Nyimbo 120
Khalani Okhazikika Monga Rute
1. Naomi ati Rute pita,
Nkana sizimukondweretsa.
Rute akana kubwerera,
Mtima’ke uli pa Naomi.
2. ‘Ayi sindidzakusiyani.
Komwe mukhala ndidzakhala.
Komwe mugona ndidzagona.
Komwe mufera ndidzafera.
3. ‘Anthu anu ndianthu anga,
M’lungu wanu ndi M’lungu wanga.
Mulungu awonjezerepo
Ngati ine ndisiya inu.’
4. Rute anaika chitsanzo!
Pakusonyeza chikonditu.
Tisonyeze kukhazikika.
Timamatire kwa Mulungu.