-
Mmene Mungalinganizire Laibulale YateokratikiNsanja ya Olonda—1994 | November 1
-
-
Mmene Mungalinganizire Laibulale Yateokratiki
SHEREZADE, kamtsikana kanzeru Kachispanya, kanali ndi zaka zinayi pamene mphunzitsi wake anauza kalasi kuti iwo akajambula zithunzithunzi za “Father Christmas.” Nthaŵi yomweyo, Sherezade anapempha chilolezo cha kusatengamo mbali. Iye anafotokoza kuti chikumbumtima chake sichikamulola kuchita zimenezo.
Atadabwa ndi kukana kumeneku, mphunzitsiyo anamuuza kuti kunali kungofanana ndi kujambula chithunzithunzi cha chidole ndi kuti panalibe choipa ndi zimenezo. Sherezade anayankha kuti: “Ngati chili chidole chabe, ineyo ndidzajambula chidolecho ngati mungandilole.”
Panthaŵi ina kalasi linauzidwa kujambula mbendera ya dzikolo. Sherezade anapemphanso kuchita kanthu kena. Pofotokoza, anauza mphunzitsiyo nkhani ya Sadrake, Mesake, ndi Abedinego.—Danieli 3:1-28.
Sipanapite nthaŵi yaitali pamene mphunzitsiyo anaimbira foni amayi a Sherezade kuwauza za kudabwa kwake. “Nthaŵi zingapo mwana wanu wamkazi walankhula nane za chikumbumtima chake,” iye anatero. “Kodi mungakhulupirire zimenezo? Mtsikana wa usinkhu wakewo kundifotokozera chifukwa chimene chikumbumtima chake chikumvutira! Tamverani, sindikuvomereza zimene mukumphunzitsa, koma ndikutsimikizirani kuti mukupambana. Ndipo ndifuna kuti mudziŵe kuti ndikuchita naye kaso mwana wanu wamkazi.”
Kodi ndimotani mmene mtsikana wa zaka zinayi angapezere chikumbumtima chophunzitsidwa Baibulo? Amayi ake, a Marina, akufotokoza kuti Sherezade ali ndi laibulale yakeyake yateokratiki m’chipinda chake. Laibulaleyo imaphatikizapo makope ake aumwini a Nsanja ya Olonda, amene iye anachonga, mabuku ake olalikira nawo, ndi zofalitsidwa zonse za Watchtower Society zimene zatulutsidwa kuyambira pamene anabadwa. Chinthu chimene amakonda kwambiri m’laibulale yake ndicho matepi a My Book of Bible Stories, amene amamvetsera usiku uliwonse akumawatsatira mwa kuŵerenga buku lake. Nkhani za m’Baibulo zimenezi ndizo zimene zinamtheketsa kupanga zosankha zotchulidwa pamwambapa.
Kodi laibulale yateokratiki yolinganizidwa bwino ingathandize inuyo ndi ana anu? Kodi nchifukwa ninji laibulale ya m’nyumba ili yofunikira?
“Laibulale Sili Chokondweretsa Chabe”
“Laibulale sili chokondweretsa chabe, koma chimodzi cha zinthu zofunikira m’moyo,” anatero Henry Ward Beecher. Mosakayikira, pafupifupi tonsefe tili ndi chimodzi cha “zinthu zofunikira m’moyo” zimenezi, ngakhale kuti sitikudziŵa. Motani? Chifukwa chakuti ngakhale ngati tili ndi Baibulo lokha, tili ndi laibulale yamtundu winawake.
Baibulo lilidi laibulale yateokratiki yabwino koposa. M’zaka za zana lachinayi, Jerome anayambitsa mawu Achilatini akuti Bibliotheca Divina (Laibulale Yaumulungu) ofotokozera buku lonse la mabuku ouziridwa limene timatcha Baibulo. Yehova anatipatsa laibulale yopatulika imeneyi kuti itipatse chithandizo, malangizo ndi chitsogozo chogwira ntchito. Sitiyenera kuinyalanyaza. Kungokhala ndi Baibulo lathunthu kumatanthauza kuti tili ndi laibulale yaikulu kwambiri kuposa imene atumiki ochuluka a Mulungu anali nayo m’nthaŵi zakale.
