Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Tapeza Ife Mesiya”!
    Nsanja ya Olonda—1992 | October 1
    • chosalekeza.” Ayuda anadziŵa bwino lomwe kuti nsembe yokha, imfa, ikakhoza kupanga chotetezera machimo.​—Levitiko 17:11; yerekezerani ndi Ahebri 9:22.

      18. (a) Kodi ndimotani mmene Yesaya chaputala 53 amasonyezera kuti Mesiya ayenera kuvutika ndi kufa? (b) Kodi nzowonekera kukhala kudzitsutsa zotani zimene ulosi umenewu umadzutsa?

      18 Yesaya chaputala 53 amalankhula za Mesiya kukhala Mtumiki wapadera wa Yehova amene akafunikira kuvutika ndi kufa kukwirira machimo a ena. Vesi 5 limati: “Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu.” Ulosi umodzimodziwo, pambuyo pa kutiuza kuti Mesiya ameneyu anayenera kufa monga “nsembe yopalamula,” umavumbula kuti Munthu mmodzimodziyu “adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m’manja mwake.” (Vesi 10) Kodi zimenezo siziri kudzitsutsa? Kodi ndimotani mmene Mesiya akanafera, ndiyeno ‘nkutanimphitsa masiku ake’? Kodi ndimotani mmene akanaperekedwera monga nsembe ndiyeno pambuyo pake kupanga ‘chomkondweretsa Yehova kukhala chachipambano’? Ndithudi, kodi ndimotani mmene, iye akanafera ndi kukhalabe wakufa popanda kukwaniritsa maulosi ofunika kopambana onena za iye, ndiko kuti kuti akalamulira kosatha monga Mfumu ndi kubweretsa mtendere ndi chimwemwe kudziko lonse lathunthu?​—Yesaya 9:6, 7.

      19. Kodi chiukiriro cha Yesu chimagwirizanitsa motani maulosi owonekera kukhala odzitsutsa onena za Mesiya?

      19 Kuwonekera kukhala kudzitsutsa kumeneku kunamveketsedwa bwino mwachozizwitsa chimodzi, chachilendo. Yesu anaukitsidwa. Ayuda owona mtima mazana ambiri anafikira kukhala mboni zowona ndi maso za chochitika chaulemerero chimenechi. (1 Akorinto 15:6) Mtumwi Paulo pambuyo pake analemba kuti: “[Yesu Kristu] adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu chikhalire; kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ake aikidwa akhale mpando ku mapazi ake.” (Ahebri 10:10, 12, 13) Inde, kunali pambuyo poti Yesu waukitsidwira kumoyo wakumwamba, ndi pambuyo pa nyengo ya ‘kulindirira,’ kuti iye potsirizira pake akaikidwa pampando wachifumu monga Mfumu ndi kuchitapo kanthu motsutsana ndi adani a Atate wake, Yehova. M’mbali yake monga Mfumu yakumwamba, Yesu Mesiyayo amayambukira moyo wa munthu aliyense amene tsopano ali ndi moyo. M’njira yotani? Nkhani yathu yotsatira idzafotokoza zimenezi.

  • Kukhalapo kwa Mesiya ndi Ulamuliro Wake
    Nsanja ya Olonda—1992 | October 1
    • Kukhalapo kwa Mesiya ndi Ulamuliro Wake

      “Yesu amene walandiridwa kumka kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuwona alinkupita kumwamba.”​—MACHITIDWE 1:11.

      1, 2. (a) Kodi ndimotani mmene angelo aŵiri anatonthozera atumwi a Yesu pamene iye anakwera kumwamba? (b) Kodi ndimafunso otani amene akudzutsidwa ndi chiyembekezo cha kubweranso kwa Kristu?

      AMUNA khumi ndi mmodzi anali mmunsi cha kummaŵa kwa Phiri la Azitona, akuyang’ana dwii kumwamba. Nthaŵi yochepa chabe yapitayo, Yesu Kristu anali atanyamuka pakati pawo, mawonekedwe ake anali kuzimiririka kufikira ataphimbidwa ndi thambo. M’zaka zawo limodzi naye, amuna ameneŵa anali atawona Yesu akupereka umboni wochuluka wakuti iye anali Mesiya; iwo anawona ngakhale mavuto a imfa yake ndi chikondwerero cha chiukiriro chake. Tsopano anali atapita.

      2 Angelo aŵiri anawonekera mwadzidzidzi nalankhula mawu otonthoza awa: “Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang’ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kumka

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena