Nyimbo 153
Yehova, Mulungu wa Chipulumutso Chathu
1. Mbuye Yehova wammwamba,
Tikhululukirenitu.
Tinabadwa mu uchimo
Tinalibechowonadi.
Chonde tipulumutseni
Timuke kudziko lanu.
Tiyanjanitsidwe nanu,
Tiimbe chipulumutso.
Tiimbe chipulumutso.
2. Tiri m’khola lanu Mbuye,
Monga nkhosa za Kristuzo.
Chipulumutso tipeza
Ife anthu osokera.
Mtendere mupereka kwa
Wodzichepetsa mitima.
Anzeru akuwopani;
Chipulumutso chafika.
Chipulumutso chafika.
3. Cho’nadicho chimakula!
Tikondwere ndi kufu’la.
Tikuwona zodabwitsa,
Mwana wanu alamula.
Ndiyo nthaŵi ya Ufumu,
Pomwe mtendere ukula.
Tilengeze dziko lonse.
Mwapatsa chipulumutso.
Mwapatsa chipulumutso.