Pamene kunali chabe malembo apamanja okwera mtengo, zili nyumba zoŵerengeka zimene zinali kukhala ndi Baibulo lonse ngati zinalipo nkomwe. Pamene Paulo anafuna kuphunzira Malemba pamene anali m’ndende kwa nthaŵi yomalizira m’Roma, anapempha Timoteo kumbweretsera mipukutu kuchokera ku Asia Minor—mwinamwake zigawo za Malemba Achihebri. (2 Timoteo 4:13) Komabe, m’masunagoge munali kusungidwa mipukutu, ndipo Yesu Kristu ndi mtumwi Paulo yemwe anagwiritsira ntchito malaibulale ameneŵa m’ntchito yawo yolalikira. (Luka 4:15-17; Machitidwe 17:1-3) Mwamwaŵi, Malemba tsopano amapezeka kwambiri kuposa mmene analili m’zaka za zana loyamba.
Chifukwa cha kupangidwa kwa makina osindikizira, lerolino pafupifupi atumiki onse a Mulungu—chilichonse chimene chingakhale chinenero chawo—akhoza kugula Baibulo lonse pamtengo wabwino. Tilinso ndi mpata wapadera wa kuwonjezera “laibulale” yopatulika imeneyi. Kwa zaka zoposa zana limodzi, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wakhala wotanganitsidwa kugaŵira chakudya chauzimu panthaŵi yake.—Mateyu 24:45-47.
Koma sitingakhoze kugwiritsira ntchito mokwanira chidziŵitso chamtengo wapatali chimenechi ngati sitilinganiza laibulale yaumwini yateokratiki. Kodi zimenezo zingachitidwe motani? Ndithudi, sitepe yoyamba ndiyo kugula mabuku amene laibulale yotero ifunikira. Kuyesayesa nkoyenera kwambiri popeza kuti kudzatikhozetsa kupeza mwamsanga chidziŵitso cholondola chofunikira kusamalira zovuta ndi kuyankhira mafunso a Baibulo.
Kodi ndi Mabuku Ati Amene Ndifunikira?
Kodi munaganizapo za mmene mungathetsere vuto la kulankhulana mu ukwati wanu kapena za mmene mungathandizire ana anu kukana anamgoneka? Kodi ndimotani mmene mungathandizire bwenzi limene likuvutika ndi kupsinjika maganizo? Kodi mungafotokoze bwino lomwe umboni umene tili nawo wakuti Mulungu aliko ndi chifukwa chimene amalolera kuipa? Kodi chilombo chofiiritsa cha m’Chivumbulutso chaputala 17 chimaimira chiyani?
Mafunso ameneŵa ndi ena ambiri angayankhidwe ngati muli ndi laibulale yokwanira yateokratiki. Watchtower Society yafalitsa mabuku, mabrosha, ndi nkhani za m’magazini zimene zimafotokoza nkhani zosiyanasiyana za Malemba. Ndiponso, mabuku ameneŵa amafotokoza za nkhani za banja, amaumba chikhulupiriro chathu mwa Mulungu ndi Baibulo, amatitheketsa kuwongolera maluso athu a kulalikira, ndipo amatithandiza kumvetsetsa maulosi a Baibulo.
Mabuku ochuluka osindikizidwa ndi Sosaite m’zaka 20 zapitazo akalipobe. Ngati mwangobwera kumene m’choonadi, kungakhale kopindulitsa kwa inu kugula mabuku onse otero amene alipo m’chinenero chanu. Mwina mabaundi voliyumu a The Watchtower a zaka zapita alipo m’chinenero chanu. Mabuku amaumboni apadera, onga ngati Insight on the Scriptures ndi Comprehensive Concordance, afalitsidwanso m’zinenero zosiyanasiyana. Komabe, kupeza mabuku ameneŵa kuli chabe sitepe yoyamba.
Linganizani Laibulale Yanu!
Kudziŵa kuti muli ndi buku kwina kwake kumasiyana ndi kupeza buku limene mukufuna. Ngati tingawononge nthaŵi yochuluka tikufunafuna buku lamaumboni, nkotheka kuti tidzachita ulesi pankhaniyo. Komabe, ngati mabuku athu ali olinganizidwa bwino, pamalo oyenera, tidzakonda kwambiri kufufuza kwaumwini.
