Nyimbo 200
Chitsimikiziro cha Kukhala Ophunzira
1. M’kusonyeza chikondi,
Akristu adziŵika.
Kristu anasonyeza
Chikondi namveratu.
Chingapezeke kuti
Chikondi choterechi?
Yense ataya moyo,
Kupatsa wina moyo.
2. Chikondi chowonacho,
Chiri cha kwa onsewo.
Nchaukoma wambiri,
Chimadalitsa ena.
Ndilamulo la Yesu;
Chikondi chithandiza,
Sichidzipindulira,
Chimathandiza ena.
3. Chimawona zabwino.
Chimangira ubale.
Chikondi kwa olakwa
Chifunira ubwino.
Dziko lidzatidziŵa
Mwa chikondi chathucho,
Mwa Mwana wa mmwambayo.
O “Mulungu nchikondi”!