Nyimbo 182
“Mvunguti mu Gileadi”
1. Tamva kuti m’Gileadi;
Mulidi mvunguti.
Utonthoza opsinjika
Uchotsa chisoni.
Umatsitsimutsa ngati
Tiritu otopa,
Nkana okondedwa athu
Agona mu imfa.
2. “Mulungu ndiye chikondi,”
Ndiwamphamvu yonse.
Zimene amatumiza
Zitipindulitsa.
Pitaninso kwa Mulungu
Pemphani kwa iye,
Musabise chirichonse;
Muuzeni zonse.
3. Kumbukirani zinthuzo,
Zochitika kale,
Zinalembedwa kuti ’fe,
Titonthozedwetu.
Landirani chithangato
Modzichepetsatu,
Chidzakuthandizanidi
Kuti mupilire.
4. Kodi mwalingalirapo,
Opsinjika ena?
Kuti enanso ambiri
Ali kuyesedwa?
Muwatonthozetu iwo
Kuti akondwere.
Mukatero mudzadziŵa
Mphamvu ya mvunguti.