Nyimbo 199
“Mawonekedwe a Dziko Lino Akusintha”
(1 Akorinto 7:31, NW)
1. Chinkana akuwononga,
Chilengedwe cha Mulungu,
Tikuyembekezerabe
Kutha kwa kuipaku (kwa dzikoli).
(Korasi)
2. Adaniwo azomola.
Afuna kuchotsa mphamvu.
Tiomba m’manja mokondwa;
Chilakiko nchathudi. (zowonadi)
(Korasi)
3. Mdaniyo adziwonetsa
Nayesa kudodometsa,
Timamatira Mawuwo
Ndi kukhala oyera. (tikhaledi)
(Korasi)
4. Dongosolo lino litha;
Satana adzamangidwa.
Tilalikire mbiriyo
—Ya amatithandiza. (mwachikondi)
(KORASi)
Chinkana dzikoli likusintha,
M’lungu wathu wachifundo
Watikonzera zonse.