Nyimbo 82
Akazi Ali Gulu Lankhondo Lalikulu
1. Yehova apereka mawu.
Akazi olalikawo
Aumba gulu la umboni;
Afuna kufika athu.
Ayenera kuyamba msanga,
Nasamala mwininyumba.
Mwa kukhala okonzekera,
Agaŵana muntchitoyo.
2. Antchito anzathu alongo,
Tiwapemphera dalitso.
Akwaniritsa kulalika,
Ifenso tiwatamanda.
Koma ambiri ngamasiye,
Onse ali ndi zovuta.
Samalephera misonkhano;
Asonyeza chipiliro.
3. Tiyeni tiwasamalire
Amayi ana akazi.
Amagaŵana mukututa,
Kuyesa kupulumutsa.
Gululi nloyenereradi.
Zochita zake nzaphindu.
Asamalirenidi bwino.
Mawu a Ya ndi owona.