‘Iwo Ankaseka’
Mwamuna wina yemwe ankatumikira m’gulu lankhondo ku Hungary akunena kuti osati kale kwambiri anthu ankaseka awo amene ankalankhula za Baibulo. Koma zinthu zasintha. Posachedwapa msirikaliyo analembera ofesi ya Watch Tower Society ku Budapest, akumati:
“Masiku ochepa apitawo, ndinaŵerenga bukhu lanu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Munthu wina anandibwereka kufikira nditamaliza kuliŵerenga. Zimene zalembedwa m’bukhumo zandikhudza kwambiri ndipo zandipangitsa kulingalira.” Msirikaliyo anafuna Baibulo ndi mawu owonjezereka. Kachitidwe koteroko sikalinso kachilendo Kum’maŵa kwa Ulaya.
Kalata ina yolandiridwa ku ofesi ya Budapest ikuti: “Ndaŵerenga bukhu lanu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Bukhuli landisangalatsa kwambiri, ndipo ndikukulemberani kupempha kuti Mboni idzandichezere kunyumba kwanga kotero kuti ndikhale ndi phunziro Labaibulo lokhazikika.”
Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi ndi bukhu lomwe limapereka chiyembekezo mwakukusonyezani mayankho a Baibulo. Ilo lakhala chisonkhezero chabwino m’kusintha miyoyo yambiri. Ngati mungakonde kulandira kope, chonde dzazani ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
Ndingakonde kulandira bukhu lachikuto cholimba lamasamba 256 la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower yakwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani patsamba 2.)
[Chithunzi patsamba 32]
Ndi chifukwa chabwino, kholo lidzalola mwana wokondedwa kuchitidwa opareshoni yopweteka. Mulungu alinso ndi zifukwa zabwino zololera anthu kuvutika kwakanthaŵi