Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 9/1 tsamba 32
  • “Chiyembekezo cha Dziko Labwinopo”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Chiyembekezo cha Dziko Labwinopo”
  • Nsanja ya Olonda—1989
Nsanja ya Olonda—1989
w89 9/1 tsamba 32

“Chiyembekezo cha Dziko Labwinopo”

Pamene anali kuchezera Montreal mu July 1985, Gilles Le Sieur mosazindikira anasiya briefcase yake m’sitima ya kumaloko. Pambuyo pa tsiku limodzi atabwerera kunyumba, makilomita 260 kuchokera ku Montreal, iye analandira foni kuchokera kwa mkazi wachichepere yemwe anapeza cholacho. Gilles ndi mkazi wake anabwerera ku Montreal kukachitenga icho. Pamene iwo anatero, anapatsa bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi kwa mkazi wachichepereyo. Chifupifupi milungu iŵiri pambuyo pake, iwo analandira kalata ya chiyamikiro kuchokera kwa iye, imene m’mawu ochepera ikunena kuti:

“Sindidziŵa ndi ndani wa ife amene anapereka utumiki wokulira kwa mnzake mlungu watha. Ngakhale kuti sindinayembekezere chirichonse mondibwezera, ndinasangalatsidwa ndi chiyamikiro chimene inu munasonyeza kwa ine. Ine mwapadera ndinayamikira chenicheni chakuti inu munafuna kugawana ndi ine magwero a chimwemwe chanu. . . . Ndamaliza kale kuŵerenga bukhu limene munandipatsa, ndipo pa nthaŵi imene mukuŵerenga kalatayi, mmodzi wa mabwenzi anga adzakhala akuliŵerenga ilo. Inu munali wolondola ponena za mapindu amene bukhuli limabweretsa. Silinandipatse kokha chiyembekezo cha dziko labwinopo koma linayankha mafunso ambiri amene chipembedzo changa sichinayankhepo konse. . . . Tsopano ndayambanso kuŵerenga Baibulo ndi chikhumbo chofuna kukhala ndi moyo wabwinopo.”

Mkazi wachichepere ameneyu anapitirizabe ndi phunziro lake la Baibulo ndipo, m’kupita kwa nthaŵi, anakhala mtumiki wa nthaŵi zonse wa zinthu zabwino zimene anaphunzira. Bukhu lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi lakhala chiŵiya m’kusintha miyoyo ya anthu ambiri kaamba ka kukhala abwinopo. Bukhulo, la ukulu wa masamba wofanana ndi magazini ino, limakambitsirana mopindulitsa chiphunzitso chirichonse cha Baibulo ndipo liri ndi zithunzithunzi zophunzitsa zoposa 150. Kuti mulandire bukhu laphindu limeneli, tangodzazani ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.

Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu lachikuto cholimba, lamasamba 256 lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Ndatsekeramo K48 (Zambia).

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena