Nyimbo 193
Lalikirani “Mbiri Yabwino Imeneyi Yaufumu”!
(Mateyu 24:14, NW)
1. Mbiri yabwinoyi Yaufumu lero
Ilengezedwe m’dziko lonse.
Ndipo dzina labwinolo la Yehova,
Lilemekezedwe ponsepo.
(Korasi)
2. Masiku ngoipa; tiombole nthaŵi
Kuzosangalatsa zadziko.
Ufumu ukhale woyamba mumoyo,
Tipezedi chuma chosatha.
(Korasi)
3. Polalika mbiriyo musawopsedwe,
Nkanatu muli ndi chitsutso.
Mwachifundo pilirani osawopa;
Khalani owona muntchito.
(KORASi)
Lalikirani ponsepo.
Kuti ena adziŵe M’lungu.
Ndipo thandizani onse aitane
pa Ya nayeretse dzinalo.