Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 4/1 tsamba 21-26
  • Ziweruzo za Mulungu Ziyenera Kulengezedwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ziweruzo za Mulungu Ziyenera Kulengezedwa
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chisonkhezero ndi Chotulukapo
  • Yeremiya Wamakono Avumbula Chikristu cha Dziko
  • Chikristu cha Dziko Chogawanitsa Chichenjezedwa
  • Chikristu cha Dziko Chivulidwa
  • Ntchito ya Yeremiya Ikufika Kumapeto
  • Chikristu cha Dziko Chavumbulidwa Monga Chopititsa Patsogolo Kulambira Konyenga
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Yeremiya—Mneneri Wachilendo wa Ziweruzo za Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • “Sindingathe Kukhala Chete”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • “Tsopano Uwauze” Mawu Awa
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 4/1 tsamba 21-26

Ziweruzo za Mulungu Ziyenera Kulengezedwa

“Nuwuke nunene kwa iwo zonse zimene ndikuuza iwe. Usawope nkhope zawo.”​—YEREMIYA 1:17.

1. Ndimotani mmene Mboni za Yehova ‘zinalolela kuwala kwawo kuwala’ mu Nazi Germany?

“CHIZUNZO cha Mboni za Yehova mu Ufumu wodzetsa Chipiyoyo [Nazi Germany] chatenga malo ake pakati pa nthaŵi zina za chiyeso m’mbiri yawo.” (Holocaust Studies Annual, Volume II​—The Churches’ Response to the Holocaust), Daily News ya ku South Africa ya July 15, 1939, inalongosolanso ponena za Mboni za chiGerman: “Monga kuwala komwe sikunakhoze kuzimiririka, bungwe laling’ono la amuna ndi akazi Achikristu limeneli limaima molimbika m’chikhulupiriro chawo, monga minga m’mbali ya Ulamuliro wa Munich [Adolf Hitler] ndi umboni wamoyo ku kusafa kwake.” Mawu amenewo amatikumbutsa ife kuti Yesu ananena kuti otsatira ake “adzakhala kuwala kwa dziko lapansi” ndipo kuti adzayenera kuleka kuwala kwawo kuwalikira dziko lonse, mosasamala kanthu za mtengo.​—Mateyu 5:11, 12, 14-16.

2, 3. Ndi chitsanzo chiti cha kulalikira kopanda mantha chimene chinachitika mu Sri Lanka?

2 Ripoti lina, lochokera ku dziko logawanikana ndi uchigaŵenga la Sri Lanka, limalankhula za Mboni yachichepere ya chiTamil, David Gunaratnam, amene, mumkhalidwe wowona wa Yeremiya, analalikira mopanda mantha kwa olamulira a nkhondo. Iye anali atazingidwa ndi amuna ena achichepere kaamba ka kufunsidwa. Ripotilo likunena kuti: “Ndunazo ndi amunawo anadabwitsidwa ndi chidziŵitso cha mabukhu cha mwamunayo, ndipo kuposa chimenecho, ndi kuwona mtima kwake kowonekeratu, makamaka pamene iye ananena kuti, ‘Ndipo ngati ndinakumana ndi awo otchedwa zigaŵenga, ndikalalikira kwa iwo chinthu chimodzimodzichi.’”

3 Usiku umodzimodziwo iye anagwidwa kuchokera kunyumba kwake ndi zigaŵenga, zomwe zinamupatsa iye mlandu wa kulankhula ndi gulu la nkhondo. Iye anaumirira pa uchete wake ndi kunena kuti anali kokha kulalikira uthenga wa Ufumu wa Mulungu. “Ndikuchita ntchito ya Mulungu ndipo ndidzapitiriza kuichita iyo. Ndimalalikira mopanda kusankha kwa wina aliyense amene angandimvere.” Mboni yolimba mtima imeneyi inawomberedwa mfuti ndi kuphedwa ndi zigaŵengazo, ikumasiya kumbuyo mkazi wamasiye ndi mwana wamwamuna.​—Yerekezani ndi Machitidwe 7:51-60.

4. Ndi chizunzo chovomerezedwa ndi atsogoleri a chipembedzo chotani cha Mboni za Yehova chimene chinachitika m’dziko la Latin America?

