadze kuchokera m’nthawi yowonongedwera kupenda Malemba Opatulika. (Sal. 1:1-3; 19:7, 8) Kodi inu mwininu mwawerenga Baibulo lathunthu? Ngati simunatero, pangani kuyesayesa kwapadera kutero. Ngakhale ngati simukumvetsetsa mokwanira chinthu chirichonse kukhala kwanu ndi lingaliro lake lonse kudzakhala kopindulitsa kwambiri. Ngati munafunikira kuwerenga masamba anai kapena asanu okha patsiku, mukanatha Baibulo pafupifupi m’chaka chimodzi.

10. (a) Kodi ndiliti pamene muchita kuwerenga Baibulo kwanu? (b) Kodi nchifukwa ninji kuwerenga nthawi yonse kuli kofunika?

10 Kodi ndi liti pamene inu mwininu mungachite makonzedwe a kuwerenga Baibulo kumeneku? Ngati muli wokhoza kupatula nthawi ngakhale mphindi 10 kapena 15 patsiku, ha nzopindulitsa chotani nanga mmene zimenezo zidzakhalira! Ngati simungakhoze, linganizani nthawi zokhazikika za kutero mlungu uliwonse, ndiyeno mamatirani ku programu imeneyo. Kuwerenga Baibulo kuyenera kukhala chizolowezi cha moyo wonse, mofanana ndi kudya chakudya. Monga mudziwa, ngati zizolowezi za kudya za munthu ziri zosayenera, thanzi lake lidzafooka. Ndimo mmenenso ziriri, ndi mkhalidwe wathu wauzimu. Moyo wathu umadalira pa kudyetsedwa mokhazikika ndi “mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.”—Mat. 4:4.

11. Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala cholinga chathu m’kuwerenga Baibulo?

11 Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala cholinga chathu m’kuwerenga Baibulo? Kukakhala kulakwa ngati chonulirapo chathu chinali kokha kufola masamba olinganizidwa kapena ngakhale kokha kupeza moyo wamuyaya. Kuti tipindule kosatha, tiyenera kukhala ndi zisonkhezero zabwino kopambana—chikondi cha pa Mulungu, chikhumbo cha kumdziwa bwino kwambiri, kuzindikira chifuniro chake ndi kumlambira movomerezeka. (Yoh. 5:39-42) Khalidwe lathu liyenera kufanana ndi la mlembi wa Baibulo amene anati: “Mundidziwitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu.”—Sal. 25:4

12. (a) Kodi nchifukwa ninji kupeza “chidziwitso cholongosoka” kuli kofunika, ndipo nkuyesayesa kotani kumene tingafunikire powerenga kuti tichipeze? (b) Monga momwe kwasonyezedwera patsamba 27, kodi ndi malingaliro otani amene tingapende nawo mopindulitsa zimene timawerenga m’Baibulo? (c) Sonyezani mwa fanizo mfundo zisanu zimenezi, imodzi imodzi, mwa kuyankha mafunso operekedwa pa mapeto a ndime ino. Tsimikizirani kugwiritsira ntchito Baibulo lanu.

12 Pamene tivomereza chiphunzitso chimenecho, chiyenera kukhala chikhumbo chathu kupeza “chidziwitso cholongosoka.” Popanda chimenecho, kodi ndimotani mmene tingagwiritsirire ntchito Mawu a Mulungu moyenerera m’miyoyo yathu kapena kuwalongosola molondola kwa ena? (Akol. 3:10; 2 Tim. 2:15) Kupeza chidziwitso cholongosoka kumafuna kuti tiwerenge mosamalitsa, ndipo ngati mawuwo ali ozamirapo tingafunikire kuwawerenga nthawi yoposa imodzi kuchitira kuti timvetsetse lingaliro lake. Tidzapindulanso ngati tikhala ndi nthawi ya kusinkhasinkha pa chidziwitsocho, tikumalingalira za mawuwo mbali zosiyanasiya. Njira zofunika zisanu zolingaliridwa kutulukirira zasonyezedwa pa tsamba 27 la bukhu lino. Mbali zambiri za Malemba zingapendedwe mopindulitsa mwa kugwiritsira ntchito imodzi kapena zowonjezereka za zimenezi. Pamene muyankha mafunso pa masamba otsatira mudzawona mmene zimenezo ziriri choncho.

(1) Kawirikawiri chigawo cha lemba chimene mukuwerenga chimasonyeza mtundu wa munthu amene Yehova ali.

Pamene tisinkhasinkha moyamikira pa chimene Baibulo limatiuza ponena za ntchito za Yehova za chilengedwe, kodi kutero kumayambukira motani khalidwe lathu kulinga kwa iye? (Sal. 139:13, 14; kuchokera pa Yobu mutu 38-42 wonani makamaka 38:1, 2 ndi 42:8 ndiyeno 42:1-6.)

Kaamba ka zimene Yesu ananena pa Yohane 14:9, 10, kodi nchiyani chimene tinganene ponena za Yehova kuchokera mu zochitika zofanana ndi cholembedwa pa Luka 5:12, 13?

