Nyimbo 86
Kukulitsa Chipatso cha Chikondi
1. Mwa chikondi M’lungu apatsa
Kwa atumiki ake onse
Zochitira chifuniro
Chake chopatulikacho.
Ayamikira mzimuwo;
Amakulitsa mphatsozi;
Nasamala kopambana—
Mphatso ija ya chikondi.
2. Modekha tisonyezetunso
Mikhalidwe yautumiki;
Komabe timasumika
Kukwanitsa chofunika.
Ndi maganizo okhatu
Sitingadyetsetu nkhosa;
Tichite ndi mtima wonse
Kupeza nawo dalitso.
3. Tiyeni tisunge mwaphamphu
Chomangira cha mtenderecho.
Tidekhedi povutika;
Ndi kuthandizanso ena.
Ngakhale mu zochepazo
Tipezetu chikondwero;
Kukwaniritsa chikondi
Ndi kufanana ndi M’lungu.