Nyimbo 99
“Chifuno Chamuyaya” cha Mulungu Chovumbulutsidwa
1. Tiyenibe tigube,
Yense m’malo mwake.
Kwa atumiki padziko
Yehova waika.
Wadzetsa kulambira
Wanena zowona.
Khamulotu lawoneka
Limutumikira.
2. Mfumu yathu Yehova
Ndi wodalirika.
Mumdima wamaganizo,
Sitiyendamonso.
Chiri chifuno chake
Chodzetsa mtendere.
M’kulamulira kwa Kristu,
Adzathetsa nkhondo.
3. Povumbula chifuno
Tiyeseyesebe
Ndi kugubira kumoyo
Ndi kugalamuka.
Chifuno cha Yehova
Chidzapambanadi.
Mwanzeru timke mtsogolo
Ndi kumlemekeza.