Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 133
  • Yesu Achita Zonse Zimene Mulungu Afuna

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Achita Zonse Zimene Mulungu Afuna
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Yesu Amaliza Zonse Zimene Mulungu Afuna
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kutsegula Njira Yobwerera ku Paradaiso
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Paradaiso Wobwezeretsedwanso Alemekeza Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Yesu Adzabweretsa Paradaiso Kenako Adzamaliza Kugwira Ntchito Imene Anapatsidwa
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 133

Mutu 133

Yesu Achita Zonse Zimene Mulungu Afuna

PAMENE Mfumu Yankhondo Yesu Kristu achotsa Satana ndi dziko lake losalungama, padzakhala chochititsa chisangalalo chotani nanga! Ulamuliro Wazaka Chikwi wamtendere wa Yesu potsirizira pake udzayamba!

Motsogozedwa ndi Yesu ndi mafumu anzake, opulumuka Armagedo adzayeretsa mabwinja osiidwa ndi nkhondo yolungamayo. Mwinamwake opulumuka apadziko lapansi adzabalanso ana kwakanthaŵi, ndipo ameneŵa adzakhala ndi phande m’ntchito yosangalatsa ya kusandutsa dziko lapansi kukhala munda wokongola koposa wonga paki.

M’nthaŵi yokwanira Yesu adzaukitsa mamiliyoni ankhaninkhani kuchokera kumanda kudzasangalala ndi Paradaiso wokongola ameneyu. Adzachita zimenezi kukwaniritsa chitsimikizo cha iye mwini chakuti: ‘Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda . . . adzatulukira.’

Pakati pa awo amene Yesu adzaukitsa padzakhala amene kale anali wochita zoipa amene anafera pambali pake pamtengo wozunzirapo. Kumbukirani kuti Yesu anamlonjeza kuti: ‘Indetu ndinena ndi iwe lerolino, Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.’ Ayi, munthuyo sadzatengeredwa kumwamba kukalamulira monga mfumu pamodzi ndi Yesu, ndiponso Yesu sadzakhala munthu kachiŵirinso ndi kukhala ndi moyo padziko lapansi la Paradaiso pamodzi naye. Mmalomwake, Yesu adzakhala ndi amene kale anali wochita zoipayo m’lingaliro lakuti Iye adzamuukitsira kumoyo m’Paradaiso ndi kutsimikirizira kuti zosoŵa zake, ponse paŵiri zakuthupi ndi zauzimu, zikusamaliridwa, monga momwe kwasonyezedwera patsamba lotsatirali.

Tangoganizani! Pansi pachisamaliro chachikondi cha Yesu, banja lonse la anthu—opulumuka Armagedo, ana awo, ndi zikwi mamiliyoni ambiri oukitsidwa amene anamumvera—adzatukulidwira ku ungwiro waumunthu. Yehova, kudzera mwa Mwana wake mfumuyo, Yesu Kristu, adzakhala ndi anthu mwauzimu. “Ndipo,” monga momwedi mawu amene Yohane anamva kuchokera kumwamba akunenera, “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.” Palibe munthu padziko lapansi amene adzavutika kapena kudwala.

Podzafika mapeto a Ulamuliro Wazaka Chikwi wa Yesu, mkhalidwewo udzakhala monga momwedi Mulungu analinganizira poyamba pamene anauza anthu aŵiri oyambawo, Adamu ndi Hava, kubalana ndi kudzaza dziko lapansi. Inde, dziko lapansi lizadzadza ndi fuko lolungama la anthu angwiro. Zimenezi ziri chifukwa chakuti mapindu a nsembe yadipo ya Yesu adzakhala atagwira ntchito kwa aliyense. Imfa yochititsidwa ndi tchimo la Adamu sidzakhalakonso!

Chotero, Yesu adzakhala atachita zonse zimene Yehova anafuna kwa iye. Chifukwa chake, pamapeto a zaka chikwi, iye adzapereka Ufumuwo ndi banja la anthu lopangidwa kukhala langwiro kwa Atate wake. Pamenepo Mulungu adzamasula Satana ndi ziŵanda zake kuchokera kuphompho la kusagwira ntchito konga imfa. Kaamba ka chifuno chotani?

Eya, podzafika mapeto a zaka chikwi, ambiri a okhala m’Paradaiso adzakhala oukitsidwa amene chikhulupiriro chawo sichinayesedwe konse. Asanafe, sanadziŵe konse malonjezo a Mulungu ndipo motero sakanasonyeza chikhulupiriro kumalonjezowo. Pamenepo, ataukitsidwa ndi kuphunzitsidwa chowonadi cha Baibulo, kunali kosavuta kwa iwo, popanda chitsutso chirichonse, kutumikira Mulungu m’Paradaiso. Koma ngati Satana anapatsidwa mpata wa kuyesa kuwalepheretsa kupitiriza kutumikira Mulungu, kodi iwo akatsimikizira kukhulupirika poyesedwa? Kuti funsolo liyankhidwe, Satana adzamasulidwa.

Vumbulutso loperekedwa kwa Yohane limavumbula kuti Ulamuliro Wazaka Chikwi wa Yesu utatha, Satana adzatsimikizira kukhala wachipambano kupatutsa chiŵerengero chosadziŵika cha anthu kuchoka pakutumikira Mulungu. Komano, pamene chiyeso chomalizira chitatha, Satana, ziŵanda zake, ndi onse amene iye adzakhoza kusocheza adzawonongedwa kosatha. Kumbali ina, opulumuka okhulupirika, oyesedwa kotheratuwo adzakhalabe ndi moyo kusangalala ndi madalitso a Atate wawo wakumwamba kuumuyaya wonse.

Mwachiwonekere, Yesu wachita, ndipo adzapitirizabe kuchita mbali yaikulu, m’kukwaniritsa zifuno zaulemerero za Mulungu. Ndimtsogolo mokondweretsa chotani nanga mmene tingakhale namo monga chotulukapo cha zonse zimene iye akukwaniritsa monga Mfumu yakumwamba yaikulu ya Mulungu. Komabe, sitingaiŵale zonse zimene anazichita pamene anali munthu.

Mofunitsitsa Yesu anadza kudziko lapansi natiphunzitsa za Atate wake. Kuwonjezera pamenepo iye anasonyeza mikhalidwe yamtengo wapatali ya Mulungu. Mitima yathu imasonkhezeredwa pamene tilingalira kulimba mtima kwake kwakukulu ndi uchamuna, nzeru zake zosayerekezeka, luso lake lopambana monga mphunzitsi, utsogoleri wake wopanda mantha, ndi chikondi chake chopanda mpeni kumphasa ndi chifundo. Pamene tikumbukira mmene anavutikira kwadzawoneni pamene anali kupereka dipo, kupyolera mwa limene tingapezere moyo, ndithudi mitima yathu imasonkhezeredwa kumuyamikira!

Ndithudi, ndimunthu wapadera chotani nanga amene tawona m’phunziroli la moyo wa Yesu! Ukulu wake ngwachiwonekere ndi wopambana. Timasonkhezeredwa kubwereza mawu a bwanamkubwa Wachiromayo Pontiyo Pilato akuti: “Tawonani munthuyu!” Inde, ndithudi, “Munthuyu,” munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako!

Mwakulandira kwathu makonzedwe a nsembe yake ya dipo, mtolo wa tchimo ndi imfa yolandiridwa kuchokera kwa Adamu zingachotsedwe pa ife, ndipo Yesu angakhale “Atate [wathu] Wosatha.” Onse amene akupeza moyo wosatha ayenera kuloŵetsa chidziŵitso osati cha Mulungu chabe komanso cha Mwana wake, Yesu Kristu. Kuŵerenga kwanu ndi kuphunzira bukhu lino kukuthandizenitu kuloŵetsa chidziŵitso chopatsa moyo choterocho! 1 Yohane 2:17; 1:7; Yohane 5:28, 29; 3:16; 17:3; 19:5; Luka 23:43; Genesis 1:28; 1 Akorinto 15:24-28; Chivumbulutso 20:1-3, 6-10; 21:3, 4; Yesaya 9:6.

▪ Kodi nchiyani chimene chidzakhala mwaŵi wosangalatsa wa opulumuka Armagedo ndi ana awo?

▪ Kodi ndani amene adzasangalala ndi Paradaiso kuwonjezera pa opulumuka Armagedo ndi ana awo, ndipo ndim’lingaliro lotani limene Yesu adzakhala nawo?

▪ Kodi mkhalidwe udzakhala wotani pamapeto a zaka chikwi, ndipo nchiyani chimene Yesu adzachita panthaŵiyo?

▪ Kodi nchifukwa ninji Satana adzamasulidwa kuchokera kuphompho, ndipo nchiyani chimene chidzamchitikira ndi onse omtsatira potsirizira pake?

▪ Kodi Yesu angakhale motani “Atate [wathu] Wosatha”?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena