-
ChikhulupiriroKukambitsirana za m’Malemba
-
-
kanthu pamalonjezo a Mulungu ndiyeno nawona umboni wa dalitso la Mulungu pa zimene wachita.—Wonani Salmo 106:9-12.
Chitsanzo: Mwinamwake inu muli ndi bwenzi limene mukananena za iro kuti: ‘Mwamuna uja ndimamkhulupirira. Ndingamdalire kuti adzasunga mawu ake; ndipo ndidziŵa kuti ngati ndiri ndi vuto, adzandithandiza.’ Sikukuwonekera ngati kuti mungakhale mukunena zimenezo ponena za munthu aliyense amene munakumana naye dzulo kwanthaŵi yoyamba, kodi sichoncho? Akafunikira kukhala munthu wina amene munakhala naye kwanthaŵi yaitali, munthu amene watsimikizira kudalirika kwake mobwerezabwereza. Nzofanana ndi chikhulupiriro cha chipembedzo. Kuti mukhale ndi chikhulupiriro, mufunikira kupeza nthaŵi ya kudziŵa Yehova ndi njira yake yochitira zinthu.
Chikhulupiriro chakuti kuli Mulungu
Wonani tsamba 306-313, pamutu waukulu wakuti “Mulungu.”
Chikhulupiriro m’chiyembekezo cha dongosolo latsopano lolungama lazinthu
Pamene munthu afikira kukhala wozoloŵerana bwino ndi cholembedwa cha ntchito za Mulungu ndi atumiki ake, amakhala ndi lingaliro lofanana ndi la Yoswa, amene anati: “Mudziŵa mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pamawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasowapo mawu amodzi.”—Yos. 23:14.
Malonjezo a Baibulo athanzi lokonzedwanso, chiukiriro cha akufa, ndi zina zotero, amatsimikiziridwa ndi cholembedwa cha zozizwitsa zochitika ndi Yesu Kristu. Zimenezi siziri nthano. Ŵerengani zolembedwa za Mauthenga Abwino ndi kuwona umboni wakuti ziri ndi chitsimikiziro chonse cha kukhala chowonadi cha zochitika za m’mbiri. Malo a kumene zinachitikira atchulidwa, maina a olamulira adziko a panthaŵiyo aperekedwa; cholembedwa choposa mboni yowona ndi maso imodzi chasungidwa. Kusinkhasinkha paumboni umenewu kungathe kulimbikitsa chikhulupiriro chanu m’malonjezo a Baibulo.
Pitani ku Nyumba Zaufumu za Mboni za Yehova ndi kumisonkhano yawo yaikulu yotsegukira anthu onse, ndipo mungadziwonere nokha umboni wakuti kugwiritsiridwa ntchito kwa uphungu wa Baibulo kumasanduliza miyoyo, kuti kungakhoze kupangitsa anthu kukhala owona mtima ndi olungama mwa makhalidwe, kuti kungakhozetse anthu a mafuko onse ndi mitundu kukhalira ndi moyo ndi kugwirira ntchito pamodzi mu mzimu waubale wopanda chinyengo wowona.
Kodi ntchito ziridi zofunika ngati munthu ali ndi chikhulupiriro?
Yak. 2:17, 18, 21, 22, 26: “Chikhulupiriro, chikapanda kukhala ndi ntchito, chikhala chakufa mkati mwakemo. Koma wina akati, Iwe uli nacho chikhulupiriro, ndipo ine ndiri nazo ntchito; undiwonetse ine chikhulupiriro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuwonetsa iwe chikhulupiriro changa chotuluka m’ntchito zanga. Abrahamu kholo lathu, sanayesedwe wolungama ndi ntchito kodi, paja adapereka mwana wake Isake nsembe paguwa lansembe? Upenya kuti chikhulupiriro chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo motuluka mwa ntchito chikhulupiriro chidayesedwa changwiro; pakuti monga thupi lopanda mzimu liri lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa.”
Chitsanzo: Mnyamata angapalane chibwenzi ndi msungwana, akumamuuza kuti amamkonda. Koma ngati mnyamatayo safunsira msungwanayo kuti akwatirane, kodi iye akusonyezadi kuti chikondi chake nchowona? Mofananamo, ntchito ndizo njira yosonyezera kutsimikizirika kwa chikhulupiriro chathu ndi chikondi. Ngati sitimvera Mulungu sitimamkondadi kapena kukhala ndi chikhulupiriro m’kulungama kwa njira zake. (1 Yoh. 5:3, 4) Komatu sitingalipidwe chipulumutso mosasamala kanthu za ntchito zimene timachita. Moyo wamuyaya uli mphatso yochokera kwa Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu, sichiri malipiro a ntchito zathu.—Aef. 2:8, 9.
-
-
Chikumbutso (Mgonero wa Ambuye)Kukambitsirana za m’Malemba
-
-
Chikumbutso (Mgonero wa Ambuye)
Tanthauzo: Chakudya chokumbukira imfa ya Yesu Kristu; chifukwa chake chikutchedwa chikumbutso cha imfa yake, imfa imene inakhala ndi ziyambukiro zazikulu kwambiri kuposa ya munthu wina aliyense. Chimenechi ndicho chochitika chokha chimene Ambuye Yesu Kristu analamula ophunzira ake kuchikumbukira. Chimatchedwanso Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, kapena Mgonero wa Ambuye.—1 Akor. 11:20.
Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la Chikumbutso?
Kwa ophunzira ake okhulupirika Yesu anati: “Chitani ichi chikumbukiro changa.” (Luka 22:19) Polembera ziŵalo zauzimu za mpingo wa obadwa ndi mzimu Wachikristu, mtumwi Paulo
-