Nyimbo 54
Tiyenera Kukhala Oyera
1. Mulungu wati tikhale oyera,
Poti Kristu anatiyeretsa.
Monga oyera, odzichepetsa,
Openyerera onse awone.
2. Yehova anatipatula ife,
“Mtundu woyera” ndi “nkhosa zina.”
Tisonyezetu mwa kayendedwe
Kuti timasunga malamulo.
3. Popitabe patsogolo Mulungu
Amatiyenga modabwitsadi.
Apatsa anthu ake cho’nadi,
Choncho ‘tisayang’ane kumbuyo.’
4. Tipeze mipata tikumakula,
M’chiyero, kuyenda m’kuunika.
Tama Yehova, mkondweretseni,
Ali Woyera ndi wolungama.