Nyimbo 126
Kulengeza Chowonadi Chaufumu
1. Chowonadi ndichapatali;
Onga nkhosa asangalala.
Mofulumira tilalike,
Ndithudi, Ufumuwo wadza.
2. Kunyumba ndi nyumba tipita;
Tifuna kubzala cho’nadi.
Tiri ndi thandizo la M’lungu.
Mzimuwo utipatsa mphamvu.
3. Tadalitsidwa ndi ntchitoyo.
Tiyeni tiyeseyesetse,
Kudzetsa chiyembekezocho.
Cho’nadi chidzawapumitsa.
4. Tilengeze m’dziko lonseli
Kuti Yesu alamulira.
Ufumuwo udzadziŵitsa
Za dzina la Yehova Mfumu.