Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 10/1 tsamba 26-30
  • Kodi Mukuthandiza Mwana Wanu Kusankha Yehova?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukuthandiza Mwana Wanu Kusankha Yehova?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chimene Achichepere Ena Amasiyira Yehova
  • Yambani Msanga
  • Patsani Ana Anu Nthaŵi Yanu
  • Mayanjano Abwino ndi Chitsanzo Chabwino
  • Chimwemwe Poona Ana Akusankha Yehova
  • Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Phunzitsani Ana Anu kukonda Yehova
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Makolo Khalani Chitsanzo Chabwino kwa Ana Anu
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 10/1 tsamba 26-30

Kodi Mukuthandiza Mwana Wanu Kusankha Yehova?

“NDINAONA ngati kuti kuphunzira Baibulo kunalidi kogwetsa ulesi ndi kotopetsa. Mwamseri, ndinagamula mumtima mwanga kuti sindidzakhala mmodzi wa Mboni za Yehova nditakula,” anatero mnyamata wina. Ngakhale kuti tili ndi chiyembekezo chakuti unyinji wa ana m’mabanja Achikristu m’kupita kwa nthaŵi udzasankha kuima kumbali ya Yehova, achichepere monga mnyamatayo amavutika kwambiri kusankha Yehova monga Mulungu wawo.

Nthaŵi zina makolo samadziŵa bwino mmene angatsogolere ana awo mogwira mtima. Amaphanaphana ndi mtima, monga tate wina wodera nkhaŵa amene panthaŵi ina anati: “Kunena zoona, nthaŵi zina ndinkayang’ana nkhope za ana anga ali mtulo, misozi ikali m’masaya awo chifukwa chogwiritsidwa mwala, ndi kulingalira kuti bwenzi ndikanakhala wolekerera kwambiri.” Ana ake aamuna aŵiri anakula nasankha kutumikira Yehova.

Komabe pali achichepere ambiri amene amasiya Yehova nachoka m’gulu Lachikristu kuloŵa m’dziko la Satana. Chotero kodi makolo angakhoze motani kuthandiza ana awo kusankha Yehova? Kuti tiyankhe funso limenelo, choyamba tiyeni tipeze chifukwa chake achichepere ena amasiyira Yehova pamene makolo awo amafuna kwambiri kuti iwo akhale kwa iye.

Chifukwa Chimene Achichepere Ena Amasiyira Yehova

Chimodzi cha zochititsa zofala kwambiri nchakuti achichepere ena samafika pakudziŵadi Yehova kapena njira zake. Ngakhale kuti amapezeka pamisonkhano Yachikristu kuyambira ukhanda, iwo amangotero mwamwambo, ndipo samamfunafunadi Yehova. (Yesaya 55:6; Machitidwe 17:27) Mnyamata wotchulidwa pamwambapo anali kuipidwa ndi misonkhano Yachikristu chifukwa chakuti sanali kumvetsetsa zimene zinali kunenedwa ndi alankhuli pa pulatifomu.

Mbewu za choonadi zimabzalidwa mwa ena, koma iwo amalola mitima yawo kukopeka ndi kakhalidwe kosasamala ndi kokondetsa zinthu zakuthupi ka dziko la Satana. Ena sangathe kulimbana ndi chikhumbo champhamvu kwambiri cha kuyanjana ndi ausinkhu wawo ndi kukhala ofanana nawo.​—1 Mbiri 28:9; Luka 8:12-14; 1 Akorinto 15:33.

Komabe, padziko lonse ana ambiri m’mabanja Achikristu asankha kuima kumbali ya Yehova. Kodi tingaphunzirepo kanthu pa njira zabwino zimene makolo awo anatenga?

Yambani Msanga

Mfungulo yofunika kwambiri yothandizira ana anu kusankha Yehova ndiyo kuyamba msanga. Kaŵirikaŵiri, mikhalidwe yokhomerezedwa ndi maphunziro olandiridwa pamene mtima ukali wanthete ndi wogwira zinthu msanga zimakhala kwa moyo wonse. (Miyambo 22:6) Chotero yambani msanga kuuza ana anu za ubwino wa Yehova, chikondi chake ndi ukulu wake, mukumayesayesa kukulitsa kukonda Yehova m’mitima yawo ndi chiyamikiro cha zimene Yehova wawachitira. Kuti achite zimenezi, makolo ambiri agwiritsira ntchito mwachipambano nkhani zochuluka zonena za zimene Yehova analenga zopezeka m’zofalitsidwa za Watchtower Society.

Kumvera ndi kulemekeza Yehova ndi kulambira kwake zili pakati pa mikhalidwe ina imene iyenera kukhomerezedwa poyambirira m’moyo. Nkosangalatsa kuona ana amene sanayambebe kupita kusukulu akuyesayesa kulemba manotsi osacholoŵana pamisonkhano Yachikristu ndi kuona malemba m’Mabaibulo awo kapena akupita kunja ndi makolo awo kukasamba kumaso ndi madzi ozizira pamene awodzera. Zimenezi ndi zinthu zazing’ono, koma zili zofunika kwambiri chotani nanga pokhomereza m’maganizo a mwanayo kuti ulemu ndi kumvera ziyenera kusonyezedwa kwa Yehova!

Ndiponso malangizo a Baibulo ofunika kwambiri aumwini ayenera kuyamba kuperekedwa mwamsanga. Pamene ana awo aamuna anali ndi zaka ziŵiri, banja lina linayamba kuwaŵerengera buku la Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuruyo.a Pambuyo pake, pamene anyamatawo anayamba sukulu, ankadzuka mmamaŵa ndi kuphunzira ndi amayi awo m’mabuku a Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ndi Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi.* Zimenezi zinkatsatiridwa ndi kukambitsirana lemba la tsiku kochititsidwa ndi atate asanadye mfisulo. Zoyesayesa za makolowo zinadzetsa mfupo yaikulu pamene ana awo aamuna posachedwapa anasankha kutumikira Yehova, akumasonyeza kudzipatulira kwawo mwa ubatizo wa m’madzi pa usinkhu wa zaka 10 ndi 11.

Mnyamata wina wabwino amene akutumikira pa ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society ku Japan anakumbukira kuti pamene anali mwana, amayi ake anamthandiza kukulitsa unansi ndi Yehova mwa kukhala pambali pake usiku, akumamphunzitsa kupemphera. Sanaiŵale phunziro limene anaphunzira​—mosasamala kanthu za kumene anali kapena zimene anachita, Yehova nthaŵi zonse anali pafupi naye, wokonzekera kumthandiza.

Makolo achipambano amaphunzira kuzindikira zikhoterero zoipa zimene ana awo ali nazo chifukwa cha kupanda ungwiro kwa choloŵa, ndipo makolowo amayamba msanga kuthandiza ana awo kuwongolera zimenezi. (Miyambo 22:15) Zikhoterero kulinga ku dyera, liuma, kunyada, kusuliza ena mopambanitsa, ziyenera kuwongoleredwa pachiyambi penipeni. Ngati sichoncho, mbewu zotero zidzakula kufikira pa kupandukira Mulungu ndi njira zake pambuyo pake. Mwachitsanzo, makolo okhala ndi cholinga chabwino koma olekerera kwambiri kaŵirikaŵiri amalola ana awo kukulitsa mikhalidwe ya kudzikonda. Ana ameneŵa amaona kulemekeza makolo awo kapena Yehova kukhala kovuta, akumakhala ngati ‘osayamikira’ otchulidwa m’Baibulo. (Miyambo 29:21, NW) Komanso, ana amene amapatsidwa ntchito zapanyumba ndi amene amaphunzitsidwa kulingalira zosoŵa za ena amakhala ndi chizoloŵezi cha kuyamikira kwambiri makolo ndi Yehova yemwe.

