Kodi Baibulo Liridi Mawu a Mulungu?
Kapena kodi Baibulo liri kokha bukhu lina lolembedwa ndi anthu? Kodi sayansi yalitsimikizira Baibulo kukhala lolakwa? Kodi zozizwitsa zosimbidwa m’Baibulo zinachitikadi?
Kalata yochokera ku Buffalo, New York, inati: “Ndangomaliza kumene kuŵerenga bukhu lakuti The Bible—God’s Word or Man’s? Ilo silikukwaniritsa kokha kusuliza Baibulo kwa munthu komanso likupereka kulongosola komvekera kwa chifukwa chake liyenera kuvomerezedwa kukhala Mawu a Mulungu.”
Dziwonereni nokha umboniwo. Landirani bukhu labwino limeneli mwakungodzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
Ndingakonde kulandira bukhu lachikuto cholimba lamasamba 192 lakuti The Bible—God’s Word or Man’s? (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower ya kwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani patsamba 2.)