Nyimbo 116
‘Muyenera Kuthandiza Ofookawo’
1. Zofooka nzambiri
Tiri nazodi.
Koma Yehova ndithu,
Atikondabe.
Iye ngwachifundo,
Timuyamikira.
Titsanze chikondicho,
Thandiza ena.
2. M’malo mwa kusuliza,
Tikumbukire
Ubwino upezedwa
Mwachifundocho.
Tikhale achangu,
Kuwalimbikitsa.
Powapatsa thandizo,
Atonthozedwa.
3. ‘Ndani wofo’ka nane?’
Ati Paulo.
Tilingalire ena,
Timve chisoni.
Kwa ’mphamvu tinena:
‘Mthandize ofo’ka.’
Anagudwa ndi Kristu,
Kupeza moyo.
4. Tithandize ofo’ka,
Ya amveketsa.
Powathandiza zedi,
Tidzadaladi.
Ali a Mulungu.
Akhale amphamvu.
Tikawathandizadi,
Tidzalimba nji.