4 Kuchokera ku dziko la Latin America, kumene chizunzo cha Mboni za Yehova chinavomerezedwa ndi kulekereredwa ndi atsogoleri ena a Chikatolika ndi a chiPresbyterian, kukubwera ripotili: “Munali Mboni za Yehova zisanu m’malo a nkhondo . . . Izo kaŵirikaŵiri zinali kumenyedwa ndi kuikidwa mopatulidwa popanda chakudya. Nduna ya ndale zadziko yoyang’anira za ziphunzitso m’gawo lathu inawalanga iwo chifukwa iwo analalikira kwa asilikari ena. Iye ananena kuti pa magulu onse a chipembedzo, Mboni za Yehova zinali zowopsya koposa.”

Chisonkhezero ndi Chotulukapo

5. Monga mmene zinaliri m’nkhani ya Yeremiya, nchiyani chimene kaŵirikaŵiri chimakhala kumbuyo kwa chizunzo cha Mboni?

5 Inde, monga mmene Yeremiya anazunzidwira ndi atsogoleri a chipembedzo ndi olamulira a ndale zadziko a m’tsiku lake, moteronso Mboni za Yehova zimayang’anizana ndi chitsutso m’dziko lonse kuchokera ku magwero ofananawo. Nchiyani chimene chimasonkhezera kachitidwe koteroko? Ngakhale kuti Mboni ziri gulu la mtendere koposa ndi losunga lamulo la mudzi uliwonse, adani awo amalingalira Mawu a Mulungu kukhala owopsya, popeza iwo amakana ndi kutsutsa uthenga wake wonena za Ufumu wa Mulungu. Kulalikira kwawo kosagonjera ndi malamulo awo amavumbulutsa dyera ndi kulowa m’malo kwa ndale zadziko, za chuma, ndi mbali za chipembedzo za dongosolo la Satana.​—Yohane 15:18, 19; 1 Yohane 5:19.

6. Ndimotani mmene Mboni za Yehova zavomerezera ku chizunzo?

6 Komabe, mosasamala kanthu za kuikidwa m’ndende, kumenyedwa, ndipo ngakhale imfa, Mboni za Yehova kuzungulira padziko lonse lapansi zimachita monga mmene anachitira Yeremiya wakale. Pamene zimasonyeza chikondi ndi luso, izo zimapitiriza kulalikira ziweruzo zachilendo za Mulungu kwa mitundu. (2 Timoteo 2:23-26) Izo zimadziŵa kuti ziyenera kumvera Mulungu monga Wolamulira kuposa anthu. (Machitidwe 4:19, 20; 5:29) Izo zimazindikira uphungu wa Paulo kwa Akristu a Chihebri, wotchedwa, kupirira m’kuchita chifuno cha Mulungu. Kenaka izo zidzawona kukwaniritsidwa kwa lonjezo, moyo wosatha. Chotero, mofanana ndi Paulo ndi Yeremiya, tiyenera kukhala okhoza kunena kuti: “Koma ife sindife a iwo akubwerera kulowa chitaiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.”​—Ahebri 10:35-39.

Yeremiya Wamakono Avumbula Chikristu cha Dziko

7. Ndimotani mmene Mboni m’zana lino la 20 zatsatirira chitsanzo cha aneneri okhulupirika a Yehova otumizidwa kwa Israyeli ndi Yuda?

7 Monga mmene Yehova anapitirizira kutumiza aneneri ake ku Israyeli ndi Yuda, iye watumiza mboni zake kuti zigogomezere pa uthenga wa chiweruzo chake chomadzacho. (Yeremiya 7:25, 26; 25:4, 8, 9) Makamaka kuyambira chaka chopatsa mphamvu mwauzimu cha 1919, otsalira odzozedwa a abale a Kristu mopanda mantha apereka ziweruzo za Mulungu, uthenga wamphamvu wa tsoka, kwa Chikristu cha Dziko. (Yerekezani ndi Yeremiya 11:9-13.) Mu chaka chimenecho magazini ya The Golden Age inatulutsidwa. Mkati mwa zaka ndi kusintha kwa mitu yake, Consolation (1937) ndi Galamukani! (1946), yatumikira kuvumbulutsa mabodza a chipembedzo a Chikristu cha Dziko ndi Chikristu chake chonyengezera.

8, 9. (a) Nchifukwa ninji matchalitchi anatsutsidwa mu 1922? (b) Ndi tsoka lotani limene linanenedweratu kaamba ka iwo?

