Nyimbo 177
Kodi Tiyenera Kukhala Mtundu Wanji wa Anthu?
1. Tikumbukire tsiku lalikulu la Ya.
Mtima wathu uli kwa iye ndi Mwanayo.
Usiku wapita tsiku liyamba;
Zinthu za Satana zichoka msanga.
Pemphero nlabwino kuti tikhale maso.
Pemphero liri lofunika kwakukulu.
Mwakupempha M’lungu ndi mtima wonsewo,
Tidzapeza mtendere umene atipatsa.
2. Chimwemwe ndi mtendere wathu sizimatha.
Tiri chiwonetso kuti anthu adziŵe.
Kodi tingakhale anthu otani?
Kodi tisonyeze ntchito zotani?
Tifuna kuuza ena za Ufumuwo
Ndi kunena za malonjezo atsopano
Ndi kuti kudzakhaladi chilungamo.
Tipitirizebe kulalikira mbiriyi.
3. Tisamale machitidwe athu a moyo
Mogwirizana ndi malamulo a phindu.
Yesu anatiyeretsa mu’chimo,
Tikondwa ndi mtendere wa Mulungu.
Tikufunabe kukhala opanda banga;
Monga atumiki a Ya ndifedi mfulu.
Tikakhala naye monga Bwenzi lathu,
Adzatithandiza kufikira kumapeto.