Nyimbo 28
Dalitsani Kusonkhana Kwathu Pamodzi
1. M’tidalitse posonkhana,
Kulambira inu, Ya.
Tiyamika malo ano;
Mzimu ukhale nafe.
2. Tisoŵatu mwauzimu;
Mutidzaze n’cho’nadi.
M’tiphunzitse kulalika,
Mutidzaze chikondi.
3. Pamsonkhano wokomawu;
Tifune chilungamo.
Kutitu tidziŵe inu
Tikhalebe ofatsa.
4. Mudalitse misonkhano;
Mtendere ndi umodzi.
Mu’tumiki Waufumu,
Titametu Ufumu.