8 Mwachitsanzo, Golden Age ya October 11, 1922, inatsutsa chipembedzo chonyenga m’mawu awa: “Zoyesayesa zonse za magulu a tchalitchi a zipembedzo, atsogoleri awo a chipembedzo, atsogoleri awo ndi othandizana nawo awo, za kusunga ndi kukhazikitsanso dongosolo la zinthu m’dziko lapansi . . . motsimikizirika ziyenera kulephera, chifukwa izo sizipanga mbali iriyonse ya ufumu wa Mesiya. Kuti mosiyanako, mkati mwa Nkhondo ya Dziko [I] atsogoleri a chipembedzo a matchalitchi a chipembedzo osiyanasiyana amenewa anali osakhulupirika kwa Ambuye Yesu Kristu mu ichi, kuti iwo molakwika anagwirizana ndi mabizinesi a akulu ndi a ndale zadziko a akulu kuti apititse patsogolo Nkhondo ya Dziko.”

9 Chitsutso chinapitiriza: “Iwo mowonjezereka anakana kuzindikira Ambuye ndi ufumu wake ndi kusonyeza kusakhulupirika kwawo mwa kudzigwirizanitsa iwo eni modzipereka ndi gulu la Satana ndipo molimba mtima kulengeza ku dziko kuti Chigwirizano cha Mitundu chiri chisonyezero cha ndale zadziko cha ufumu wa Mulungu padziko lapansi.” Pomalizira panabwera uthenga wa “tsoka,” kapena chiweruzo: “Tsopano chikuyandikira ndipo chiri pafupi kugwera mitundu ya dziko lapansi, mogwirizana ndi mawu a Kristu Yesu, nthaŵi yaikulu ya ‘chisautso chonga sichinakhalepo kuyambira chiyambi cha dziko kufikira tsopano, ayi, ndipo sichidzakhalanso.’”

10. Ndi chitsutso chotani chimene chinapangidwa mu 1926?

10 Ntchito ya Yeremiya inafutukulidwa kupyolera m’kugwiritsira ntchito zofalitsidwa zina, monga ngati magazini ya Nsanja ya Olonda, timabukhu, ndi mabukhu. Mwachitsanzo, mu 1926 bukhu la Deliverance linaphatikiza kuvumbulutsa kwamphamvu kwa ziphunzitso zosokeretsa za Chikristu cha Dziko. Pa tsamba 203 ilo linanena kuti: “Ziphunzitso zonyenga zinayambitsidwa mwaufulu [mu Chikristu cha Dziko cha mpatuko] ndipo zinalowa m’malo chowonadi. Pakati pa izi panali ndipo pali ziphunzitso za utatu, kusafa kwa miyoyo yonse, chizunzo chosatha cha oipa, ndi kuyenera kwaumulungu kwa atsogoleri a chipembedzo ndi kuyenera kwaumulungu kwa mafumu kulamulira. M’kupita kwanthaŵi Mariya, mayi wa mwana Yesu, anasonyezedwa kukhala monga mulungu; ndipo anthu anaitanira pa iye m’kulambira monga mayi wa Mulungu.”

Chikristu cha Dziko Chogawanitsa Chichenjezedwa

11, 12. (a) Ndimotani mmene kaimidwe kosakhala kauchete ka atsogoleri a chipembedzo kavumbulutsidwira? (b) Ndi chenjezo lotani limene linaperekedwa ndi gulu la Yeremiya?

11 Chofalitsidwa chimodzimodzicho chinavumbulutsa kutenga mbali koipa m’nkhondo kwa atsogoleri a chipembedzo, chikumanena kuti: “Atsogoleri a chipembedzo a madongosolo osiyanasiyana a alengezi amadalitsa magulu ankhondo omwe amatumizidwa ndi mbali za chuma ndi ndale zadziko, ndipo dalitso lawo likufutukulidwa mosasamala kanthu kuti ndi mbali iti imene magulu ankhondo amenewa akumenyana nayo. Atsogoleri a chipembedzo onse amanyengezera kupemphera kwa Mulungu mmodzimodziyo kaamba ka dalitso pa magulu ankhondo omenyanawo a mbali zonse ziŵiri.” (Yerekezani ndi Yeremiya 7:31.) Kenaka chiweruzo chotsimikizirika chinaperekedwa: “Zinthu zonsezi zomwe zimapita kupanga mbali yowonekera ya gulu la Satana zikusonkhanitsidwa pamodzi ndi kusonkhanitsidwa kaamba ka nkhondo yaikulu ya Armagedo.”​—Chivumbulutso 16:14-16.

