Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Choikidwiratu
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Mwana wake kuti iye akhale mwana woyamba wa abale ambiri.” (Ndiponso Aefeso 1:5, 11) Komabe, kwa anthu amodzimodzi amenewa, 2 Petro 1:10 amati: “Wonjezani kuchita changu kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe anu; pakuti mukachita izi simudzakhumudwa nthaŵi yonse.” (Ngati anthu anaikidwiratu ku chipulumutso, sikukanatheka kwa iwo kulephera, mosasamala kanthu za chimene anachita. Popeza kuyesayesa kuli kofunika kwa anthu, kuyenera kukhala kagulu kamene kali koikidwiratu. Mulungu analinganiza kuti kagulu kathunthu kakachita mogwirizana ndi chitsanzo choperekedwa ndi Yesu Kristu. Komabe, awo osankhidwa ndi Mulungu kukhala mbali ya kaguluko, ayenera kutsimikizira kukhala okhulupirira ngati ati apezedi mphotho yoikidwa pamaso pawo.)

      Aef. 1:4, 5: “Monga anatisankha ife mwa iye [Yesu Kristu] lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima ndi opanda chirema pamaso pake m’chikondi. Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a iye yekha mwa Yesu Kristu, monga umo kunakomera chifuniro chake.” (Nkokondweretsa kuwona kuti, pa Luka 11:50, 51 Yesu akugwirizanitsa “kukhazikika kwa dziko” ndi nthaŵi ya Abele. Abele ndiye munthu woyamba amene anapitirizabe kukhala ndi chiyanjo cha Mulungu nthaŵi yonse ya moyo wake. Chotero, panali pambuyo pa chipanduko mu Edene, koma Abele asanakhaliridwe pakati pamene Mulungu anapanga chifuno chake cha kutulutsa “mbewu” kupyolera mwa imene chilanditso chikaperekedwa. [Gen. 3:15] Mulungu analinganiza kuti limodzi ndi Mbewu yaikuluyo, Yesu Kristu pakakhala kagulu ka otsatira ake okhulupirika amene akakhala ndi mbali limodzi naye m’boma latsopano lolamulira dziko lapansi, Ufumu Waumesiya.)

      Kodi nyenyezi ndi maplaneti zimasonkhezera zochitika m’miyoyo yathu kapena kupereka zizindikiro zimene tiyenera kupenda popanga zosankha?

      Kodi ndiati amene ali magwero a kupenda nyenyezi?

      “Kupenda nyenyezi kwa maiko Akumadzulo kungalondoledwe m’mbuyo mwachindunji kukafika kunthanthi ndi zizoloŵezi za Akaladayo a m’ma 2000 B.C.”—The Encyclopedia Americana (1977), Vol. 2, p. 557.

      “Kupenda nyenyezi kunali kozikidwa pamalingaliro aŵiri Achibabulo: zakuthambo, ndi kulingaliridwa kukhala milungu kwa zakuthambo. . . . Ababulo analingalira kuti maplaneti anali ndi chisonkhezero chimene munthu akayembekezera kwa milungu yawo yosiyanasiyana.”—Great Cities of the Ancient World (New York, 1972), L. Sprague de Camp, p. 150.

      “M’Babulo kudzanso m’Suriya monga mphukira yachindunji ya miyambo Yachibabulo . . . kupenda nyenyezi kumapezeka m’mazoma amwambo monga imodzi ya njira ziŵiri zazikulu zogwiritsidwa ntchito ndi ansembe . . . zotsimikizirira chifuniro ndi cholinga cha milungu, ina ikumakhala kupendedwa kwa chiŵindi cha nyama yoperekedwa nsembe. . . . Mayendedwe a dzuŵa, mwezi ndi maplaneti asanu zinaŵerengedwa kukhala zoimira ntchito ya milungu isanu yonenedwayo, limodzi ndi mulungu mwezi Sin ndi mulungu dzuŵa Shamash, pokonzekera kuwonekera padziko lapansi.”—Encyclopædia Britannica (1911), Vol. II, p. 796.

      Kodi nchiyani chimene chiri lingaliro la Mlengi wa anthu kulinga ku chizoloŵezi chimenechi?

      Deut. 18:10-12: “Asapezeke mwa inu munthu . . . wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Popeza yense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.”

      Kwa Ababulo iye anati: “Openda nyenyezi anu, oyang’anitsitsa nyenyezi anu amene amaneneratu mtsogolo mwanu mwezi ndi mwezi, achitetu khama, nakupulumutseni! Koma tawonani, iwo amuka mofanana ndi mungu . . . Chotero kwa amatsenga anu ochulukawo mwatsatsa nawo malonda moyo wanu wonse: akhumudwa, yense panjira yakale, ndipo palibe mmodzi wakukupulumutsani.”—Yes. 47:13-15, NE.

  • Dipo
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Dipo

      Tanthauzo: Mtengo wolipiridwa kuwombolera kapena kumasula kungongole kapena mkhalidwe wopsinjika. Mtengo wa dipo wapadera koposa ndiwo wa mwazi wokhetsedwa wa Yesu Kristu. Mwa kulipirira mtengo wa dipo limenelo kumwamba, Yesu anatsegulira njira ana a Adamu yolanditsidwira ku uchimo ndi imfa zimene tonsefe timalandira monga choloŵa chifukwa cha uchimo wa kholo lathu Adamu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena