Pitirizanibe Kuchita Zochuluka m’Ntchito ya Ambuye
1 Monga Mboni za Yehova, ife ndife anthu otanganitsidwa. Tili ndi “zochita zochuluka m’ntchito ya Ambuye” ndipo tili ndi chidaliro chakuti, pamene tisungabe cholinga chathu cha utumiki wathu chili chabwino ndipo chozikidwa pa chikondi, ‘ntchito yathu sili chabe mogwirizana ndi Ambuye.’ (1 Akor. 15:58, NW) Timaitana anthu ena a mitundu yonse kudzagaŵana nafe m’ntchito yathu yabwino yolengeza mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. Pokhala okondweretsedwa ndi kupita patsogolo kwa ntchito imeneyi ya Ufumu, timasunga cholembedwa cha ntchito yathu, cha maola otheredwa m’kulalikira ndi zotulukapo zopezedwa.
2 Nkolimbikitsa kuona kuti m’miyezi yaposachedwapa m’Malaŵi muno, chiŵerengero cha ofalitsa ochitira lipoti utumiki wawo wakumunda chawonjezeka. Komabe, padakali mbali zambiri zimene zikufunikira kuwongolera. Pali kufunikira kwa kuwonjezera ntchito yathu mwa kukhala ndi phande mu utumiki wa kukhomo ndi khomo, mwa kuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba ndi mwa kugaŵira magazini. Mpingo uliwonse uyenera kutsimikizira kuti uli ndi makonzedwe a ntchito ya Tsiku la Magazini lokhazikika monga ngati pa masiku a Loŵeruka, monga momwe kunagogomezedwera mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 1994, tsamba 24, ndime 17. Kodi mpingo wanu uli ndi makonzedwe ameneŵa? Ngati ulibe, bwanji osayamba tsopano?
3 Monga momwe kwatchulidwira m’ndime yoyamba, kuchitira lipoti utumiki wathu wakumunda kuli kanthu kena kamene tonsefe tiyenera kukaona kukhala kofunika. Nkokondweretsa kuona kuti mipingo yambiri tsopano ikutumiza malipoti awo amwezi ndi mwezi panthaŵi yake. Tikufuna kukuthokozani chifukwa cha zimenezi. Wofalitsa aliyense apitirizetu kulabadira zikumbutso zonena za malipoti ochedwa zoperekedwa kumipingo mobwerezabwereza mu Utumiki Wathu Waufumu. Chikumbutsocho chili motere: “Ngati muchoka pampingo wanu kwanyengo yaifupi yosafika miyezi itatu, pitirizanibe kutumiza malipoti a utumiki wanu wakumunda kumpingo wa kwanu. Ngati mutumiza malipoti oposa limodzi panthaŵi imodzi lembani mosiyanitsa kaamba ka mwezi uliwonse. MUSAPHATIKIZE malipoti a miyezi yosiyana pasilipi limodzi.”—Onani Utumiki Wathu Waufumu wa December 1993, tsamba 4.
4 Mfundo ina imene ifunikira chisamaliro cha ofalitsa onse njonena za utumiki wa upainiya wothandiza. Nkwabwino kuona kuti chiŵerengero cha awo amene akukhala ndi phande m’ntchitoyi chawonjezereka pamene chiyerekezeredwa ndi chiŵerengero chapamwamba cha chaka chatha. Komabe, polingalira chiŵerengero cha ofalitsa m’dziko lathuli, zikusonyeza kuti padakali ofalitsa ambiri amene sakukhala ndi phande mu upainiya wothandiza. Kodi nchiyani chimene chingakhale vuto? Ena a ife tili ndi zifukwa zomveka. Komabe, sitiyenera kuiŵala kuti Satana ndi dongosolo lake la zinthu amayesa kuchititsa moyo kukhala wovuta ndi kutitanganitsa kwambiri kwakuti timakhala ndi nthaŵi yochepa ya zinthu za Ufumu kapena imatisoŵeratu. (Mat. 6:33) Monga munthu panokha, kodi mungasinthe zochita zanu kotero kuti lingaliro lanu, zonulirapo zanu, ndi moyo wanu zikhale zosavuta, zosacholoŵana?
5 Akulu ndi atumiki otumikira ayenera kutsogolera mu ntchito ya upainiya wothandiza. Kukhala ndi ofalitsa ambiri okhala ndi phande m’kuchita upainiya wothandiza kungadzetse mapindu ambiri auzimu mu mpingo monga momwe zitsanzo zotsatirazi zikusonyezera. Mkulu wina anasimba kuti zakhala “zolimbikitsa kwambiri mu mpingo ndipo zathandiza mkhalidwe wauzimu ndi chiŵerengero cha osonkhana.” Mkulu winanso amene iyemwiniyo analembetsa upainiya anali wokondwa kwambiri: “Ambiri agwirizana nafe . . . pamene ena, amene sanalembetse, afutukulabe utumiki wawo kwambiri.” Ndemanga zambiri zofanana nazo zikusonyeza kuti makonzedwe ameneŵa achirikiza kwambiri chisangalalo ndi mkhalidwe wauzimu wa mipingo kuwonjezera pa kusonkhezera utumiki wachangu wowonjezereka ndi wogwira mtima.
6 Kodi mungakhale ndi phande mu ntchito ya upainiya wothandiza m’miyezi ikudzayo? Kodi muli ndi nthaŵi ya kukhala ndi phande mu ntchito imeneyi? Kodi mungasinthe zochita zanu kuti mukhale ndi nthaŵi? Lingalirani mikhalidwe yanuyo mwapemphero. Kuchita upainiya wothandiza ndiko mlatho wowolokerera ku utumiki wa upainiya wokhazikika. Bwanji osapempha ena a mu mpingo amene amakwaniritsa zofunika za ntchito ya upainiya wothandiza kutumikira nanu?
7 Gwiritsirani ntchito uphungu umene Paulo anapatsa Timoteo wa kupangitsa ‘kukula mtima kwanu kuonekera’ ndi “kukwaniritsa utumiki wanu kotheratu.” Pempherani kuti Yehova adalitse zoyesayesa zanu ndi za anthu ake kulikonse amene nawonso akuyesayesa ‘kukwaniritsa utumiki wawo kotheratu.’ Ntchito yathu yochitidwa mogwirizana imeneyi imlemekezetu.—1 Tim. 4:15; 2 Tim. 4:5, NW.