Ngati nkotheka, kuli kothandiza kukhala ndi mabuku ochuluka ateokratiki pamalo amodzi. Mashelufu a mabuku angapangidwe, ndipo kaŵirikaŵiri pamtengo wotsika, ngati sitingakhoze kugula opangidwa kale, ndipo safunikira kutenga malo aakulu. Kupeza mabuku mosavuta pa laibulale nkofunikanso. Mabuku osungidwa pa tandala sathandiza kwambiri ndipo amangogwira fumbi.
Sitepe yotsatira ndiyo kulinganiza mabukuwo. Nthaŵi yochepa chabe yotheredwa pa kulinganiza mabuku kuwaika mwadongosolo imadzetsa mapindu.
Bwanji ngati ochuluka m’banja lanu sali Mboni za Yehova? Ngakhale kuti simungakhoze kulinganiza laibulale monga momwe mukanafunira, mungakhale ndi shelufu ya mabuku m’chipinda chanu imene ili ndi zofalitsidwa za Malemba.
Laibulale Yateokratiki Ingathandize Kuumba Mkhalidwe Wauzimu
Titalinganiza mabuku athu, tifunikira njira yotithandiza kupeza chidziŵitso. Timaiŵala, ndipo mwina sitingadziŵe mwachindunji zamkati mwa buku lililonse limene lili m’laibulale yathu yateokratiki. Chikhalirechobe, chidziŵitso chonse m’laibulale chikhoza kupezeka mwamsanga. Ngati ilimo m’chinenero chathu, Watch Tower Publications Index ingatitheketse kupeza chidziŵitso chakutichakuti m’nthaŵi yochepa chonena za pafupifupi nkhani iliyonse.
Julián, amene watumikira kwa zaka zambiri monga mpainiya wapadera ndi mkulu, akufotokoza kuti Index njofunika koposa pophunzitsa mwana wake wamng’ono pa onse kuchita phunziro laumwini. “Jairo, amene ali ndi zaka zisanu ndi ziŵiri, tsiku lina posachedwapa anafika panyumba kuchokera kusukulu nandifunsa kuti, ‘Atate, kodi nchiyani chimene Sosaite yanena ponena za ma dinosaur?’ Tinapita mu Index ndi kufuna liwulo ‘dinosaurs.’ Panthaŵi yomweyo tinapeza nkhani yapachikuto ya mu Galamukani! yonena za zimenezo. [February 8, 1990] Tsiku lomwelo, Jairo anayamba kuiŵerenga. Iye akudziŵa kale kuti laibulale yathu yateokratiki ili ndi chidziŵitso chothandiza pafupifupi pankhani iliyonse. Ine pandekha, ndikhulupirira kuti pamene ana athu aphunzira kugwiritsira ntchito bwino laibulale yateokratiki, imawathandiza kukula mwauzimu. Amadziŵa kulingalira bwino, ndiponso, amapeza kuti phunziro laumwini lingakhale losangalatsa.”
Fausto, atate ake Sherezade wotchulidwa poyamba, akhulupirira kuti muyenera kuyambirira kuphunzitsa ana kugwiritsira ntchito laibulale yateokratiki. “Tayamba kale kusonyeza Sherezade, amene tsopano ali ndi zaka zisanu ndi chimodzi, mmene angagwiritsirire ntchito Index,” iwo akufotokoza motero. “Popeza kuti amachita chidwi ndi chiyembekezo cha Paradaiso wa padziko lapansi, tinayamba mwa kumsonyeza liwulo ‘paradise’ mu Index ndiyeno kuyang’ana nkhani za mu Nsanja ya Olonda zotchulidwa. Kaŵirikaŵiri tinali kungomsonyeza zithunzithunzi. Komabe, mwa njira imeneyi iye anadziŵa kuti Index ndiyo mfungulo yopezera chidziŵitso m’laibulale ya m’nyumba mwathu. Tinadziŵa kuti iye anadziŵa zimenezo pamene tsiku lina anachokera kusukulu ndi funso lonena za mapwando a Isitala. ‘Kodi sitingagwiritsire ntchito Index kufufuzira zimenezi?’ iye anafunsa amayi ake.”
