Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Zipatso—Zabwino ndi Zoipa
    Nsanja ya Olonda—1994 | March 1
    • 15. Kodi ndimotani mmene Israyeli wauzimu lerolino ndi atsamwali awo onga nkhosa alabadirira chifundo cha Yehova?

      15 Chabwino, bwanji za tsiku lathu? Yehova wasonyeza chifundo chachikulu kwa otsalira ake a Israyeli wauzimu ndi atsamwali awo onga nkhosa. Diso lake lakhala lili pa iwo nthaŵi zonse chiyambire kulanditsidwa kwawo kwauzimu mu 1919. Monga momwe ananeneratu kupyolera mwa Yesaya, iwo amalandira malangizo aumulungu tsiku ndi tsiku kuchokera kwa Mphunzitsi wamkulu koposa m’chilengedwe chonse, Yehova Mulungu. (Yesaya 54:13) Chiphunzitso chaumulungu chimenechi, choperekedwa kupyolera mwa Mwana wake wokondedwa, Yesu Kristu, chachititsa mtendere wochuluka pakati pawo ndipo chawadzetsa mosalekeza muunansi wapafupi ndi Yehova. Ndimkhalidwe wauzimu wokondweretsa chotani nanga umene zimenezi zimapereka kwa tonsefe kuti tidziŵe Yehova, kumumvetsera, ndi kupitirizabe kubala zipatso zabwino m’miyoyo yathu​—zipatso zimene zimadzetsa chitamando kwa Yehova! Zimasungitsa moyo wathu weniweniwo!

      16. Kodi ndikugwiritsira ntchito kwaumwini kotani kwa masomphenya a mitanga iŵiri ya nkhuyu kumene aliyense wa ife angapange?

      16 Koma mosasamala kanthu za chifundo chachikulu cha Mulungu, padakali ena amene amakhala opanduka ndi amitima youma, monga momwe ambiri anachitira m’Yuda wakale, ndi amene amabala zipatso zoipa, zowola m’miyoyo yawo. Nzatsoka chotani nanga zimenezi! Aliyense wa ife asaphonyetu phunziro lachenjezo lofotokozedwa bwino lomwe kwa ife ndi mitanga iŵiri imeneyi ya nkhuyu ndi zipatso zake​—zabwino ndi zoipa. Pamene chiweruzo choyenera cha Yehova pa Dziko Lachikristu lopatuka chikudza mofulumira, tilabadiretu chilangizo cha mtumwi Paulo chakuti: “Mukayende koyenera [Yehova, NW] kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino.”​—Akolose 1:10.

      Kupenda “Zipatso​—Zabwino ndi Zoipa” ndi ndime 1-4 za “Mlandu wa Yehova ndi Mitundu ya Anthu”

      ◻ Kodi mtanga wa nkhuyu zabwino umaimiranji?

      ◻ Kodi ndimotani mmene mtanga wa m’masomphenya wa nkhuyu zoipa waonekerera?

      ◻ Kodi ndiphunziro lochenjeza lotani limene uthenga wa Yeremiya umapereka kwa ife?

      ◻ Kodi nchiyani chimene chinali chapadera ndi chaka cha 607 B.C.E.? ndi 1914 C.E.?

  • Mlandu wa Yehova ndi Mitundu ya Anthu
    Nsanja ya Olonda—1994 | March 1
    • Mlandu wa Yehova ndi Mitundu ya Anthu

      “Phokoso lidzadza ku malekezero a dziko lapansi; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi mitundu ya anthu.”​—YEREMIYA 25:31.

      1, 2. (a) Kodi nchiyani chimene chinachitika m’Yuda pambuyo pa imfa ya Mfumu Yosiya? (b) Kodi ndani amene anali mfumu yotsiriza ya Yuda, ndipo kodi ndimotani mmene anasautsidwira chifukwa cha kusakhulupirika kwake?

      DZIKO la Yuda linayang’anizana ndi nthaŵi zoŵaŵitsa zovuta kuchita nazo. Mfumu ina imodzi yabwino, Yosiya, inaimitsa kwakanthaŵi mkwiyo waukulu wa Yehova. Koma kodi nchiyani chimene chinatsatira pamene Yosiya anaphedwa mu 629 B.C.E.? Mafumu amene anamloŵa mmalo ananyoza Yehova.

      2 Mfumu yotsiriza ya Yuda, Zedekiya, mwana wachinayi wa Yosiya, inapitirizabe, monga momwe pa 2 Mafumu 24:19 pamanenera, ‘kuchita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adachita Yoyakimu [mkulu wake].’ Kodi nchiyani chinali chotulukapo chake? Nebukadinezara anaukira Yerusalemu, anagwira Zedekiya, anapha ana ake aamuna pamaso pake, anamuboola maso, ndi kumtengera ku Babulo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena