Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/96 tsamba 4
  • Kupeza Mfungulo ya Chimwemwe cha Banja

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupeza Mfungulo ya Chimwemwe cha Banja
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 2/96 tsamba 4

Kupeza Mfungulo ya Chimwemwe cha Banja

1 Mabanja amene amagwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo ndi kukhala moyo wawo malinga ndi ufumu wa Mulungu aona kuti mavuto awo amachepetsedwa, ngati sathetsedwa, ndipo apeza chimwemwe. Kodi umenewu si uthenga wofunika kwambiri wopereka ku mabanja m’gawo lanu mkati mwa mwezi wa February, mukumagwiritsira ntchito buku la Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe?

2 Kodi zimenezi tidzazichita motani? Mwa kuwasonyeza Mawu a Mulungu, amene amafotokoza mapulinsipulo a chimwemwe cha banja. Anthu amalingalira za moyo wa banja. Khalani wofunitsitsa kulankhulapo. Asonyezeni mmene bukulo lingawathandizire. Koma sonyezaninso kuti mavuto a moyo wa banja sadzatheratu mpaka ufumu wa Mulungu utachotsapo kuipa konse pa dziko lapansi. Zimenezo nzimene anthu amapempherera pamene amapemphera Pemphero la Ambuye, koma ambiri a iwo samazindikira zimenezo. (Mat. 6:9, 10) Mutu womaliza wa buku la moyo wa banjalo ungawathandize kuzindikira choonadi chimenechi.

3 Mungayambe motere:

◼ “Ndabwera kudzagaŵana nanu nkhani ina yonena za vuto limene likuyambukira anthu ambiri lerolino. Ilo limakhudza moyo wa banja. Tonsefe timafuna banja lathu kukhala lachimwemwe, koma timadziŵa kuti mabanja ambiri saali achimwemwe kwenikweni. Kodi mumaganiza kuti nchiyani chimene chingathandize anthu kupeza chimwemwe chachikulu m’moyo wawo wa banja? [Aloleni ayankhe.] Kodi simukuvomereza kuti kungakhale kopindulitsa kumvetsera zimene Mlengi wa banja akunena? Iye amapereka chitsogozo chofunika m’Baibulo. Mapulinsipulo ameneŵa akufotokozedwa m’buku ili lakuti Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe. Taonani mbali za nkhaniyi zimene zikufotokozedwa. [Sonyezani ndandanda ya zamkati.] Buku limeneli limasonyezanso njira yokhalitsa yothetsera mavuto a anthu. Mosakayikira mumaipempherera. Mumalidziŵa Pemphero la Ambuye, si choncho kodi? [Gwirani mawu Mateyu 6:9, 10.] Nchifuno cha Mulungu kuti ufumu wake uchotse kuipa konse pa dziko lapansi. Mutu womaliza wa bukuli umasonyeza mmene moyo wa banja wa anthu onse amene tsopano ali ndi chikhulupiriro mu ufumu wa Mulungu udzapindulira. Tikusiya bukuli pa K4.00 yokha.”

4 Komabe, pamene mulankhula ndi anthu za mavuto a moyo wa banja, mudzafunikira kukhala ochenjera. Peŵani kupereka lingaliro lakuti mukuganiza kuti mwini nyumba ali ndi mavuto m’banja mwake. Kungakhale bwino kulankhula za vutolo monga limene anthu ambiri ali nalo.

5 Kusonyeza chikondwerero m’mabanja: Kodi sikungakhale bwino kuti tipange chonulirapo cha kulankhula ndi mabanja ambiri omwe tingathe m’mwezi wa February? Kumbukirani zimenezi pamene muika maziko a ulendo wanu wobwereza. Pamene makambitsirano akutha paulendo wanu woyamba, munganene kuti: “Popeza tikufuna kukambitsirana Baibulo ndi mabanja, ndingakonde kubweranso panthaŵi imene banja lanu lonse lili panyumba kuti tidzapitirize makambitsirano athu. [Funsani imene ingakhale nthaŵi yabwino yodzabweranso.] Izi zikali choncho mungafune kusuzumiramo m’bukuli, ndipo pamene ndibweranso tingadzakambitsirane mutu umene uli wabwino kwambiri kwa inu ndi banja lanu.”

6 Tikukhulupirira mukuvomereza kuti bukuli lidzakhaladi lothandiza kwa mabanja a m’gawo lanu. M’zaka zambiri zapitazi talandira makalata ambiri oyamikira uphungu wabwino wopezeka m’buku limeneli. Mwamuna wina anati: “Pamene mkazi wanga ndi ine tikupitiriza kuphunzira bukuli, banja lathu likupitirizabe kuwongokera.” Mwachionekere inu munali ndi malingaliro amodzimodziwo pamene munaŵerenga buku limeneli.

7 Motero, pamene mukuyesayesa kupanga ophunzira, lingalirani za kuthandiza mabanja onse athunthu. Athandizeni kuona kufunika kwa uthenga wa Ufumu kotero kuti akakhale pamodzi m’madalitso amtsogolo.—Chiv. 21:4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena