Nyimbo 24
‘Sitiri a Dziko Lapansi’
1. M’lungu anatipatula,
Timpatsatu mtima wathu.
Sitiri mbali ya dziko;
Monga Kristu, timasankha.
2. Tipeŵe njira zadziko,
Tichite ntchito ya M’lungu.
Tipeŵe zinthu zathupi
Kuti tikhale ndi moyo.
3. Oyanjana ndi Mulungu,
Adzadedwa ndi dzikoli.
Tiyembekeza chizunzo,
Koma M’lungu ateteza.
4. Chotero timalimbika.
Mbuye anatipemphera:
‘Asamalireni ndithu.’
Ndipo atisamalira.