Chofunika china ndicho kuyamba msanga kukhazikitsa zonulirapo zateokratiki zimene mwana angazifikire moyenerera. Ngati zimenezi sizichitidwa poyamba kapena nthaŵi zonse, ena angadzaze zonulirapo zosiyana m’maganizo mwake ndi mumtima mwake. Kuŵerenga Baibulo lonse, kuphunzira mwaumwini chimodzi cha zofalitsidwa za Watchtower Society, kulembetsa Sukulu Yautumiki Wateokratiki, kukhala mlengezi wa mbiri yabwino, ndi kubatizidwa ziyenera kuphatikizidwa pa zonulirapo zimenezi.

Takafumi akukumbukira kuti amayi ake anamphunzitsa chizoloŵezi cha kuŵerenga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! mwa kumlembera mafunso osavuta ndi kuwasiya pa thebulo la m’khichini kuti iye awapeze atabwera kunyumba kuchokera kusukulu. Yuri amakumbukira kuti kukhala masiku angapo ndi apainiyab otumikira kumene kunali kusoŵa kokulira kwa atumiki Achikristu, kupita nawo muutumiki, kuwapenyerera akuphika chakudya chokoma, ndi kuona chimwemwe ndi changu chawo kunasonkhezera kwambiri chikhumbo chake cha kutumikira Yehova mwanjira yofananayo. Achichepere ambiri amasimba kuti makolo awo ankapita nawo ku Beteli nthaŵi zambiri, monga mmene malikulu ndi nthambi za Watch Tower Society zimatchedwera, kumene ankaona anyamata ndi atsikana ena akutumikira Yehova mokondwa. Ambiri mwa awo amene ankachezera malowo akali ana tsopano akutumikira m’Mabeteli padziko lonse.

Patsani Ana Anu Nthaŵi Yanu

Kuchuluka ndi mkhalidwe wa nthaŵi imene mumathera ndi ana anu mosakayikira zidzakhala ndi chiyambukiro chachindunji ponena zakuti kaya iwo adzasankha kutumikira Yehova kapena ayi. Iwo amadziŵa msanga kuchuluka kwa nthaŵi imene mumathera nawo pochita phunziro la Baibulo ndi mmene mumalikonzekerera. Ngati simungakumbukire pamene munaimira paphunziro lapapitapo kapena ngati simuchita phunzirolo pazifukwa zazing’ono, mukupereka uthenga wakuti phunzirolo nlosafunika kwambiri. Komabe, pamene iwo aona kuti makolo amadzimana chifukwa cha phunziro, akumalikonzekera bwino ndi kuchititsa phunzirolo mokhazikika zivute zitani, uthenga wosiyana kotheratu ndi zimenezo umaperekedwa. Ngakhale kuti sichofunikira, amayi ena amavala bwino pa phunziro la ana awo, monga momwe amachitira popita ku misonkhano kapena pochititsa phunziro la Baibulo ndi wachinansi. Chimene chimakhomerezedwa mwa anawo nchakuti kulambira Yehova nkofunika.

Nthaŵi yochuluka ndi kuyesayesa kwakukulu zidzafunikira kuti muchititse maphunziro a Baibulo a ana anu kukhala osangalatsa, ofika pamtima wawo. Makamaka ana ocheperapo amachita chidwi pamene aona zinthu zimene akuphunzira zikuseŵeredwa pamaso pawo. Mwachitsanzo, tate wina anathandiza ana ake kuyerekezera chiukiriro mwa kuseŵera nkhani ya m’Baibulo ya kuuka kwa Lazaro. Iye analoŵa m’kachipinda koikamo zovala ndiyeno natuluka monga Lazaro woukitsidwayo.​—Yohane 11:17-44.

Pamene anawo akuloŵa mu uchikulire, kumafunadi nthaŵi yochulukirapo ndi luso kulimbana ndi malingaliro ochuluka atsopano, zikayikiro, ndi nkhaŵa zimene amayang’anizana nazo. Nthaŵi yopatulidwa ndi makolo achikondi ndi ozindikira panyengo imeneyi ili yofunika kwambiri ngati ana ati akulitse chidaliro mwa Yehova. Tate wina wachipambano wa ana anayi anasimba kuti pamene ana ake anayang’anizana ndi zovuta zosiyanasiyana, iye ankafufuza ndi kukambitsirana nawo masiku onse nkhani zokhudza zimenezo za m’zofalitsidwa za Watchtower kufikira zovutazo zitalakidwa kotheratu.

Mayi wina amene ali mpainiya wotanganitsidwa wa ana aŵiri anaona kuti mwana wake wamkazi anali kudzipatula ndipo anasoŵa chimwemwe m’ntchito zateokratiki. Chotero mayiyo anayesayesa kumapezeka panyumba pamene mwanayo anaweruka kusukulu masana aliwonse, akumakambitsirana ndi mwana wamkaziyo pamene onsewo anali kumwa tiyi. Mwa kukambitsirana kwachikondi kwa mayi ndi mwana wake wamkazi, mtsikanayo analandira thandizo limene anafunikira. Tsopano, popeza anamaliza maphunziro a sukulu ya sekondale, iye wagwirizana ndi amayi ake muutumiki waupainiya.​—Miyambo 20:5.

Mayanjano Abwino ndi Chitsanzo Chabwino

Kuwonjezera pa kupereka nthaŵi yawo, makolo ayenera kupereka mayanjano oyenera kwa mbadwa zawo. Miyambo 13:20 imati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.”

Makolo ambiri achipambano amazindikira kuona kwa mwambi umenewo. Tate wina wa ana anayi akuti: “Pamene ndilingalira za kumbuyoku, ndimalingalira kuti anali mabwenzi a m’choonadi ochuluka a ana athu amene anathandizira kuwasonkhezera kutumikira Yehova. Ndinawalimbikitsa kukhala ndi mabwenzi m’mipingo ina limodzinso ndi mumpingo wathu ndi kusunga maubwenzi amenewo.” Mkulu wina Wachikristu amene watumikira pa Beteli kwa zaka zambiri anakumbukira motere: “Pamene ndinali wamng’ono, tinkakhala m’nyumba yaing’ono, koma inkaperekedwa nthaŵi zonse monga malo ogona woyang’anira dera. Ndiponso, apainiya apadera a mumpingo wathu ankadya nafe chakudya chamadzulo nthaŵi zambiri. Ankasamba kunyumba kwathu ndi kuyanjana nafe. Kumvetsera zokumana nazo zawo ndi kuona chimwemwe chawo kunandithandiza kukulitsa chiyamikiro kaamba ka utumiki wa nthaŵi yonse.”

Mayanjano abwino amathandiza awo amene ali ndi zovuta. Mayi wina amene mwana wake wamwamuna anali ndi vuto lalikulu anakambitsirana chothetsa nzerucho ndi woyang’anira woyendayenda wa Mboni za Yehova. Iye anapereka lingaliro lakuti mayiyo azipita ndi mnyamatayo muutumiki wakumunda. “Ngati mudzatero, mkhalidwe wake wauzimu ndi zothetsa nzeru zina zilizonse zidzawongokera,” woyang’anirayo anatero. Mayiyo akusimba kuti: “Mumpingo wathu munali makonzedwe a umboni wa madzulo, ndipo ana ambiri ausinkhu wopita kusukulu, apainiya okhazikika angapo achikulire, ndi mkulu mmodzi kapena kuposerapo anakhalamo ndi phande. Poyamba inali nkhondo kuchititsa mwana wanga wamwamunayo kutulukira mokhazikika, koma zimenezo sizinatenge nthaŵi yaitali pakuti iye nthaŵi zonse anabwera kunyumba ali wachimwemwe ndi wolimbikitsidwa kwambiri ndi mayanjano oyenera. Pamene anali kuphunzira pasukulu ya sekondale, anabatizidwa nayamba kutumikira monga mpainiya wothandiza mwezi uliwonse, ndipo pamene anamaliza maphunziro, anakhala mpainiya wokhazikika.” Mayanjano oyenera limodzinso ndi kuchita chifuniro cha Yehova zinadzetsa zotsatirapo zabwino.

