Mutu 115
Mkangano Ubuka
KUCHIYAMBIYAMBI kwa madzulowo, Yesu anaphunzitsa phunziro labwino kwambiri muutumiki wodzichepetsa mwa kusambitsa mapazi a atumwi ake. Pambuyo pake, anayambitsa Chikumbutso cha imfa yake yoyandikirayo. Tsopano, makamaka polingalira zimene zangochitika kumene, chochitika china chodabwitsa chikuchitika. Atumwi ake akuphatikizidwa mu mkangano wowopsa wonena zakuti ndani amene akuwonekera kukhala wamkulu koposa pakati pawo! Mwachiwonekere, umenewu uli mbali ya mkangano wosatha.
Kumbukirani kuti Yesu atasandulika paphiri, atumwiwo anakangana ponena za amene ali wamkulu koposa pakati pawo. Ndiponso, Yakobo ndi Yohane anapempha malo apamwamba mu Ufumu, kukumachititsa mkangano wowonjezereka pakati pa atumwiwo. Tsopano, pausiku wake womalizira kukhala nawo, Yesu ayenera kukhala wachisoni chotani nanga kuwawona akukangananso! Kodi iye akuchitanji?
Mmalo mwa kunyodola atumwiwo chifukwa cha khalidwe lawolo, Yesu kachiŵirinso moleza mtima akulingalira nawo akumati: “Mafumu a anthu amitundu awachitira ufumu; ndipo iwo amene awachitira ulamuliro anenedwa, Ochitira zabwino. Koma sipadzatero ndi inu, . . . Pakuti wamkulu ndani, iye wakuseyama pachakudya kapena wakutumikirapo? sindiye wakuseyama pachakudya kodi?” Kenako, akumawakumbutsa chitsanzo chake, iye akuti: “Koma ine ndiri pakati pa inu monga ngati wotumikira.”
Mosasamala kanthu za kupanda ungwiro, kwawo atumwiwo amamatirana ndi Yesu mkati mwa mayeso ake. Chotero iye akuti: “Ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate anandiikira ine.” Pangano limeneli laumwini pakati pa Yesu ndi otsatira ake okhulupirika likuwagwirizanitsa kwa iye kukhala ndi phande muulamuliro wake waufumu. Chiŵerengero chokhala ndi polekezera cha 144,000 chokha potsirizira chikuloŵetsedwa m’pangano limeneli la Ufumu.
Ngakhale kuli kwakuti atumwiwo alonjezedwa chiyembekezo chodabwitsa chimenechi cha kugaŵana ndi Kristu muulamuliro Waufumu, iwo pakali pano ali ofooka mwauzimu. “Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha ine usiku uno,” Yesu akutero. Komabe, akuuza Petro kuti Iye wapemphera mmalo mwake, Yesu akufulumiza kuti: “Pamene watembenuka ukhazikitse abale ako.”
“Tiana,” Yesu akufotokoza, “katsala kanthaŵi ndikhala ndi inu. Mudzandifunafuna ine; ndipo monga ndinanena kwa Ayuda, kuti kumene ndimkako ine, inu simungathe kudza, momwemo ndinena kwa inu tsopano. Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”
“Ambuye, mumuka kuti?” Petro akufunsa motero.
“Kumene ndimukako sungathe kunditsata ine tsopano,” Yesu akuyankha motero, “koma udzanditsata bwino lomwe.”
“Ambuye, sindingathe kukutsatani inu tsopano chifukwa ninji?” Petro akufuna kudziŵa. “Ndidzataya moyo wanga chifukwa cha inu.”
“Moyo wako kodi udzautaya chifukwa cha ine?” Yesu akufunsa. “Ndithu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asanalire kaŵiri udzandikana ine katatu.”
“Ngakhale ine ndikafa ndi inu,” Petro akutsutsa motero, “sindidzakukanani inu iyayi.” Ndipo pamene kuli kwakuti atumwi enawo akugwirizana naye kunena chinthu chimodzimodzicho, Petro akudzitamandira kuti: “Ngakhale onse adzakhumudwa chifukwa cha inu, ine sindidzakhumudwa nthaŵi zonse.”
Ponena za nthaŵi pamene anatumiza atumwiwo paulendo wokalalikira ku Galileya popanda thumba la ndalama ndi thumba la kamba, Yesu akufunsa kuti: “Munasoŵa kanthu kodi?”
“Iyayi,” iwo akuyankha.
“Koma tsopano, iye amene ali ndi thumba la ndalama, alitenge, ndi thumba la kamba lomwe,” iye akutero, “ndipo amene alibe, agulitse chofunda chake, nagule lupanga. Pakuti ndinena ndi inu, chimene chidalembedwa chiyenera kukwaniritsidwa mwa ine, Ndipo anaŵerengedwa ndi anthu opanda lamulo; pakuti izi za kwa ine ziri nacho chimaliziro.”
Yesu akusonya kunthaŵi pamene adzapachikidwa pamodzi ndi ochita zoipa, kapena osayeruzika. Iye akusonyezanso kuti pambuyo pake otsatira ake adzayang’anizana ndi chizunzo chowopsa. “Ambuye, tawonani, malupanga aŵiri siwa,” iwo akutero.
“Chakwanira,” iye akuyankha motero. Monga momwe tidzawonera, kukhala kwawo ndi malupanga kudzalola Yesu kuwaphunzitsa phunziro lina lofunika koposa posachedwapa. Mateyu 26:31-35; Marko 14:27-31; Luka 22:24-38; Yohane 13:31-38; Chivumbulutso 14:1-3.
▪ Kodi nchifukwa ninji mkangano wa atumwiwo uli wodabwitsa kwambiri?
▪ Kodi Yesu akusamalira motani mkanganowo?
▪ Kodi nchiyani chikukwaniritsidwa ndi pangano limene Yesu akuchita ndi ophunzira ake?
▪ Kodi ndilamulo latsopano lotani limene Yesu akupereka, ndipo kodi nlofunika motani?
▪ Kodi ndichidaliro chonkitsa chotani chimene Petro akusonyeza, ndipo kodi Yesu akunenanji?
▪ Kodi nchifukwa ninji malangizo a Yesu onena za kunyamula thumba la ndalama ndi thumba la kamba ali osiyana ndi amene iye anapereka poyambirira?