(2) Lingalirani mmene cholembedwacho chimathandizira kukulitsa mutu wankhani wa Baibulo, ndiko kuti, kulemekezedwa kwa dzina la Yehova mwa Ufumu wokhala m’manja mwa Yesu Kristu Mbewu Yolonjezedwa.

Kodi ndimotani mmene miliri pa Aigupto imagwirizanira ndi mutu wankhani umenewu? (Wonani Eksodo 5:2; 9:16; 12:12.)

Kodi bwanji za cholembedwa chokondweretsa mtima chonena za Rute mkazi Wachimoabu? (Rute 4:13-17; Mat. 1:1, 5)

Kodi ndimotani mmene chilengezo cha Gabrieli kwa Mariya cha kubadwa kunalimkudza kwa Yesu chimayenerera? (Luka 1:26-33)

Kodi nchifukwa ninji kudzozedwa kwa ophunzira a Yesu ndi mzimu woyera pa Pentekoste kuli kofunika? (Mac. 2:1-4; 1 Pet. 2:4, 5, 9; 2 Pet. 1:10, 11)

(3) Mawu apatsogolo ndi pambuyo ali ndi chiyambukiro pa tanthauzo la mavesi akuti-akuti.

Kodi nkwayani kumene mawu a pa Aroma 5:1 ndi 8:16 analunjikitsidwako? (Wonani Aroma 1:7.)

Kodi mawu apatsogolo ndi pambuyo amasonyeza kuti 1 Akorinto 2:9 akulankhula za moyo wapadziko lapansi m’Dongosolo Latsopano la Mulungu? Monga momwe kwasonyezedwera m’vesi 6-8, kodi ndimaso ndi makutu ayani amene sanali kumvetsetsa zinthu zimene Paulo anali kulemba?

(4) Dzifunseni mmene mungagwiritsirire ntchito inu mwini zimene mukuwerenga.

Kodi cholembedwa chonena za kupha Abele kwa Kaini chiri kokha chokondweretsa cha m’mbiri kapena kodi muli uphungu kaamba ka ife? (Gen. 4:3-12; 1 Yoh. 3:10-15; Aheb. 11:4)

Pamene tiwerenga (mu Eksodo mpaka ku Deuteronomo) ponena za zokumana nazo za Israyeli m’chipululu, kodi ndikugwiritsira ntchito kwa umwini kotani kumene tiyenera kupanga? (1 Akor. 10:6-11)

Kodi uphungu wa kudzisungira wolembedwera Akristu odzozedwa umagwira ntchito kwa anthu amene ali ndi chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi? (Yerekezerani Numeri 15:16; Yohane 10:16.)

Ngakhale ngati tiri m’kaimidwe kabwino ndi mpingo Wachikristu, kodi pali kufunikira kulingalira njira zimene tingagwiritsirire ntchito modzala uphungu wa Baibulo umene tikuudziwa kale? (2 Akor. 13:5; 1 Ates. 4:1)

(5) Lingalirani mmene mungagwiritsirire ntchito zimene mukuwerenga ndi kuthandiza ena.

Kodi ndani amene angathandizidwe ndi cholembedwa cha chiukiriro cha mwana wamkazi wa Yairo? (Luka 8:41, 42, 49-56)

13. Kodi nzotulukapo zotani zimene tingayembekezere kuchokera ku programu ya kuwerenga Baibulo yopitirizabe ndi kuphunzira ndi gulu la Yehova?

13 Ha ndikopindulitsa kwambiri chotani nanga mmene kuwerenga Baibulo kumakhalira pamene kuchitidwa mwa dongosolo iri! Ndithudi, kuwerenga Baibulo ndikovuta—ntchito imene tingaichite mopindulitsa kwanthawi yonse yamoyo. Koma pamene titero tidzakhala amphamvu kwambiri mwauzimu. Kudzatiyandikizitsa pafupiko ndi Atate wathu wachikondi, Yehova, ndi kwa abale athu Achikristu. Kudzatithandiza kulabadira uphungu wa kupitirizabe ‘kugwiritsitsa pamawu amoyo.’—Afil. 2:16.

Makambitsirano a Kupenda

● Kodi nchifukwa ninji Baibulo linalembedwa ndi kutetezeredwa kufikira tsiku lathu?

● Kodi ndimotani mmene tingathandizire ena kulizindikira?

● Kodi nchifukwa ninji kuwerenga Baibulo kwa ife eni kwanthawi zonse kuli kopindulitsa? Kodi nkuchokera m’malingaliro asanu otani amene tingapende mopindulitsa zimene tiwerenga?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 27]

Pamene Muwerenga Baibulo Sinkhasinkhani—

Chimene mbali iriyonse imakuuzani ponena za Yehova monga munthu

Mmene imagwirizanira ndi mutu wankhani wonse wa Baibulo

Mmene mawu apa-tsogolo ndi pambuyo amayambukirira tanthauzo

Mmene ingayambukirire moyo wanu

Mmene mungayigwiritsirire ntchito kuthandiza ena

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena