Nyimbo 198
Kufika Pakudziŵa Mulungu Wathu
1. Ndithu tidziŵa, Mmene M’lungu,
amveradi.
Watimasula Mwachisomo
Ali nafe.
2. Ndi wachifundo Ndi chikondi,
Tizidziŵa.
Timudalira; Ndife fumbi,
Ngwachifundo.
3. Tiphunziratu, Zambiridi,
Za Mulungu.
Tiyesayesa Kuyendabe
Mwa Kristuyo.
4. Titsanziretu Chikondicho,
M’ntchito zathu.
Tidziŵikitse Dzina la Ya,
Ngwowonadi.