Nyimbo 183
Malo a Achichepere m’Makonzedwe a Mulungu
1. Onse ali n’malo m’makonzedwe a Ya.
Aitana ana ndi akulunso.
Kuyankha kwa anawo nkokondweretsa,
Polengeza za Ufumu padziko.
Umboni wawo uli wogwira mtima,
Ali audongo ndi aulemu!
Iwo ali ofunika kwa Yehova;
Kwa akulunso adzetsa chimwemwe.
2. Achichepere onsewo odziŵa Ya,
Ndichisangalalo chotani nanga!
Pomalingalira zamtsogolo mwawo
—Moyo wosathawo m’Paradaiso!
Panopo tikukhala m’zitsenderezo
Zado ngosolo limene likutha.
Timenyere nkhondo kuti tililake;
Tikhulupirike ku Ufumuwo.
3. Angapeze mabwenzi mwa anthu a Ya.
Afunirenji ubwenzi ndi dziko?
Atanganitsidwe ndi zinthu zomanga,
Adalire pamawu a Mulungu.
Mumavuto afufuze owakonda,
Kuwauza zothetsa nzeru zawo.
Koma bwenzi lawo lalikulu ndi Ya;
Adzamupeza ali wachifundo.
4. Tiri ziŵalo za mpingo Wachikristu,
Kumene Yesu agaŵira zonse.
Mokhulupirika tiime nayedi;
Tilabadire uphungu wakewo.
Tisapanikizidwetu ndi dzikoli;
Mawu a Ya ayeretse mitima.
Tonsefe tikhale okhulupirika;
Kumtamanda ndiko moyo wosatha.