12 Monga mmene zinaliri m’tsiku la Yeremiya, pamene atsogoleri ananena kuti iwo anali achisungiko ndipo anali pa mtendere ndi Mulungu, “moteronso atsogoleri a alaliki amenewa amadzinenera iwo eni kuti ali osungika, kuti amangofunikira kokha kutchulidwa ndi dzina la Kristu, pamene akupitiriza kuseŵera ndi moto wa Mdyerekezi. Iwo amadzichititsa khungu iwo eni ku mkhalidwe weniweni mwakuika mchenga m’maso mwawo limodzinso ndi m’maso mwa anthu anzawo.” (Deliverance, tsamba 270) Kudzinyenga kwawo kunavumbulutsidwa ndi Ophunzira Baibulo achangu amenewo, monga mmene Mboni za Yehova zinali kudziŵikira panthaŵiyo.​—Mateyu 7:21-23.

13. Ndi chochitika chotani chimene chinachitika mu 1931, ndipo nchifukwa ninji chinali choyenerera?

13 Pamene nthaŵi inapita, Ophunzira Baibulo anakhala ozindikirika kwenikweni ndi Yeremiya pamene, mu 1931, pa msonkhano mu Columbus, Ohio, U.S.A., chinalengezedwa kuti dzina la m’Baibulo kaamba ka gulu lolimba mtima la Akristu limeneli liyenera kukhala “Mboni za Yehova.” (Yesaya 43:10-12) Dzina limenelo linabweretsedwa kutsogolo m’zana la chisanu ndi chitatu B.C.E. pamene Yehova analigwiritsira ntchito ilo kwa Israyeli. Chotero, chifupifupi zaka zana limodzi pambuyo pake, pamene Yeremiya anatumikira monga mneneri, iye analinso mboni kaamba ka Yehova. (Yeremiya 16:21) Mofananamo Yesu, pamene anabwera ku dziko lapansi monga m’Yuda, anali mboni kaamba ka Atate wake, Yehova. (Yohane 17:25, 26; Chivumbulutso 1:5; 3:14) Chotero, chinali choyenera kuti panthaŵi yoikika ya Mulungu, anthu ake ayenera pomalizira kuyeneretsedwa kaamba ka dzina loikidwa mwaumulungu limeneli​—“Mboni za Yehova.”​—Yohane 17:6, 11, 12.

Chikristu cha Dziko Chivulidwa

14. Ndimotani mmene Chikristu cha Dziko chavumbulutsidwira mkati mwa zaka 70 zapita?

14 Mkati mwa zaka makumi asanu ndi aŵiri zomalizira, m’chigwirizano ndi kulengeza chiyembekezo chowala cha kudza kwa Ufumu wa Yehova, Mboni za Yehova zafalitsa kuzungulira padziko chitsutso chowona chokulira ndi chiweruzo. Mu mazana a mamiliyoni, a zofalitsidwa zowona zachindunji zozikidwa pa Baibulo iwo avumbulutsa Chikristu cha Dziko monga magwero a mphamvu kwambiri m’mbali ya chipembedzo, “Babulo Wamkulu,” wolengezedwa mu Chivumbulutso mitu 17 ndi 18. (Onani “Babylon the Great Has Fallen!” God’s Kingdom Rules!, masamba 576-615, lofalitsidwa mu 1963 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.)

15. Ndimotani mmene Chikristu cha Dziko chinavumbulidwira mu 1955?

15 Mu 1955 Mboni za Yehova zinagawira mamiliyoni a makope a kabukhu kakuti Christendom or Christianity​—Which One Is “the Light of the World”? Zikwi zambiri zinagawiridwa mwachindunji kwa atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko. Ndipo nchiyani chimene kabukhuko kanawauza iwo? Mumkhalidwe wowona wa Yeremiya, kananena kuti: “Mosasamala kanthu za mwaŵi wake wonse umene wamukankhira iye kutsogolo mwachuma, mwamalingaliro ndi mwankhondo, Chikristu cha Dziko sichinadzitsimikizire icho cheni ‘kukhala kuwunika kwa dziko.’ Chifukwa ninji ayi? . . . Icho sichilalikira kapena kuchita Chikristu cha [Baibulo].” Kenaka iko kanadzutsa funso: “Kodi kuvumbulutsa zipembedzo zonyenga kuli chizunzo kwa atsatiri ake? Kodi iko kuli malingaliro aumwini opanda Chikristu?”

16. Kodi kunali kukondetsa chikhulupiriro chawo kwa Mboni kuvumbula Chikristu cha Dziko? Longosolani.

16 Yankho linali: “Ayi; zikadakhala tero, Yesu Kristu akadakhala wozunza wodziŵa zake wa Ayuda, . . . ndipo onse a aneneri a Yehova a nthaŵi zakale [kuphatikizapo Yeremiya] asanabwere Yesu akadakhala azunzi ndipo okonda chipembedzo chawo, popeza onsewo anavumbulutsa chipembedzo chonyenga cha Ayuda ampatuko ndi mitundu ya chikunja.” Ndithudi, ngati Akristu owona ayenera kukhala “kuwunika kwa dziko,” chotero “mdima” wauzimu uyenera kuvumbulutsidwa. (2 Akorinto 6:14-17) Ichi sichimatanthauza kuti munthu aliyense payekha amawukiridwa koma, m’malomwake, ndi dongosolo limene limawaika iwo mu ukapolo. Chotero, Yehova anapereka lamulo kwa Yeremiya: “Koma iwe ukwinde m’chuwuno mwako, nuuke, nunene kwa iwo zonse zimene ndikuuza iwe. Usawope nkhope zawo . . . Ndipo adzamenyana ndi iwe, koma sadzakuposa, chifukwa ‘Ine ndiri ndi iwe,’ ati Yehova, ‘kukulanditsa.’”​—Yeremiya 1:17, 19.

Ntchito ya Yeremiya Ikufika Kumapeto

17, 18. (a) Ndimotani mmene Mboni za Yehova zapitirizira ntchito yawo ya Yeremiya mu zaka zaposachedwapa? (b) Ndi uphungu wotani umene waperekedwa kwa owona mtima?

17 Kodi Mboni za Yehova zatsitsa pansi chiweruzo cha Mulungu? Zowona, tikukhala m’mbadwo umene kusuliza chipembedzo china sikulingaliridwa kukhala chinthu choyenera kuchichita. Mosasamala kanthu za chimenecho, zofalitsidwa za Mboni za Yehova zikupereka uthenga umodzimodziwo wa chiweruzo kaamba ka Chikristu cha Dziko monga mwa nthaŵi zonse. Mwachitsanzo, zaka zinayi zapita Mboni za Yehova zasindikiza makope 32 miliyoni a bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, mu zinenero 76. Chofalitsidwa chimenechi chimapereka mayankho ku mafunso ambiri aposachedwapa, monga ngati “Kodi Chimachitika Nchiyani pa Imfa?” “Kodi Nchifukwa Ninji Mulungu Walola Kuipa?” ndi “Kudziŵa Chipembedzo Chowona.” Koma limaperekanso chenjezo lomvekera ponena za ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga.

18 Mu mutu 25, wokhala ndi mutu wakuti “Kodi Mukuchirikiza Dziko la Satana, kapena Dongosolo Latsopano la Mulungu?” limanena kuti: “M’Baibulo chipembedzo chonyenga chikuphiphiritsiridwa kukhala ‘mkazi wachigololo wamkulu,’ kapena wadama, ndi dzinalo ‘Babulo Wamkulu.’ . . . Ndipo nkotsimikizirika kuti mkati mwa mbiri yonse chipembedzo chaphatikizidwa ndi ndale zadziko, kaŵirikaŵiri chikumauza maboma chochita.” Chotero, ndi kachitidwe kotani kamene bukhulo likuyamikira? Ilo likufunsa: “Kodi mukufuna kukhala mbali ya dziko la Satana? Kapena kodi mukuchirikiza dongosolo latsopano la Mulungu? Ngati mukuchirikiza dongosolo latsopano la Mulungu, mudzakhala olekana ndi dziko, kuphatikizapo chipembedzo chake chonyenga. Mudzamvera lamulolo: ‘Tulukani m’menemo [Babulo Wamkulu], anthu anga.’ (Chivumbulutso 18:4)”

