Nyimbo 102
Chisangalalo cha Chiukiliro
1. Lazaro nagona
M’manda amwala.
Alongo namlira!
Sakumudzutsa.
‘Ngati bwenzi Yesu
Akanadzatu,
Akali kudwala
Sakadafatu.’
Kumandako Yesu
Anafuula,
Kwa wakufa uja:
‘Lazaro uka!’
Nkana womangidwa
Lazaro ’namva.
Mabwezi akewo
Anakondwera!
2. Odalira Kristu
Kuwamasula,
Anamva chisoni
Pomwe anafa.
Mabwenzi a Yesu
Anamuika.
Anadzadzidwatu
Ndi chisonidi!
Komabe m’Hademo
Sanasiyidwe.
Anaukitsidwa
Ndi Mulunguyo.
Ophunzira ake
Anakondwera.
Mfungulo za imfa
Ziri ndi Kristu.
3. Tchimo la Adamu
Ladzetsa imfa;
Chiukilirocho
Chidza ndi Kristu.
Okhala mu Hade
Adzamumvatu
Nadzaukitsidwa
Nadzakondwera.
Adzaweruzidwa
Mwachilungamo
Pazochita zawo
Mu Ufumuwo.
Awo olembedwa
M’bukhu la M’lungu
Adzakhala m’dziko
Latsopanolo.