Nyimbo 188
Mphatso ya Pemphero
1. Ya amva mapemphero
A onse omumvera.
Mwa Yesu Kristu yekha
Tingafike mpandowo.
2. Mapemphero ofika
Ya akhale owona.
Ochokera mumtima
Alemekeza M’lungu.
3. Popemphera kwa M’lungu
Tiyeni tidzipende,
Tisabwereze mawu,
Komatu mwachikondi.
4. Tipemphe nthaŵi zonse
Poyenda munjirayi.
Pemphero litonthoza;
Ndimphatso ya Mulungu.