Nyimbo 74
Yehova, Wopereka Populumukira
1. M’tsiku lathu ulosi ukukwanira.
Satanayo wagwa; tsokadi padziko.
Mulungu wakhazika Yesu Mfumu. Tiimba:
‘Ya apulumutsa’ (indedi).
(Korasi)
2. Kukhulupirika kwathu kuyesedwa;
Mzimu wa dzikoli umatiukira.
Kuganiza kukhale koyeradi, tilimbe,
Ndi kupulumuka (o eya).
(Korasi)
3. Yesu adzaphwanya Satana pa Nkhondo,
Kulira ndi imfa sizidzakhalako.
Mmwamba dziko zikhala zatsopano, adziŵa
Tapulumutsidwa (ndithudi).
(KORASI)
Yehova apereka pothaŵira.
Adani azadziŵa kuti Ya ndi Thanthwe.
Molimbika, timtumikire, timtamanda
Yehovayo, Pothaŵirapo, Mtamandeni.