Mosasamala kanthu za usinkhu wathu, Baibulo limatilimbikitsa ‘kuyesa zonse; ndi kusunga chokomacho.’ (1 Atesalonika 5:21) Zimenezi zimafuna kuti tipende zimene Malemba amanena. (Machitidwe 17:11) Ngati tili ndi laibulale yateokratiki yolinganizidwa bwino, kufufuza koteroko kungakhale kokondweretsa. Nthaŵi iliyonse pamene tigwiritsira ntchito mwachipambano laibulale yathu pokonza nkhani, pofuna uphungu wothandiza wosamalirira vuto lina, kapena pofuna chidziŵitso chosangalatsa, phindu lenileni la laibulale yathu lidzakhomerezedwa mwa ife.
Makolo a Sherezade akunena kuti: “M’banja Lachikristu, laibulale yateokratiki sili chokondweretsa chabe ayi!”
[Bokosi patsamba 30]
KODI NDIMOTANI MMENE MUNGALINGANIZIRE MABUKU ANU?
Palibe malamulo olimba ponena za kulinganiza mabuku anu. Chikhalirechobe, zigawo zoyenera zotsatirazi zikusonyeza njira ina imene mungalinganizire mabuku anu malinga ndi zamkati mwake.
1. Mabuku amene amalongosola mbali zina za Baibulo vesi ndi vesi
(Zitsanzo: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, Revelation—Its Grand Climax At Hand!, “The Nations Shall Know That I Am Jehovah”—How?, “Your Will Be Done on Earth”)
2. Mabuku okhudza moyo wa banja
(Zitsanzo: Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe, Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo)
3. Mabaibulo ndi mabuku amaumboni
(Zitsanzo: New World Translation of the Holy Scriptures—With References, Mabaibulo ena, Watch Tower Publications Indexes, Comprehensive Concordance, Insight on the Scriptures, The Kingdom Interlinear Translation of the Greek Scriptures, dikishonale yabwino)
4. Mabuku amene tsopano akugwiritsiridwa ntchito pa Phunziro Labuku Lampingo ndi mu Sukulu Yautumiki Wateokratiki
5. Makaseti ndi mavidiyo
6. Mabaundi voliyumu a The Watchtower ndi Awake!
7. Mbiri ya Mboni za Yehova
(Zitsanzo: Yearbooks of Jehovah’s Witnesses, Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom)
8. Mabuku ndi mabrosha amene timagwiritsira ntchito nthaŵi ndi nthaŵi mu utumiki wathu
(Zitsanzo: Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, Kukambitsirana za m’Malemba, Mtendere Weniweni ndi Chisungiko Kodi Mungazipeze Motani? Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona)
[Chithunzi patsamba 31]
Sherezade ali kale wophunzira Baibulo wabwino
[Chithunzi patsamba 31]
Ngakhale kuti ali wamng’ono, mnyamatayu akugwiritsira ntchito laibulale yateokratiki
-
-
Chiŵalo China cha Bungwe LolamuliraNsanja ya Olonda—1994 | November 1
-
-
Chiŵalo China cha Bungwe Lolamulira
NDI cholinga cha kuwonjezera antchito m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, kuyambira pa July 1, 1994, chiŵalo china chawonjezedwa pa akulu 11 amene akutumikira tsopano lino. Chiŵalo chatsopanocho ndiye Gerrit Lösch.
Mbale Lösch analoŵa utumiki wanthaŵi yonse pa November 1, 1961, namaliza maphunziro m’kalasi ya 41 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower. Anatumikira m’ntchito yadera ndi ya chigawo ku Austria kuyambira 1963 mpaka 1976. Anakwatira mu 1967, ndipo iye ndi mkazi wake, Merete, pambuyo pake anatumikira kwa zaka 14 monga ziŵalo za banja la Beteli la ku Austria ku Vienna. Zaka zinayi zapitazo iwo anasamutsidwira ku malikulu a Sosaite ku Brooklyn, New York, kumene Mbale Lösch wakhala akutumikira m’Maofesi Oyang’anira ndipo monga wothandiza Komiti Yautumiki. Chifukwa cha kuzoloŵera kwake kwambiri munda wa ku Ulaya ndi kudziŵa kwake Chijeremani, Chingelezi, Chiromaniya, ndi Chitaliyana, iye adzathandiza kwambiri pantchito ya Bungwe Lolamulira.
-