Bukhu Ili Linasintha Miyoyo Yawo
Zaka zambiri zapitazo mkazi wina anasudzulidwa ndi mwamuna wake. M’kupita kwa nthaŵi mwana wake Steve anakhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Steve anayesayesa kulankhula ndi amayi ake ponena za zikhulupiriro zake koma popanda chipambano. Iye anapitanso kukawona bambo wake, omwe ankamwalira ndi kansa.
Mmalo molankhula zambiri, Steve anangosiya bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi kumbali kwa kama wa bambo wake nanena kuti kuliŵerenga ilo kukawathandiza. Bambo wake anaŵerenga bukhulo ndipo anangodziyambira kupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova mu January 1988.
Panthaŵiyi, amayi a Steve anali ndi mwaŵi pakukumana kwabanja kuwona umunthu watsopano wosonyezedwa ndi omwe kale anali amuna awo. Ichi chinawasangalatsa kwambiri kwakuti anavomera kupezeka pamsonkhano wa Mboni za Yehova. Iwo anayamba kupezeka pamisonkhano mokhazikika, ndipo mwamsanga anayamba kupezekapo ndi omwe kale anali amuna awo. Potsirizira pake anakwatirananso.
Bambo wa Steve anamwalira mu September 1988 koma atayamba kale kukhala ndi phande muuminisitala Wachikristu. Amayi a Steve, omwe anasamalira bambo wake m’miyezi yomalizira ya matenda awo, anabatizidwa mu June 1988 ndipo tsopano ndi Mboni yachangu.
Bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi limapereka chiyembekezo mwakusonya ku mayankho a Baibulo a mavuto a moyo. Ilo lakhala lothandiza m’kusintha miyoyo yambiri. Landirani kope mwakudzaza ndi kutumiza kapepala kalipansipa.
Ndingakonde kulandira bukhu lachikuto cholimba lamasamba 256 la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. (Kunja kwa Zambia, lemberani ku nthambi ya Watch Tower ya kwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani tsamba 2.)