19. Ndimotani mmene mungasonyezere kuti liwu la Yeremiya wamakono liri losaletsedwa pa nthaŵi ino?

19 Uthenga wamphamvu umodzimodziwo wa kulekanitsa ndi chiweruzo umalira momvekera mu bukhu la Worldwide Security Under the “Prince of Peace,” lofalitsidwa mu 1986 (makope mamiliyoni asanu ndi limodzi mu zinenero 25). Ilo limavumbulutsa atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko kaamba ka ‘kulalikira amuna achichepere kuwalola m’mabwalo ankhondo’ a Nkhondo ya Dziko I. Ilo likupitiriza: “Chikristu cha Dziko chikupitirizabe monga mdani wa Mulungu Wam’mwambamwamba kufikira ku nthaŵi ino. Motsimikizirika iye alibe chinjirizo laumulungu, ndipo kaamba ka chifukwa chachikulu ichi kukhalapo kwake kukupitirizabe kukhala kopanda chisungiko.” (Onani masamba 30-2.) Liwu la Yeremiya wamakono siliri losamvedwa! Pamene kuli kwakuti zoyesayesa zikupangidwa ndi atsogoleri a chipembedzo ndi andale zadziko kuletsa kulalikira kwa ziweruzo za Mulungu, mboni zake zokhulupirika zikupitabe patsogolo, zogamulapo kumaliza ntchito yochenjeza.​—Yeremiya 18:18.

20. Nchifukwa ninji Mboni za Yehova zidzapitiriza kulengeza ziweruzo za Yehova kwa mitundu?

20 Ndipo nchifukwa ninji ntchito imeneyi iyenera kutsirizidwa? Chifukwa Yehova, Mfumu yamoyo Ambuye wa chilengedwe, ali ndi kuŵerengera ndi mitundu ndi zipembedzo zawo. Monga mmene Yehova anafunsira Yuda ndi Yerusalemu wonyenga, mofananamo funsolo limagwiranso ntchito ku Chikristu cha Dziko lerolino: “‘Kodi sindidzawalanga chifukwa cha zimenezi?’ ati Yehova. ‘Kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu woterewu?’” Chotero, Mboni za Yehova zidzapitiriza kuchezera anthu a mitundu yonse ndi uthenga umene umaluma unyinji monga chiweruzo chachilendo koma uli mbiri yabwino ya chimwemwe kwa ochepera​—mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu.​—Yeremiya 5:9, 29; 9:9; Machitidwe 8:4, 12.

21. Mosasamala kanthu za tsoka lonenedweratu, kodi ndi chiyembekezo chachikulu chotani chimene chiri kutsogolo kwa awo omapereka labadiro ku ntchito ya Yeremiya? (Masalmo 37:9, 11, 18, 19, 28, 29)

21 Pamene kuli kwakuti Yeremiya kaŵirikaŵiri anatchedwa wofuula tsoka, komabe chirinso chowona kuti uthenga wake unapereka cheza cha chiyembekezo kwa Ayuda. (Yeremiya 23:5, 6; 31:16, 17) M’njira yofananayo, pamene Mboni za Yehova zikulengeza “chisautso chachikulu” choyandikira, ndi chiweruzo cha Armagedo cha Mulungu, iwo akulengezanso madalitso a “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano” zomwe zidzatulukamo m’kubwezeretsedwa kwa chilungamo ndi Paradaiso ku pulaneti iri, limodzi ndi moyo wosatha. (Mateyu 24:21, 22; Chivumbulutso 16:16; 21:1-4) Chotero, tsopano iri nthaŵi ya kulabadira uthenga wa chiweruzo wa Yehova ndi kupereka chirikizo ku kumalizidwa kwa ntchito ya Yeremiya wamkulu.​—Yerekezani ndi Yeremiya 38:7-13.

Kodi Mumakumbukira?

◻ Mofanana ndi Yeremiya, ndimotani mmene Mboni za Yehova zikuzunzidwira?

◻ Nchifukwa ninji Mboni zimaumirira m’kulalikira?

◻ Ndimotani mmene ntchito ya Yeremiya yafutukulidwira?

◻ Ndi zitsanzo zaposachedwapa zotani zimene zimasonyeza kuti chitsutsocho sichinasinthe?

◻ Mosasamala kanthu za uthenga wa tsoka, ndi chiyembekezo chotani chimene chikuperekedwanso?

[Chithunzi patsamba 23]

Mkupita kwa nthaŵi, Mariya . . . anasonyezedwa monga mulungu ndipo anthu anaitanidwa kudzamlemekeza iye monga “Amayi wa Mulungu”

[Chithunzi patsamba 24]

Mu 1931 Ophunzira Baibulo analandira dzina lakuti “Mboni za Yehova” pa msonkhano wawo mu Columbus, Ohio

[Zithunzi patsamba 25]

Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse lapansi zikutsatira chitsanzo cha Yeremiya

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena