Nyimbo 138
O Yendani ndi Mulungu!
(Mika 6:8)
1. Yendani ndi Ya mofatsa;
Kondani chifundo.
Sungani umphumphu wanu;
M’lungu alimbitsa.
Mukasungabe cho’nadi,
Simunamizidwa;
M’lungu akutsogolere,
Mongatu kamwana.
2. Yendani ndi Ya m’chiyero;
Musachite tchimo.
Khalani achikulire
Muvomerezedwe.
Pa zirizonse zoyera
Ndi zokoma mtima,
Pa izi ganizirani,
Mudalire M’lungu.
3. Yendani ndi Ya mowona,
Ndipo mudzapeza
Kukwana ndi umulungu,
Zopindulitsadi.
Yendanitu ndi Mulungu
Zitamando imba.
Chisangalalo chanucho
Chidza ndi ntchitoyo.