Nyimbo 216
‘Khalani ndi Chikondi Chenicheni’
1. Ndichikondi chotani Yehova wasonya
Kwa akumfunafuna!
Chifundo ukoma zibweretsa chimwemwe;
Mwa iye tiri ndi mpumulo.
2. Tichitirane chifundocho chaubale
Potumikira M’lungu.
Tisonyeze khalidwe labwino kwambiri
Mwa mtenderedi muumodzi.
3. Popeza ndife Akristu tiri amodzi,
Chikondicho chikule.
Tipatse ulemu abale athu onse
Tisawakhumudwitse ndithu.
4. Tipereke chisamaliro kuchikondi,
Yesu anaphunzitsa.
Ukoma wa mtima ndi kudziŵa chikondi
Kumatidzetsera chimwemwe.