Mwina kwanuko kungakhale kulibe achichepere amene angakhale ndi chisonkhezero choyenera pa mwana wanu, koma zimene achichepere ambiri amene anasankha kutumikira Yehova anena zimakhudza zitsanzo za makolo awo. Achichepere ambiri anakhumbira kuchita monga makolo awo ndipo anafuna kuwatsanzira. Yuri amakumbukira kuchereza alendo kwa amayi ake ndi mmene anasamalirira ena, kuwaimbira foni ndi kukonzera chakudya odwala. Tatsuo, wochokera m’banja la anyamata anayi, onse ali achikulire tsopano ndipo akutumikira Yehova, anati: “Amayi sankaphunzira nafe mokhazikika chifukwa chakuti Atate anali osakhulupirira ndipo amayi ankatsutsidwa kwambiri ndi achibale. Koma ndinasonkhezeredwa kwambiri pakuona kuchirikiza kwawo choonadi ndi chimwemwe chawo potumikira Yehova. Ndiponso anali kukonda kukhalabe maso kufikira mbandakucha kuti atithandize pa zothetsa nzeru zathu.” Mawu anzeru a makolo amakhala ndi mphamvu pamene achirikizidwa ndi ntchito zokhulupirika. Yoichiro anati ponena za makolo ake: “Sindikukumbukira kuti iwo ananenapo zoipa ponena za ena mumpingo; ndipo sanatilole anafe kuneneza ena pa zolakwa zawo.”​—Luka 6:40-42.

Chimwemwe Poona Ana Akusankha Yehova

Palibe njira yosavuta yothandizira ana anu kusankha Yehova. Padzakhala nyengo zodetsa nkhaŵa zochuluka. Koma atate wodera nkhaŵa wotchulidwa poyamba anati: “Monga makolo tinayesa nthaŵi zonse mokhulupirika kutsatira malingaliro operekedwa ndi gulu looneka la Yehova. Zimenezi zinathandiza kwambiri kulaka zothetsa nzeru.” Zoyesayesa zawo zinapambana.

Inde, mwa kuyesayesa kwanu kutsatira zitsogozo za Baibulo, kupatsa ana anu zifukwa zabwino zokondera Yehova, zochirikizidwa ndi chitsanzo chanu chokhulupirika ndi zoyesayesa zoona za kuthandiza, nanunso m’kupita kwa nthaŵi mungapeze kuti zoyesayesa zanu zapambana. Kodi mukumkumbukira mnyamata uja wotchulidwa poyamba, yemwe panthaŵi ina anatsimikiza kuti sakakhala mmodzi wa Mboni za Yehova? Eya, amayi ake atamthandiza mwachipambano kupyola m’zaka zake zovuta, iye anati: “Ndili wokondwa kuti iwo sanagonje!” Zofanana ndi zimenezo zingachitikire ana anu.​—Agalatiya 6:9.

[Mawu a M’munsi]

a Ofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

b Atumiki a nthaŵi yonse a Mboni za Yehova amatchedwa apainiya. Mpainiya wothandiza amathera maola osachepera pa 60 muutumiki mwezi uliwonse, mpainiya wokhazikika maola 90, ndi mpainiya wapadera maola 140.

[Chithunzi patsamba 30]

Kodi mungakumbukire mwachimwemwe zaka zanu za kulera ana pamene muyang’ana kumbuyo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena