Nyimbo 44
Yehova Amasamaladi
1. Chisamaliro cha M’lungu.
Chimatitonthoza ife.
‘Adziŵa ngakhale tsitsi lathu.’
Tingaderenji nkhaŵa?
2. Ngakhale tisautsidwa,
Sitidzachita tondovi.
Ngati Ya asamala mbalame,
Adzatisamaladi.
3. Mazunzo ambirimbiri
Amagwera Akristuwo.
M’zimenezi Ya amatiyenga;
Adzatithandizabe.
4. Mosakayikira M’lungu,
Adzatisamaliradi.
Pochitabe utumiki wathu,
Adzatipatsa mphotho.